Miyambo 25:11-20 CCL

Miyambo 25:11-20

Mawu amodzi woyankhulidwa moyenera

ali ngati zokongoletsera zagolide mʼzotengera zasiliva.

Kwa munthu womvetsa bwino, kudzudzula kwa munthu wanzeru kuli ngati ndolo zagolide

kapena chodzikongoletsera china cha golide wabwino kwambiri.

Wamthenga wodalirika ali ngati madzi ozizira pa nthawi yokolola

kwa anthu amene amutuma;

iye amaziziritsa mtima bwana wake.

Munthu wonyadira mphatso imene sayipereka

ali ngati mitambo ndi mphepo yopanda mvula.

Kupirira ndiye kumagonjetsa mfumu,

ndipo kufewa mʼkamwa kutha kumafatsitsa munthu wowuma mtima.

Ngati upeza uchi, ingodya okukwanira,

kuopa ungakoledwe nawo ndi kuyamba kusanza.

Uzipita kamodzikamodzi ku nyumba ya mnzako

ukawirikiza kupita, udzadana naye.

Munthu wochitira mnzake umboni wonama,

ali ngati chibonga kapena lupanga kapena muvi wakuthwa.

Kudalira munthu wosankhulupirika pa nthawi ya mavuto,

kuli ngati dzino lobowoka kapena phazi lolumala.

Kuyimbira nyimbo munthu wachisoni

kuli ngati kuvula zovala pa nyengo yozizira

kapena kuthira mchere pa chilonda.

Read More of Miyambo 25