Miyambo 23:29-35, Miyambo 24:1-4 CCL

Miyambo 23:29-35

Ndani ali ndi tsoka? Ndani ali ndi chisoni?

Ndani ali pa mkangano? Ndani ali ndi madandawulo?

Ndani ali ndi zipsera zosadziwika uko zachokera? Ndani ali ndi maso ofiira?

Ndi amene amakhalitsa pa mowa,

amene amapita nalawa vinyo osakanizidwa.

Usatengeke mtima ndi kufiira kwa vinyo,

pamene akuwira mʼchikho

pamene akumweka bwino!

Potsiriza pake amaluma ngati njoka,

ndipo amajompha ngati mphiri.

Maso ako adzaona zinthu zachilendo

ndipo maganizo ndi mawu ako adzakhala osokonekera.

Udzakhala ngati munthu amene ali gone pakati pa nyanja,

kapena ngati munthu wogona pa msonga ya mlongoti ya ngalawa.

Iwe udzanena kuti, “Anandimenya, koma sindinapwetekedwe!

Andimenya koma sindinamve kanthu!

Kodi ndidzuka nthawi yanji?

Ndiye ndifunefunenso vinyo wina.”

Read More of Miyambo 23

Miyambo 24:1-4

Usachitire nsanje anthu oyipa,

usalakalake kuti uzikhala nawo,

pakuti mitima yawo imalingalira chiwawa,

ndipo pakamwa pawo pamayankhula zoyambitsa mavuto.

Nyumba imamangidwa ndi anthu anzeru,

ndipo imakhazikika ndi anthu odziwa zinthu;

Munthu wodziwa zinthu angathe kudzaza zipinda zake

ndi chuma chamtengowapatali ndiponso chabwino.

Read More of Miyambo 24