Miyambo 24:23-34
Malangizo Enanso a Anthu Anzeru
Malangizo enanso a anthu anzeru ndi awa:
Kukondera poweruza mlandu si chinthu chabwino:
Aliyense amene amawuza munthu wolakwa kuti, “Iwe ndi munthu wosalakwa,”
anthu a mitundu yonse adzamutemberera, ndi mitundu ya anthu idzayipidwa naye.
Koma olanga anthu oyipa zinthu zidzawayendera bwino
ndipo madalitso ochuluka adzakhala pa iwo.
Woyankhula mawu owona
ndiye amaonetsa chibwenzi chenicheni.
Ugwiriretu ntchito zako zonse,
makamaka za ku munda
ndipo pambuyo pake uyambe kumanga nyumba.
Usakhale mboni yotsutsa mnzako popanda chifukwa,
kapena kugwiritsa ntchito pakamwa pako kunena zachinyengo.
Usanene kuti, “Ine ndidzamuchitira iye monga momwe wandichitira ine;
ndidzamubwezera munthu ameneyo zimene anandichitira.”
Ndinkayenda mʼmbali mwa munda wa munthu waulesi
ndinadutsa munda wamphesa wa munthu wopanda nzeru.
Ndinapeza kuti paliponse mʼmundamo munali mutamera minga,
mʼnthaka imeneyo munali mutamera khwisa,
ndipo mpanda wake wamiyala unali utawonongeka.
Tsono nditaona ndinayamba kuganizira mu mtima mwanga
ndipo ndinatolapo phunziro ili:
Ukati, “Bwanji ndigone pangʼono,” kapena “Ndiwodzereko pangʼono,”
kapenanso “Ndipinde manja pangʼono kuti ndipumule,”
umphawi udzafika pa iwe ngati mbala
ndipo usiwa udzakupeza ngati munthu wachifwamba.