Nehemiya 7:4-73, Nehemiya 8:1-18 CCL

Nehemiya 7:4-73

Mndandanda wa Anthu Oyamba Kubwera Kuchokera ku Ukapolo

Tsono mzinda wa Yerusalemu unali wotambasuka ndiponso waukulu koma munali anthu ochepa ndipo nyumba zinali zisanamangidwe. Ndipo Mulungu wanga anayika mu mtima mwanga maganizo oti ndisonkhanitse anthu olemekezeka, akuluakulu ndi anthu onse kuti alembetse mayina mwa mabanja awo. Ndinapeza buku limene munalembedwa mayina a mabanja a iwo amene anayamba kubwera kuchokera ku ukapolo. Izi ndi zimene ndinazipeza zitalembedwa mʼmenemo:

Awa ndi anthu a mʼchigawo cha Yuda amene anabwerera kuchokera ku ukapolo amene Nebukadinezara mfumu ya Babuloni anawatenga ukapolo. Iwo anabwerera ku Yerusalemu ndi ku Yuda, aliyense ku mzinda wa makolo ake. Anabwera pamodzi ndi atsogoleri awa: Zerubabeli, Yesuwa, Nehemiya, Azariya, Raamiya, Nahamani, Mordekai, Bilisani, Misipereti, Bigivai, Nehumu ndi Baana.

Tsono chiwerengero cha anthu a ku Israeli chinali chotere:

Zidzukulu za Parosi 2,172Zidzukulu za Sefatiya 372Zidzukulu za Ara 652Zidzukulu za Pahati-Mowabu (kudzera mu mʼbado wa Yesuwa ndi Yowabu) 2,818Zidzukulu za Elamu 1,254Zidzukulu za Zatu 845Zidzukulu za Zakai 760Zidzukulu za Binuyi 648Zidzukulu za Bebai 628Zidzukulu za Azigadi 2,322Zidzukulu za Adonikamu 667Zidzukulu za Abigivai 2,067Zidzukulu za Adini 655Zidzukulu za Ateri (kudzera mwa Hezekiya) 98Zidzukulu za Hasumu 328Zidzukulu za Bezayi 324Zidzukulu za Harifu 112Zidzukulu za Gibiyoni 95.

Anthu a ku Betelehemu ndi Netofa188Anthu a ku Anatoti 128Anthu a ku Beti-Azimaveti 42Anthu a ku Kiriati Yeyarimu Kefira ndi Beeroti 743Anthu a ku Rama ndi Geba 621Anthu a ku Mikimasi 122Anthu a ku Beteli ndi Ai 123Anthu a ku Nebo winayo 52Ana a Elamu wina 1,254Zidzukulu za Harimu 320Zidzukulu za Yeriko 345Zidzukulu za Lodi, Hadidi ndi Ono721Zidzukulu za Senaya 3,930.

Ansembe anali awa:

A banja la Yedaya (ndiye kuti zidzukulu za Yesuwa) 973Zidzukulu za Imeri 1,052Zidzukulu za Pasi-Huri 1,247Zidzukulu za Harimu 1,017.

Alevi anali awa:

A banja la Yesuwa ndi Kadimieli, ndiye kuti zidzukulu za Hodaviya 74.

Anthu oyimba:

   Zidzukulu za Asafu 148.

Alonda a ku Nyumba ya Mulungu anali awa:

Zidzukulu za   Salumu, Ateri, Talimoni, Hatita ndi Sobai 138.

Anthu ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu anali awa:

Zidzukulu za   Ziha, zidzukulu za Hasufa, zidzukulu za Tabaoti,Zidzukulu Kerosi, zidzukulu za Siya, zidzukulu za PadoniZidzukulu za Lebana za Hagaba, ndi za Salimayi,Zidzukulu za Hanani, zidzukulu za Gideli, zidzukulu za Gahari,Zidzukulu za Reyaya, zidzukulu za Rezini, zidzukulu za Nehoda,Zidzukulu za Gazamu, zidzukulu za Uza, zidzukulu za Paseya,Zidzukulu za Besai, zidzukulu za Meunimu, zidzukulu za Nefusimu,Zidzukulu za Bakibuku, zidzukulu za Hakufa, zidzukulu za Harihuri,Zidzukulu za Baziliti, zidzukulu za Mehida, zidzukulu za Harisa,Zidzukulu za Barikosi, zidzukulu za Sisera, zidzukulu za TemaZidzukulu za Neziya, ndi zidzukulu za Hatifa.

