Miyambo 7:21-27 CCL

Miyambo 7:21-27

Ndi mawu ake onyengerera amamukakamiza mnyamatayo;

amukopa ndi mawu ake oshashalika.

Nthawi yomweyo chitsiru chimamutsatira mkaziyo

ngati ngʼombe yopita kukaphedwa,

monga momwe mbawala ikodwera mu msampha,

mpaka muvi utalasa chiwindi chake,

chimakhala ngati mbalame yothamangira mʼkhwekhwe,

osadziwa kuti moyo wake uwonongeka.

Tsono ana inu, ndimvereni;

mvetsetsani zimene ndikunena.

Musatengeke mtima ndi njira za mkazi ameneyu;

musasochere potsata njira zake.

Paja iye anagwetsa anthu ambiri;

wapha gulu lalikulu la anthu.

Nyumba yake ndi njira yopita ku manda,

yotsikira ku malo a anthu akufa.

Read More of Miyambo 7