Aroma 9:1-21 CCL

Aroma 9:1-21

Chisankho Chopambana cha Mulungu

Ine ndikunena zoona mwa Khristu. Sindikunama ndipo chikumbumtima changa kudzera mwa Mzimu Woyera chikundichitira umboni. Ndili ndi chisoni chachikulu ndipo ndikumva kupwetekeka kosalekeza mu mtima mwanga. Pakuti ndikanafuna ine mwini nditatembereredwa ndi kuchotsedwa mwa Khristu chifukwa cha abale anga, amene ndi a mtundu wanga, anthu Aisraeli. Iwo anasankhidwa kukhala ana. Mulungu anawapatsa ulemerero, anachita nawo mapangano, kuwapatsa Malamulo, Nyumba yopembedzeramo ndi malonjezano ake. Awo ndi makolo athu. Kuchokera kwa iwo mʼthupi ndi kumene kunachokera makolo a Khristu Yesu amene ndi Mulungu wolamulira zinthu zonse, alemekezeke mpaka muyaya! Ameni.

Sikuti mawu a Mulungu analephera. Pakuti si onse obadwa mwa Israeli amene ndi Israeli. Kapena kuti ana ake chifukwa anachokera mwa Abrahamu. Koma zidzukulu zako zidzachokera mwa Isake. Kutanthauza kuti, si ana obadwa mʼthupi amene ndi ana a Mulungu koma ndi ana a lonjezano amene amatengedwa kukhala zidzukulu za Abrahamu. Pakuti Mulungu analonjeza ponena kuti, “Pa nthawi yake ngati yomwe ino chaka chamawa ndidzabweranso, ndipo Sara adzakhala ndi mwana wamwamuna.”

Ndipo si pokhapo ayi. Ana awiri a Rebeka aja abambo awo anali mmodzi, kholo lathu Isake. Komabe, ana amapasawa asanabadwe kapena asanachite chilichonse chabwino kapena choyipa, nʼcholinga choti chifuniro cha Mulungu chosankhiratu munthu aliyense chipitirire, osati chifukwa cha ntchito za munthu koma chifuniro cha Iye mwini, anawuza Rebeka kuti, “Wamkulu adzatumikira wamʼngʼono.” Monga momwe kwalembedwa kuti, “Ine ndinakonda Yakobo, koma ndinamuda Esau.”

Nanga tsono tidzanena chiyani? Kodi Mulungu ndi osalungama? Ayi, ndi pangʼono pomwe! Pakuti Mulungu anawuza Mose kuti,

“Ine ndidzachitira chifundo amene ndikufuna kumuchitira chifundo,

ndipo ndidzakomera mtima amene ndikufuna kumukomera mtima.”

Nʼchifukwa chake, izi sizitengera zokhumba za munthu kapena kuyesetsa koma chifundo cha Mulungu. Malemba akuti Mulungu anamuwuza Farao kuti, “Ine ndakuyika kukhala mfumu ndi cholinga choti ndionetse mphamvu zanga, kuti mwa iwe dzina langa litchuke pa dziko lonse lapansi.” Choncho Mulungu amachitira chifundo munthu amene akufuna kumuchitira chifundo ndipo amawumitsa mtima munthu amene Iye akufuna kumuwumitsa mtima.

Tsono mmodzi wa inu nʼkundifunsa kuti, “Nanga nʼchifukwa chiyani Mulungu amatipeza olakwa? Nanga ndani amene amakana chifuniro chake?” Koma ndiwe yani, munthu wamba, woti nʼkutsutsana ndi Mulungu? “Kodi chimene chinawumbidwa nʼkufunsa amene anachiwumba kuti, ‘Kodi unandiwumbiranji motere?’ ” Kodi wowumba alibe ufulu wowumba kuchokera ku dothi lomwelo mbiya yamtengowapatali ndi ina yamtengo wotsika?

Read More of Aroma 9