Zidzukulu za antchito a Solomoni:

Zidzukulu za   Sotai, zidzukulu za Sofereti, zidzukulu za Peridazidzukulu za Yaala, zidzukulu za Darikoni, zidzukulu za Gideli,zidzukulu za Sefatiya, zidzukulu za Hatilu   zidzukulu za Pokereti-Hazebaimu ndi zidzukulu Amoni.Anthu onse ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu pamodzi ndi zidzukulu za antchito a Solomoni analipo 392.

Ali munsiwa anachokera ku Teli-Mela, Teri-Harisa, Kerubi, Adoni, ndi Imeri, koma sanathe kunena mwa tchutchutchu kuti makolo awo kapena mafuko awo analidi Aisraeli kapena ayi.

Zidzukulu za   Delaya, zidzukulu za Tobiya ndi zidzukulu za Nekoda 642.

Ndiponso ena pakati pa ansembe anali awa:

zidzukulu za

Hobiya, zidzukulu za Hakozi ndi zidzukulu za Barizilai (munthu amene anakwatira mwana wamkazi wa Barizilai wa ku Giliyadi ndipo amatchedwa dzina limenelo).

Iwowa anafufuzafufuza mayina awo mʼbuku la mibado ya mabanja awo ndipo sanapeze mayina awo kotero anachotsedwa pa unsembe nawerengedwa ngati odetsedwa pa chipembedzo. Choncho bwanamkubwa anawawuza anthuwo kuti asamadye nawo chakudya china chilichonse choperekedwa kwa Mulungu mpaka patapezeka wansembe wodziwa kugwiritsa bwino ntchito ya Urimu ndi Tumimu.

Chiwerengero chonse cha anthuwa chinali 42,360. Kuwonjezera pamenepa panali antchito awo aamuna ndi aakazi 7,337 ndiponso anthu aamuna ndi aakazi oyimba nyimbo okwanira 245. Panali akavalo 736, abulu angʼonoangʼono 245. Ngamira zawo zinalipo 435 ndipo abulu analipo 6,720.

Atsogoleri ena a mabanja anapereka mphatso zothandizira ntchito. Bwanamkubwa anapereka ku thumba losungira chuma, ndalama zagolide za makilogalamu asanu ndi atatu, mabeseni makumi asanu ndi zovala za ansembe 530. Atsogoleri ena amabanja anapereka ku thumba losungira chuma ndalama zagolide zokwana makilogalamu 168, ndiponso ndalama za siliva zokwana makilogalamu 1,250. Anthu ena onse otsala anapereka ndalama zagolide zokwana makilogalamu 168, ndalama za siliva zokwana makilogalamu 140, ndiponso zovala za ansembe 67.

Choncho ansembe, Alevi, alonda a Nyumba ya Mulungu, anthu oyimba nyimbo, ena mwa anthu wamba, ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu pamodzi ndi Aisraeli ena onse ankakhala mʼmizinda yawo.

Ezara Awerenga Malamulo

Pofika mwezi wachisanu ndi chiwiri Aisraeli onse anali atakhazikika mʼmizinda yawo.

Read More of Nehemiya 7

Nehemiya 8:1-18

Anthu onse anasonkhana ngati munthu mmodzi pabwalo limene lili patsogolo pa Chipata cha Madzi. Iwo anawuza mlembi Ezara kuti abwere ndi buku la malamulo a Mose limene Yehova anapereka kwa Aisraeli.

Choncho pa tsiku loyamba la mwezi wachisanu ndi chiwiri wansembe Ezara, anabwera ndi buku la malamulo ku msonkhano wa amuna, akazi ndi ana onse amene ankatha kumvetsa zinthu bwino. Choncho Ezara anawerenga bukulo atayangʼana bwalo la Chipata cha Madzi kuyambira mmawa mpaka masana pamaso pa amuna, akazi ndi onse amene ankamvetsa bwino zinthu. Ndipo anthu onse anatchera khutu kuti amve malamulowo.

