Numeri 23:27-30, Numeri 24:1-25, Numeri 25:1-18 CCL

Numeri 23:27-30

Uthenga Wachitatu wa Balaamu

Kenaka Balaki anati kwa Balaamu, “Bwera ndikutengere ku malo ena. Mwina chidzamukondweretsa Mulungu kuti uwatemberere kumeneko mʼmalo mwanga.” Ndipo Balaki anamutengera Balaamu pamwamba pa Peori, poyangʼanana ndi chipululu.

Balaamu anati kwa Balaki, “Mundimangire maguwa ansembe asanu ndi awiri pano ndipo mundikonzere ngʼombe zazimuna zisanu ndi ziwiri, nkhosa zazimuna zisanu ndi ziwiri.” Balaki anachita monga Balaamu ananenera ndipo anapereka nsembe ngʼombe imodzi yayimuna ndi nkhosa imodzi yayimuna pa guwa lililonse.

Read More of Numeri 23

Numeri 24:1-25

Tsopano Balaamu ataona kuti kunakomera Yehova kudalitsa Israeli, sanapitenso ku mawula monga ankachitira kale, koma kuyangʼana ku chipululu. Balaamu atayangʼana, anaona Aisraeli atamanga misasa yawo fuko ndi fuko. Pamenepo mzimu wa Mulungu unabwera pa iye ndipo ananena uthenga wake:

“Uthenga wa Balaamu mwana wa Beori,

uthenga wa amene diso lake ndi lotsekuka,

uthenga wa amene amamva mawu a Mulungu,

yemwe amaona masomphenya wochokera kwa Wamphamvuzonse,

yemwe amagwa chafufumimba, koma maso ake ali chipenyere:

“Matenti ako ndi okongola kwambiri iwe Yakobo,

misasa yako, iwe Israeli!

“Monga zigwa zotambalala,

monga minda mʼmbali mwa mtsinje,

monga aloe wodzalidwa ndi Yehova,

monga mikungudza mʼmbali mwa madzi.

Madzi adzayenderera mʼmitsuko yake;

mbewu zake zidzakhala ndi madzi ambiri.

“Mfumu yake idzakhala yamphamvu kuposa Agagi;

ufumu wake udzakwezedwa.

“Mulungu womutulutsa mʼdziko la Igupto

ali ndi mphamvu ngati za njati.

Amawononga mitundu yomuwukira

ndi kuphwanya mafupa awo,

amalasa ndi mivi yake.

Monga mkango waumuna, amabisala nagona pansi,

monga mkango waukazi, adzamuputa ndani?

“Amene adalitsa iwe, adalitsike

ndipo amene atemberera iwe, atembereredwe!”

Kenaka Balaki anakwiyira Balaamu. Anawomba mʼmanja ndi kunena naye kuti, “Ndinakuyitana kuti utemberere adani anga, koma taona, wawadalitsa katatu konseka. Tsopano choka msanga uzipita kwanu! Ndinanena kuti ndidzakulipira bwino kwambiri, koma Yehova sanafune kuti ulandire malipirowo.”

Balaamu anayankha Balaki kuti, “Kodi sindinawawuze amithenga amene munawatumiza kwa ine, kuti ngakhale Balaki atandipatsa nyumba yake yaufumu yodzaza ndi siliva ndi golide sindingathe kuchita zinthu mwa ine ndekha, zabwino kapena zoyipa, kuposa lamulo la Yehova ndi kuti ndiyenera kunena zokhazo zimene Yehova akunena? Tsopano ndikupita kwa anthu anga, koma tabwerani ndikuchenjezeni zimene anthu awa adzachitira anthu anu masiku akubwerawa.”

Uthenga Wachinayi wa Balaamu

Ndipo iye ananena uthenga wake nati,

“Uthenga wa Balaamu mwana wa Beori,

uthenga wa amene diso lake ndi lotsekuka.

Uthenga wa amene amamva mawu a Mulungu,

amene ali ndi nzeru zochokera kwa Wammwambamwamba,

amene amaona masomphenya wochokera kwa Wamphamvuzonse,

amene amagwa chafufumimba koma diso lake lili lotsekuka:

“Ndikumuona iye koma osati tsopano;

ndikumupenya iye koma osati pafupi.

Nyenyezi idzatuluka mwa Yakobo;

ndodo yaufumu idzatuluka mwa Israeli.

Iye adzagonjetsa Mowabu

ndi kugonjetsa ana onse a Seti.

