Miyambo 29:1-9 CCL

Miyambo 29:1-9

Munthu amene amawumitsabe khosi lake atadzudzulidwa kwambiri,

adzawonongeka mwadzidzidzi popanda chomuchiritsa.

Anthu olungama akamalamulira mʼdziko anthu amakondwa,

koma ngati dziko lilamulidwa ndi anthu oyipa mtima anthu amadandaula.

Munthu amene amakonda nzeru amasangalatsa abambo ake,

koma woyenda ndi akazi achiwerewere amasakaza chuma chake.

Mfumu imalimbitsa dziko poweruza mwachilungamo,

koma mfumu imene imawumiriza anthu kuti ayipatse mphatso imawononga dziko.

Munthu woshashalika mnzake,

akudziyalira ukonde mapazi ake.

Munthu woyipa amakodwa ndi machimo ake,

koma wochita chilungamo amayimba lokoma.

Munthu wolungama amasamalira anthu osauka,

koma woyipa salabadira zimenezi.

Anthu onyoza atha kuwutsa ziwawa mu mzinda,

koma anthu anzeru amaletsa ukali.

Ngati munthu wanzeru atsutsana ndi chitsiru,

chitsirucho chimachita phokoso ndi kumangoseka ndipo sipakhala mtendere.

Read More of Miyambo 29