Zekariya 5:1-11, Zekariya 6:1-15, Zekariya 7:1-14, Zekariya 8:1-23 CCL

Zekariya 5:1-11

Chikalata Chowuluka

Ndinayangʼananso ndipo taonani ndinaona chikalata chimene chimawuluka.

Mngelo uja anandifunsa kuti, “Kodi ukuona chiyani?”

Ndinayankha kuti, “Ndikuona chikalata chikuwuluka, mulitali mwake mamita asanu ndi anayi ndipo mulifupi mwake mamita anayi ndi theka.”

Ndipo mngeloyo anandiwuza kuti, “Awa ndi matemberero amene akupita pa dziko lonse lapansi; potsata zimene zalembedwa mʼkati mwa chikalatamo, aliyense wakuba adzachotsedwa, ndipo potsata zomwe zalembedwa kunja kwake, aliyense wolumbira zabodza adzachotsedwanso. Yehova Wamphamvuzonse akunena kuti, ‘Temberero limeneli ndidzalitumiza, ndipo lidzalowa mʼnyumba ya munthu wakuba ndi munthu wolumbira zabodza mʼdzina langa. Lidzakhala mʼnyumbamo mpaka kuyiwonongeratu, matabwa ake ndi miyala yake yomwe.’ ”

Mkazi mu Dengu

Kenaka mngelo amene amayankhula nane uja anabwera patsogolo panga ndipo anandiwuza kuti, “Kweza maso ako tsopano kuti uwone kuti ndi chiyani chikubwerachi.”

Ndinafunsa kuti, “Kodi chimenechi nʼchiyani?”

Mngeloyo anayankha kuti, “Limeneli ndi dengu loyezera.” Ndipo anawonjezera kunena kuti, “Umenewu ndi uchimo wa anthu mʼdziko lonse.”

Pamenepo chovundikira chake chamtovu chinatukulidwa, ndipo mʼdengumo munali mutakhala mkazi. Mngeloyo anati, “Chimenechi ndi choyipa,” ndipo anamukankhira mkaziyo mʼdengu muja, nabwezera chovundikira chamtovu chija pamwamba pake.

Kenaka ndinayangʼananso, ndipo ndinaona akazi awiri akuwuluka kubwera kumene kunali ine; akuwuluzika ndi mphepo. Iwo anali ndi mapiko ngati a kakowa, ndipo ananyamula dengu lija, kupita nalo pakati pa mlengalenga ndi dziko lapansi.

Ine ndinafunsa mngelo amene amayankhula nane kuti, “Dengulo akupita nalo kuti?”

Iye anayankha kuti, “Ku dziko la Babuloni kuti akalimangire nyumba. Nyumbayo ikadzatha, adzayikamo dengulo.”

Read More of Zekariya 5

Zekariya 6:1-15

Magaleta Anayi

Ndinayangʼananso ndipo taonani ndinaona magaleta anayi akutuluka pakati pa mapiri awiri, mapiri amkuwa. Galeta loyamba limakokedwa ndi akavalo ofiira, lachiwiri ndi akavalo akuda, lachitatu ndi akavalo oyera, ndipo lachinayi ndi akavalo otuwa a mawanga ofiirira, onsewa anali akavalo amphamvu kwambiri. Ndinafunsa mngelo amene amayankhula nane uja kuti, “Kodi mbuye wanga chimenechi nʼchiyani?”

Mngeloyo anandiyankha kuti, “Imeneyi ndi mizimu inayi yakumwamba, imene ikuchokera pamaso pa Ambuye wa dziko lonse. Galeta la akavalo akuda likupita ku dziko la kumpoto, galeta la akavalo oyera likutsatira, ndipo galeta la akavalo amawanga ofiirira likupita ku dziko la kummwera.”

Pamene akavalo amphamvuwa ankapita, anali ndi changu chofuna kuyendera dziko lapansi. Ndipo iye anati, “Pitani, kayendereni dziko lapansi!”

Pamenepo anandiyitana, “Taona, akavalo amene apita ku dziko la kumpoto apumulitsa Mzimu wanga kumeneko.”

