Miyambo 11:29-31, Miyambo 12:1-7 CCL

Miyambo 11:29-31

Wovutitsa a mʼnyumba mwake adzalowa mʼmavuto,

ndipo chitsiru chidzakhala kapolo wa munthu wa nzeru.

Chipatso cha ntchito zabwino ndi moyo,

ndipo kusatsata malamulo kumawonongetsa moyo.

Ngati anthu olungama amalandira mphotho zawo pa dziko lapansi,

kuli bwanji anthu osapembedza ndi ochimwa!

Read More of Miyambo 11

Miyambo 12:1-7

Munthu amene amakonda mwambo amakonda kudziwa zinthu,

koma amene amadana ndi chidzudzulo ndi wopusa.

Munthu wabwino amapeza kuyanja pamaso pa Yehova,

koma Yehova amatsutsa munthu wochita chinyengo.

Munthu sangakhazikike bwino pochita zoyipa,

koma maziko a anthu olungama sadzatekeseka.

Mkazi wakhalidwe labwino ali ngati chipewa chaufumu kwa mwamuna wake,

koma mkazi wochititsa manyazi ali ngati chilonda cha mafinya kwa mwamuna wake.

Maganizo a anthu olungama ndi owongoka,

koma malangizo a anthu oyipa ndi achinyengo.

Mawu a anthu oyipa ndi ophetsa,

koma mawu a anthu olungama amapulumutsa.

Anthu oyipa amagonjetsedwa ndipo amayiwalika,

koma nyumba ya anthu olungama idzakhalabe.

Read More of Miyambo 12