1. Kongebog 4 – BPH & CCL

Bibelen på hverdagsdansk

1. Kongebog 4:1-20

Salomons embedsmænd

1Salomon var konge over hele Israels folk, 2og det følgende er en liste over hans højeste embedsmænd:

Azarja, søn af Zadok, var præst ved helligdommen; 3Elihoref og Ahija, Shishas sønner, var statssekretærer; Joshafat, søn af Ahilud, havde ansvaret for de historiske arkiver; 4Benaja, søn af Jojada, var øverstbefalende for hæren; Zadok og Ebjatar var præster; 5Azarja, søn af Natan, havde opsyn med alle distriktsguvernørerne; Zabud, søn af Natan, var hofpræst og kongens personlige rådgiver; 6Ahishar var hofmarskal; Adoniram, søn af Abda, havde opsyn med alle slaverne.

7Salomons 12 distriktsguvernører havde ansvar for at opkræve skat til kongens hof. Hvert distrikt havde ansvar for at sende forsyninger til kongen og hans hof én måned om året. 8Det følgende er en liste over distriktsguvernørerne og de områder, de havde ansvar for:

Hurs søn var guvernør over Efraims bjergland; 9Dekers søn over Makatz-Sha’albim, Bet-Shemesh og Elon-Bet-Hanan; 10Heseds søn over byerne Arubbot og Soko samt hele Hefer-området; 11Abinadabs søn, som var gift med Salomons datter Tafat, over Dors højland; 12Ba’ana, Ahiluds søn, over byerne Ta’anak og Megiddo samt hele området omkring Bet-Shan, som ligger ved Zaretan neden for Jizre’elsletten og op til Abel-Mehola og Jokmeam området; 13Gebers søn over Ramot-Gilead, Jairs landsbyer (opkaldt efter Manasses søn Jair) og Argob-området i Bashan, i alt 60 større befæstede byer med portslåer af bronze; 14Ahinadab, Iddos søn over Mahanajim-området; 15Ahima’atz, der var gift med Basemat—en anden af Salomons døtre—over Naftalis land; 16Ba’ana, Hushajs søn, over Ashers land med byen Alot; 17Joshafat, Paruas søn, over Issakars land; 18Shimi, Elas søn, over Benjamins land; 19Geber, Uris søn, over Gilead-området med den del, der havde tilhørt amoritterkongen Sihon og kong Og af Bashan. Der var kun én garnison i hele det område.

Israels og Judas storhedstid

20Under kong Salomon oplevede Juda og Israel en vældig opblomstring. Befolkningstallet voksede stærkt, og alle havde nok at spise og var glade og tilfredse.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Mafumu 4:1-34

Nduna za Solomoni ndi Abwanamkubwa

1Ndipo Mfumu Solomoni inakhala mfumu ya Aisraeli onse. 2Nduna zake zikuluzikulu zinali izi:

Azariya mwana wa Zadoki anali wansembe;

3Elihorefe ndi Ahiya, ana a Sisa, anali alembi;

Yehosafati mwana wa Ahiludi, anali mlembi wa zochitika;

4Benaya mwana wa Yehoyada, anali mtsogoleri wa ankhondo;

Zadoki ndi Abiatara, anali ansembe;

5Azariya mwana wa Natani, anali woyangʼanira nduna za mʼzigawo;

Zabudi mwana wa Natani, anali wansembe ndi bwenzi la mfumu;

6Ahisara, anali mkulu woyangʼanira nyumba ya mfumu;

Adoniramu mwana wa Abida, anali mkulu woyangʼanira ntchito za thangata.

7Solomoni analinso ndi abwanamkubwa khumi ndi awiri amene ankayangʼanira zigawo zonse za dziko la Israeli. Iwo ankapereka chakudya kwa mfumu ndiponso ku banja laufumu. Bwanamkubwa aliyense ankapereka chakudya mwezi umodzi pa chaka. 8Mayina awo ndi awa:

Beni-Huri, wa ku dziko la mapiri la Efereimu;

9Beni-Dekeri, woyangʼanira mizinda ya Makazi, Saalibimu, Beti-Semesi ndi Eloni Beti-Hanani;

10Beni-Hesedi, woyangʼanira mizinda ya Aruboti (Soko ndi dziko lonse la Heferi);

11Beni-Abinadabu, woyangʼanira Nafoti Dori (iye anakwatira Tafati mwana wa Solomoni);

12Baana mwana wa Ahiludi, anali woyangʼanira Taanaki ndi Megido, ndi ku Beti Sani konse, kufupi ndi ku Zaretani kumunsi kwa Yezireeli, kuyambira ku Beti-Seani mpaka ku Abeli-Mehola kukafika mpaka ku Yokineamu;

13Beni-Geberi, anali woyangʼanira Ramoti Giliyadi (midzi ya Yairi inali ya mwana wa Manase ku Giliyadi, pamodzinso ndi chigawo cha Arigobu ku Basani ndiponso mizinda yake yayikulu makumi asanu ndi umodzi yokhala ndi malinga ndi mipiringidzo yamkuwa).