Chipewa Chaufumu cha Yoswa

Yehova anayankhula nane kuti, “Landira mphatso kuchokera kwa anthu amene abwera ku ukapolo, Helidai, Tobiya ndi Yedaya, amene achokera ku Babuloni. Tsiku lomwelo pita ku nyumba ya Yosiya mwana wa Zefaniya. Tenga siliva ndi golide upange chipewa chaufumu, ndipo uchiyike pamutu pa mkulu wa ansembe, Yoswa mwana wa Yehozadaki. Muwuze kuti zimene akunena Yehova Wamphamvuzonse ndi izi: ‘Taonani, munthu wotchedwa Nthambi ndi ameneyu, ndipo adzaphuka pomwe alipo ndi kumanga Nyumba ya Yehova. Ndiye amene adzamange Nyumba ya Yehova, adzalandira ulemerero waufumu ndipo adzalamulira pa mpando wake waufumu. Adzakhalanso wansembe pa mpando wake waufumu. Ndipo padzakhala mtendere.’ Chipewa cha ufumucho adzachipereka kwa Helemu, Tobiya, Yedaya, ndi kwa Heni mwana wa Zefaniya, kuti chikhale chikumbutso mʼNyumba ya Yehova. Anthu okhala kutali adzabwera kudzathandiza kumanga Nyumba ya Yehova, ndipo iwe udzadziwa kuti Yehova Wamphamvuzonse wandituma kwa iwe. Zimenezi zidzachitika ngati mudzamvera mwachangu Yehova Mulungu wanu.”

Read More of Zekariya 6

Zekariya 7:1-14

Chiweruzo Cholungama ndi Chifundo, Osati Kusala Zakudya

Pa chaka chachinayi cha Mfumu Dariyo, pa tsiku lachinayi la Kisilevi, mwezi wachisanu ndi chinayi, Yehova anayankhula ndi Zekariya. Anthu a ku Beteli anali atatuma Sarezeri ndi Regemu-Meleki pamodzi ndi anthu awo, kuti akapemphe chifundo kwa Yehova pokafunsa kwa ansembe a ku Nyumba ya Yehova Wamphamvuzonse ndi aneneri kuti, “Kodi ine ndizilira ndi kusala zakudya pa mwezi wachisanu, monga mmene ndakhala ndikuchitira pa zaka zambiri?”

Pamenepo Yehova Wamphamvuzonse anayankhula nane kuti, “Funsa anthu onse a mʼdziko ndi ansembe kuti, ‘Pamene munkasala zakudya pa mwezi wachisanu ndi wachisanu ndi chiwiri pa zaka 70 zapitazi, kodi munkasala chifukwa cha Ine? Ndipo pamene munkadya ndi kumwa, kodi simunkachita zimenezi podzisangalatsa nokha? Kodi awa si mawu amene Yehova ankanena kudzera mwa aneneri oyamba aja pamene Yerusalemu ndi mizinda yake yozungulira anali pa mtendere ndi pa ulemerero, ndi pamene Negevi ndi ku madera akumadzulo a mʼmbali mwa phiri munali anthu?’ ”

Ndipo Yehova anayankhulanso ndi Zekariya kuti, “Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Muziweruza molungama; muzichitirana chifundo ndi kumverana chisoni. Musamazunze akazi amasiye kapena ana amasiye, alendo kapena osauka. Musamaganizirane zoyipa mʼmitima mwanu.’

“Koma makolo anu anakana kumvera uthenga umenewu; anawumitsa mtima nandifulatira, natseka makutu awo kuti asamve. Anawumitsa mitima yawo ngati mwala wa sangalabwi ndipo sanamvere lamulo kapena mawu amene Yehova Wamphamvuzonse anawatumiza mwa Mzimu wake kudzera mwa aneneri oyamba aja. Kotero Yehova Wamphamvuzonse anakwiya kwambiri.

“ ‘Pamene ndinawayitana, iwo sanamvere; choncho pamene iwo anandiyitana, Ine sindinamverenso,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse. ‘Ndinawamwaza ndi kamvuluvulu pakati pa mitundu yonse ya anthu, kumene anali alendo. Dziko lawo linatsala litasakazidwa kwambiri kotero kuti palibe amene amabwera kapena kupitamo. Umu ndi mmene anasandutsira dziko labwino kukhala chipululu.’ ”

Read More of Zekariya 7

Zekariya 8:1-23

Yehova Alonjeza Kudalitsa Yerusalemu

Awa ndi mawu amene Yehova Wamphamvuzonse ananena. Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Ine ndikuchitira nsanje yayikulu Ziyoni. Mtima wanga ukupweteka chifukwa cha nsanje pa iyeyo.”

