Miyambo 31:1-9 CCL

Miyambo 31:1-9

Mawu a Mfumu Lemueli

Nawa mawu a mfumu Lemueli wa ku Massa amene anamuphunzitsa amayi ake:

Nʼchiyani mwana wanga? Nʼchiyani mwana wa mʼmimba mwanga?

Nʼchiyani iwe mwana wanga amene ndinachita kupempha ndi malumbiro?

Usapereke mphamvu yako kwa akazi.

Usamayenda nawo amenewa popeza amawononga ngakhale mafumu.

Iwe Lemueli si choyenera kwa mafumu,

mafumu sayenera kumwa vinyo.

Olamulira asamalakalake chakumwa choledzeretsa

kuopa kuti akamwa adzayiwala malamulo a dziko,

nayamba kukhotetsa zinthu zoyenera anthu osauka.

Perekani chakumwa choledzeretsa kwa amene ali pafupi kufa,

vinyo kwa amene ali pa mavuto woopsa;

amwe kuti ayiwale umphawi wawo

asakumbukirenso kuvutika kwawo.

Yankhula mʼmalo mwa amene sangathe kudziyankhulira okha.

Uwayankhulire anthu onse osiyidwa pa zonse zowayenera.

Yankhula ndi kuweruza mwachilungamo.

Uwateteze amphawi ndi osauka.

Read More of Miyambo 31