Miyambo 27:23-27, Miyambo 28:1-6 CCL

Miyambo 27:23-27

Uzidziwe bwino nkhosa zako momwe zilili.

Kodi usamalire bwino ziweto zako?

Paja chuma sichikhala mpaka muyaya,

ndipo ufumu sukhala mpaka mibado yonse.

Pamene udzu watha, msipu nʼkumera;

ndipo atatuta udzu wa ku mapiri,

ana ankhosa adzakupatsani chovala

ndipo pogulitsa mbuzi mudzapeza ndalama yogulira munda.

Mudzakhala ndi mkaka wambuzi wambiri

kuti muzidya inuyo ndi banja lanu

ndi kudyetsa antchito anu aakazi.

Read More of Miyambo 27

Miyambo 28:1-6

Munthu woyipa amathawa ngakhale palibe wina womuthamangitsa,

koma wolungama ndi wolimba mtima ngati mkango.

Pamene mʼdziko muli kuwukirana, dzikolo limakhala ndi olamulira ambiri,

koma anthu omvetsa ndi odziwa zinthu bwino ndiwo angakhazikitse bata mʼdzikolo nthawi yayitali.

Munthu wosauka amene amapondereza osauka anzake

ali ngati mvula yamkuntho imene imawononga mbewu mʼmunda.

Amene amakana malamulo amatamanda anthu oyipa,

koma amene amasunga malamulo amatsutsana nawo.

Anthu oyipa samvetsa za chiweruzo cholungama,

koma amene amafuna kuchita zimene Yehova afuna amachimvetsetsa bwino.

Munthu wosauka wa makhalidwe abwino

aposa munthu wolemera wa makhalidwe okhotakhota.

Read More of Miyambo 28