Miyambo 4:20-27 CCL

Miyambo 4:20-27

Mwana wanga, mvetsetsa zimene ndikunena;

tchera khutu ku mawu anga.

Usayiwale malangizo angawa,

koma uwasunge mu mtima mwako.

Pakuti amapatsa moyo kwa aliyense amene awapeza

ndipo amachiritsa thupi lake lonse.

Ndipotu mtima wako uziwuyangʼanira bwino ndithu

pakuti ndiwo magwero a moyo.

Usiyiretu kuyankhula zokhotakhota;

ndipo ulekeretu kuyankhula zinthu zonyansa.

Maso ako ayangʼane patsogolo;

uziyangʼana kutsogolo molunjika.

Uzilingalira bwino kumene kupita mapazi ako

ndipo njira zako zonse zidzakhala zosakayikitsa.

Usapatukire kumanja kapena kumanzere;

usapite kumene kuli zoyipa.

Read More of Miyambo 4