Edomu adzagonjetsedwa;

Seiri, mdani wake, adzawonongedwa

koma mphamvu za Israeli zidzachuluka.

Wolamulira adzachokera mwa Yakobo

ndipo adzawononga otsala a mu mzindamo.”

Uthenga Wachisanu wa Balaamu

Kenaka Balaamu anaona Aamaleki ndipo ananena uthenga wake uwu:

“Aamaleki anali oyamba mwa mitundu ya anthu

koma potsiriza pake adzawonongeka.”

Uthenga Wachisanu ndi Chimodzi wa Balaamu

Kenaka anaonanso Akeni ndipo ananena uthenga wake,

“Malo amene mukukhalamo ndi otetezedwa,

chisa chanu chinayikidwa pa thanthwe;

komabe inu Akeni mudzawonongedwa,

pamene Asuri adzakutengeni ukapolo.”

Uthenga Wachisanu ndi Chiwiri wa Balaamu

Ndipo ananenanso uthenga wina kuti,

“Aa, ndani adzakhala ndi moyo Mulungu akachita zimenezi?

Sitima zapamadzi zidzabwera kuchokera ku madooko a Kitimu;

kupondereza Asuri ndi Eberi,

koma iwonso adzawonongeka.”

Pamenepo Balaamu ananyamuka ndi kubwerera kwawo ndipo Balaki anapitanso njira yake.

Read More of Numeri 24

Numeri 25:1-18

Aisraeli Achita Chigololo

Aisraeli akukhala ku Sitimu, anayamba kuchita chigololo ndi akazi a ku Mowabu, amene ankawayitana ku nsembe za milungu yawo. Anthuwo anadya chakudya chopereka kwa milungu ndi kupembedza milunguyo. Motero Aisraeli anapembedza nawo Baala-Peori ndipo Yehova anawapsera mtima kwambiri.

Pamenepo Yehova anawuza Mose kuti, “Tenga atsogoleri onse a anthu awa, uwaphe poyera, pamaso pa Yehova kuti mkwiyo waukulu wa Yehova uchoke pa Israeli.”

Choncho Mose anawuza oweruza a Israeli kuti, “Aliyense wa inu ayenera kupha anthu ake amene anapembedza nawo Baala-Peori.”

Kenaka mwamuna wina wa ku Israeli anabweretsa ku banja lake mkazi wa Chimidiyani pamaso pa Mose ndi anthu onse a Israeli pamene ankalira pa khomo la tenti ya msonkhano. Finehasi mwana wa Eliezara, mwana wa wansembe Aaroni ataona izi, anachoka pa msonkhanowo, natenga mkondo mʼdzanja lake. Ndipo anatsatira Mwisraeliyu mpaka mʼtenti yake. Anasolola mkondowo ndi kubaya awiriwo kupyola Mwisraeliyo mpaka mʼthupi la mkaziyo. Pamenepo mliri unaleka pakati pa Aisraeli. Pa mliriwo, anthu okwana 24,000 anafa.

Yehova anawuza Mose kuti, “Finehasi mwana wa Eliezara, mwana wa wansembe Aaroni wabweza mkwiyo wanga pa Aisraeli chifukwa sanalole kuti wina aliyense apembedze mulungu wina koma Ine ndekha. Nʼchifukwa chake sindinawawononge mu mkwiyo wanga. Tsono muwuze kuti ndikhazikitsa pangano langa la mtendere ndi iye. Ndikupangana naye pangano la unsembe wosatha, iyeyo pamodzi ndi zidzukulu zake zonse, chifukwa sanalole kuti anthu awukire Ine Mulungu, ndipo anachita ntchito yopepesera machimo Aisraeli.”

Dzina la Mwisraeli yemwe anaphedwa ndi mkazi wa Chimidiyani anali Zimuri mwana wa Salu, mtsogoleri wa banja la Simeoni. Ndipo dzina la mkazi wa Chimidiyani, yemwe anaphedwayo, linali Kozibi mwana wa Zuri, mtsogoleri wa fuko la ku Midiyaniko.

Yehova anawuza Mose kuti, “Amidiyani ndi adani anu ndipo uwaphe, chifukwa ankakuonani inu ngati adani awo pamene anakupusitsani pa nkhani ya ku Peori, ndiponso za mlongo wawo Kozibi, mwana wamkazi wa mtsogoleri wa Amidiyani, mkazi yemwe anaphedwa pamene mliri unabwera chifukwa cha zimene zinachitika ku Peori.”

Read More of Numeri 25