Miyambo 7:6-20 CCL

Miyambo 7:6-20

Tsiku lina pa zenera la nyumba yanga

ndinasuzumira pa zenera.

Ndinaona pakati pa anthu opusa,

pakati pa anyamata,

mnyamata wina wopanda nzeru.

Iye ankayenda njira yodutsa pafupi ndi nyumba ya mkaziyo,

kuyenda molunjika nyumba ya mkaziyo.

Inali nthawi yachisisira madzulo,

nthawi ya usiku, kuli mdima.

Ndipo mkaziyo anadzakumana naye,

atavala ngati munthu wachiwerewere wa mtima wonyenga.

(Mkaziyo ndi wolongolola ndiponso nkhutukumve,

iye ndi wosakhazikika pa khomo.

Mwina umupeza pa msewu, mwina umupeza pa msika,

ndipo amadikirira munthu pa mphambano iliyonse).

Tsono amagwira mnyamatayo ndi kupsompsona

ndi nkhope yake yopanda manyazi amamuwuza kuti,

“Ndinayenera kupereka nsembe zachiyanjano.

Lero ndakwaniritsa malumbiro anga.

Choncho ndinabwera kudzakumana nawe;

ndinkakufunafuna ndipo ndakupeza!

Pa bedi panga ndayalapo

nsalu zosalala zokongola zochokera ku Igupto.

Pa bedi panga ndawazapo zonunkhira

za mure, mafuta onunkhira a aloe ndi sinamoni.

Bwera, tiye tikhale malo amodzi kukondwerera chikondi mpaka mmawa;

tiye tisangalatsane mwachikondi!

Mwamuna wanga kulibe ku nyumbako;

wapita ulendo wautali:

Anatenga thumba la ndalama

ndipo adzabwera ku nyumba mwezi ukakhwima.”

Read More of Miyambo 7