14Ahinadabu mwana wa Ido, anali woyangʼanira Mahanaimu;

15Ahimaazi anali woyangʼanira Nafutali (iyeyu anakwatira Basemati mwana wa Solomoni);

16Baana mwana wa Husai, anali woyangʼanira Aseri ndi Bealoti;

17Yehosafati mwana wa Paruwa, anali woyangʼanira Isakara;

18Simei mwana wa Ela, anali woyangʼanira Benjamini;

19Geberi mwana wa Uri, anali woyangʼanira Giliyadi (dziko la Sihoni mfumu ya Aamori ndi dziko la Ogi mfumu ya Basani). Iye ankayangʼanira chigawo chonsechi yekha.

Chakudya cha Tsiku ndi Tsiku cha Solomoni

20Anthu a ku Yuda ndi ku Israeli anali ochuluka ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja. Ankadya ndi kumwa ndipo ankasangalala. 21Ndipo Solomoni analamulira mayiko onse kuyambira ku mtsinje wa Yufurate mpaka ku dziko la Afilisti, kukafika mpaka ku malire a dziko la Igupto. Mayikowa ankabweretsa mphatso ndipo anali pansi pa ulamuliro wa Solomoni moyo wake wonse.

22Chakudya cha tsiku ndi tsiku cha Solomoni chinali madengu 150 a ufa wosalala ndi madengu 300 a mgayiwa, 23ngʼombe khumi zonenepa zodyetsera mʼkhola, ngʼombe za ku busa makumi awiri, ndiponso nkhosa ndi mbuzi 100, pamodzinso ndi mbawala, agwape, mphoyo ndi mbalame zoweta zonona. 24Pakuti ankalamulira dziko lonse la kumadzulo kwa mtsinje wa Yufurate kuyambira ku Tifisa mpaka ku Gaza, mafumu onse a kumadzulo kwa Mtsinje, ndipo anali pa mtendere ndi mayiko onse ozungulira. 25Pa nthawi ya Solomoni, Yuda ndi Israeli anali pa mtendere, kuyambira ku Dani mpaka ku Beeriseba. Munthu aliyense ankangodzikhalira pansi pa mpesa wake ndi mtengo wake wa mkuyu.

26Solomoni anali ndi zipinda 4,000 zodyeramo akavalo okoka magaleta ake ndi anthu 12,000 oyendetsa magaleta.

27Abwanamkubwa a zigawo aja, aliyense pa mwezi wake, ankapereka chakudya cha Mfumu Solomoni ndi cha anthu onse amene ankadya naye. Iwo ankaonetsetsa kuti pasasowe kalikonse. 28Ankabweretsanso ku malo ake ofunikira muyeso wawo wa barele ndi udzu wa akavalo okoka magaleta ndiponso akavalo ena.

Nzeru za Solomoni

29Mulungu anamupatsa Solomoni nzeru ndi luntha losaneneka ndipo nzeru zake zinali zochuluka ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja. 30Nzeru za Solomoni zinali zoposa nzeru za anthu onse a Kummawa ndiponso nzeru zonse za ku Igupto. 31Iye anali wanzeru kuposa munthu wina aliyense, kuposa ngakhale Etani wa banja la Ezara, Hemani, Kalikoli ndi Darida, ana a Maholi. Ndipo mbiri yake inamveka kwa mitundu yonse ya anthu ozungulira. 32Solomoni anapeka miyambi 3,000 ndi kulemba nyimbo 1,005. 33Iye ankaphunzitsa za mitengo, kuyambira mtengo wa mkungudza wa ku Lebanoni mpaka kachitsamba ka hisope khomera pa khoma. Iye ankaphunzitsanso za nyama ndi mbalame, zinthu zokwawa pansi ndiponso za nsomba. 34Anthu a mitundu yonse ankabwera kudzamva nzeru za Solomoni. Anthu amenewa ankatumizidwa ndi mafumu onse a dziko lapansi amene anamvapo za nzeru zakezo.