Miyambo 29:19-27 CCL

Miyambo 29:19-27

Munthu wantchito sangalangizidwe ndi mawu okha basi;

ngakhale awamvetse mawuwo sadzatha kuchitapo kanthu.

Ngakhale munthu wa uchitsiru nʼkuti ndiponi popeza chikhulupiriro chilipo

kuposa munthu wodziyesa yekha kuti ndi wanzeru poyankhula.

Ngati munthu asasatitsa wantchito wake kuyambira ali mwana,

potsirizira adzapeza kuti wantchitoyo wasanduka mlowachuma wake.

Munthu wamkwiyo amayambitsa mikangano,

ndipo munthu waukali amachita zolakwa zambiri.

Kunyada kwa munthu kudzamutsitsa,

koma munthu wodzichepetsa amalandira ulemu.

Woyenda ndi munthu wakuba ndi mdani wa moyo wake womwe;

amalumbira koma osawulula kanthu.

Kuopa munthu kudzakhala ngati msampha,

koma aliyense amene amadalira Yehova adzatetezedwa.

Anthu ambiri amafunitsitsa kuti wolamulira awakomere mtima,

koma munthu amaweruzidwa mwachilungamo ndi thandizo la Yehova basi.

Anthu olungama amanyansidwa ndi anthu achinyengo;

koma anthu oyipa amanyansidwa ndi anthu a mtima wowongoka.

Read More of Miyambo 29