Miyambo 5:1-14 CCL

Miyambo 5:1-14

Chenjezo kwa Mkazi Wachigololo

Mwana wanga, mvetsera bwino za nzeru zimene ndikukuwuzazi,

tchera khutu ku mawu odziwitsa bwino zinthu ndikukupatsa,

kuti uthe kuchita zinthu mochenjera ndi mwanzeru

ndiponso kuti utetezedwe ku mayankhulidwe a mkazi wachilendo.

Pakuti mkazi wachigololo ali ndi mawu okoma ngati uchi.

Zoyankhula zake ndi zosalala ngati mafuta,

koma kotsirizira kwake ngowawa ngati ndulu;

ngakuthwa ngati lupanga lakuthwa konsekonse.

Mapazi ake amatsikira ku imfa;

akamayenda ndiye kuti akupita ku manda.

Iye saganizirapo za njira ya moyo;

njira zake ndi zokhotakhota koma iye sadziwa izi.

Tsopano ana inu, mundimvere;

musawasiye mawu anga.

Uziyenda kutali ndi mkazi wotereyo,

usayandikire khomo la nyumba yake,

kuopa kuti ungadzalanditse ulemerero wako kwa anthu ena;

ndi zaka zako kwa anthu ankhanza,

kapenanso alendo angadyerere chuma chako

ndi phindu la ntchito yako kulemeretsa anthu ena.

Potsiriza pa moyo wako udzabuwula,

thupi lako lonse litatheratu.

Ndipo udzati, “Mayo ine, ndinkadana ndi kusunga mwambo!

Mtima wanga unkanyoza chidzudzulo!

Sindinamvere aphunzitsi anga

kapena alangizi anga.

Ine ndatsala pangʼono kuti ndiwonongeke

pakati pa msonkhano wonse.”

Read More of Miyambo 5