Yehova akuti, “Ndidzabwerera ku Ziyoni ndi kukakhala ku Yerusalemu. Pamenepo Yerusalemu adzatchedwa Mzinda wa Choonadi ndipo phiri la Yehova Wamphamvuzonse lidzatchedwa Phiri Lopatulika.”

Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Abambo ndi amayi okalamba adzakhalanso mʼmisewu ya mu Yerusalemu, aliyense ali ndi ndodo mʼmanja mwake chifukwa cha kuchuluka kwa masiku ake. Ndipo misewu ya mu mzindamo idzadzaza ndi anyamata ndi atsikana akusewera.”

Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Ngati zikuoneka kuti nʼzosatheka kwa anthu otsala pa nthawi ino, kodi zidzakhala zosathekanso kwa Ine?” akutero Yehova Wamphamvuzonse.

Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Taonani ndidzapulumutsa anthu anga kuchokera ku mayiko a kummawa ndi kumadzulo. Ndidzawabweretsa kuti adzakhale mu Yerusalemu; adzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wawo, wokhulupirika ndi wolungama pakati pawo.”

Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Inu amene tsopano mukumva mawu awa amene akuyankhula aneneri amene analipo pamene ankayika maziko a nyumba ya Yehova Wamphamvuzonse, ‘limbani mtima kuti mumange Nyumba ya Yehova.’ Mpaka nthawi imeneyi panalibe munthu wolandira malipiro pa ntchito kapena ndalama zolipirira nyama zogwira ntchito. Panalibe munthu amene ankadzigwirira ntchito mwamtendere chifukwa choopa adani ake, pakuti Ine ndinkawayambanitsa. Koma tsopano sindidzachitira otsala mwa anthu awa zomwe ndinachita kale,” akutero Yehova Wamphamvuzonse.

“Pakuti mbewu zidzamera bwino, mpesa udzabala zipatso zake, nthaka idzatulutsa zomera zake, ndi thambo lidzagwetsa mame. Ndidzapereka zonse kukhala cholowa cha otsala mwa anthu awa. Monga mwakhala muli chinthu chotembereredwa pakati pa mitundu ina ya anthu, inu Yuda ndi Israeli, choncho ndidzakupulumutsani, ndipo mudzakhala dalitso. Musachite mantha, koma limbani mtima.”

Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Monga ndinatsimikiza mtima kubweretsa choyipa pa inu, komanso osakuchitirani chisoni pamene makolo anu anandikwiyitsa,” akutero Yehova, “Choncho tsopano ndatsimikiza mtima kuchitiranso zabwino Yerusalemu ndi Yuda. Musachite mantha. Zinthu zoti muchite ndi izi: Muziwuzana zoona zokhazokha, muziweruza moona ndi mwachilungamo mʼmabwalo anu; musamachitire mnzanu chiwembu, musamakonde kulumbira zonama. Zonsezi Ine ndimadana nazo,” akutero Yehova.

Yehova Wamphamvuzonse anayankhulanso nane. Ndipo ananena kuti, “Kusala zakudya kwa pa mwezi wachinayi, chisanu, chisanu ndi chiwiri ndi wakhumi, kudzakhala nthawi yachimwemwe, ya chisangalalo ndi nthawi ya madyerero chikondwerero kwa Yuda. Nʼchifukwa chake muzikonda choonadi ndi mtendere.”

Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Anthu a mitundu yambiri ndi anthu okhala mʼmizinda yambiri adzabwerabe, ndipo nzika za mzinda wina zidzapita ku mzinda wina, kukanena kuti, ‘Tiyeni mwamsanga tikapemphe madalitso kwa Yehova ndi kukapembedza Yehova Wamphamvuzonse. Inenso ndikupita kumeneko.’ Anthu ambiri ndiponso a ku mayiko amphamvu adzabwera ku Yerusalemu kudzapembedza Yehova Wamphamvuzonse ndi kudzapempha madalitso.”

Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Masiku amenewo anthu khumi ochokera ku mitundu ya anthu a ziyankhulo zosiyana adzagwira mkanjo wa Myuda ndi kunena kuti, ‘Tipite nawo, chifukwa tamva kuti Mulungu ali nanu.’ ”

Read More of Zekariya 8