Mlembi Ezara anayimirira pa nsanja ya mitengo imene anthu anamanga chifukwa cha msonkhanowu. Ku dzanja lake lamanja kunayimirira Matitiya, Sema, Anaya, Uriya, Hilikiya ndi Maaseya, ndipo kudzanja lake lamanzere kunali Pedaya, Misaeli, Malikiya, Hasumu, Hasibadana, Zekariya ndi Mesulamu.

Tsono Ezara anatsekula buku, akuona popeza anayima pa nsanja. Pamene anafutukula bukulo anthu onse anayimirira. Ezara anatamanda Yehova, Mulungu wamkulu, ndipo anthu onse anakweza manja awo ndi kuyankha kuti, “Ameni, ameni.” Pambuyo pake onse anaweramitsa pansi mitu yawo napembedza Yehova akanali chizolikire choncho.

Anthuwo atayimiriranso Alevi awa: Yesuwa, Bani, Serebiya, Yamini, Akubu, Sabetayi, Hodiya, Maaseya, Kerita, Azariya, Yozabadi, Hanani ndi Pelaya anawathandiza kuti amvetse bwino malamulowo. Iwo anawerenga buku la malamulo a Mulungu momveka bwino ndi kutanthauzira mawuwo kuti anthu amvetse bwino zowerengedwazo.

Tsono bwanamkubwa Nehemiya pamodzi ndi wansembe ndi mlembi Ezara komanso Alevi amene amaphunzitsa anthu anati kwa anthu onse, “Lero ndi tsiku lopatulika kwa Yehova Mulungu wanu. Musakhale ndi chisoni ndipo musalire.” Anayankhula choncho popeza anthu onse ankalira atamva mawu a buku la malamulo lija.

Nehemiya anatinso, “Pitani, kachiteni phwando ku nyumba ndipo mukawagawireko ena amene alibe kanthu kalikonse popeza lero ndi tsiku lopatulika kwa Yehova. Musakhale ndi chisoni, pakuti chimwemwe cha Yehova ndiye mphamvu yanu.”

Alevi anakhalitsa bata anthu onse powawuza kuti, “Khalani chete, pakuti lero ndi tsiku lopatulika ndipo musakhale ndi chisoni.”

Anthu onse anachoka kupita kukadya ndi kumwa. Chakudya china anatumiza kwa anzawo. Choncho panali chikondwerero chachikulu popeza tsopano anali atamvetsa bwino mawu a Mulungu amene anawawerengera ndi kuwafotokozerawo.

Mmawa mwake atsogoleri a mabanja pamodzi ndi ansembe ndi alevi anasonkhana kwa Ezara, mlembi wa malamulo kuti aphunzire mawu a malamulowo. Tsono anapeza kuti zinalembedwa mʼbuku la malamulo kuti Yehova analamula kudzera mwa Mose kuti Aisraeli azikhala mʼzithando pa nthawi yonse ya chikondwerero cha mwezi wachisanu ndi chiwiri. Choncho analengeza ndi kufalitsa mʼmizinda yawo yonse ndi mu Yerusalemu kuti, “Pitani ku phiri mukadule nthambi za mtengo wa olivi, za mtengo wa olivi wa kutchire, za mtengo wa mchisu, za mtengo wa mgwalangwa ndiponso za mitengo ina ya masamba, zomangira zithando monga zalembedweramu ndi kubwera nazo.”

Choncho anthu anapita kukatenga nthambi ndipo aliyense anadzimangira misasa pa denga ya nyumba yake, mʼmabwalo awo, mʼmabwalo a Nyumba ya Mulungu, mʼbwalo la pa Chipata cha Madzi ndiponso mʼbwalo la pa Chipata cha Efereimu. Gulu lonse la anthu limene linabwera ku ukapolo linamanga misasa ndipo linakhala mʼmenemo. Kuyambira nthawi ya Yoswa mwana wa Nuni mpaka tsiku limenelo nʼkuti Aisraeli asanachitepo zimenezi. Choncho panali chimwemwe chachikulu.

Tsiku ndi tsiku, kuyambira tsiku loyamba mpaka lomaliza, Ezara ankawerenga buku la malamulo a Mulungu. Anthu anachita chikondwerero masiku asanu ndi awiri. Pa tsiku lachisanu ndi chitatu panachitika msonkhano potsata buku la malamulo lija.

Read More of Nehemiya 8