Mateyu 18:10-35 CCL

Mateyu 18:10-35

Fanizo la Nkhosa Yotayika

“Onetsetsani kuti musanyoze mmodzi wa anawa. Pakuti ndikuwuzani kuti angelo awo kumwamba amakhala pamaso pa Atate anga akumwamba nthawi zonse.” (Mwana wa Munthu anabwera kudzapulumutsa chimene chinatayika).

“Kodi mukuganiza bwanji? Ngati munthu ali ndi nkhosa 100 ndipo imodzi nʼkusowa, kodi sasiya 99 zija mʼmapiri ndi kupita kukafuna imodzi yosocherayo? Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti akayipeza amasangalala kwambiri chifukwa cha nkhosa imodziyo kuposa nkhosa 99 zimene sizinasochere. Chimodzimodzinso Atate anu akumwamba safuna kuti mmodzi wa anawa atayike.

Za Mʼbale Amene Akuchimwirani

“Ngati mʼbale wako akuchimwira, pita kamuwuze cholakwa chake pa awiri. Ngati akumvera, wamubweza mʼbale wakoyo. Koma ngati sakumvera, katenge wina mmodzi kapena ena awiri, ‘kuti nkhani itsimikizike ndi umboni wa anthu awiri kapena atatu.’ Ngati iye akana kuwamvera iwo, kaneneni ku mpingo; ndipo ngati sakamvera ngakhale mpingo, muchite naye monga mukanachitira ndi wakunja kapena wolandira msonkho.

“Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti chilichonse chimene muchimanga pa dziko lapansi, chidzamangidwanso kumwamba, ndipo chilichonse chimene muchimasula pa dziko chidzamasulidwanso kumwamba.

“Komanso ndikukuwuzani inu kuti ngati awiri a inu pa dziko lapansi avomerezana kanthu kalikonse kamene mukapempha, Atate anga akumwamba adzakuchitirani. Pakuti pamene awiri kapena atatu asonkhana pamodzi mʼdzina langa, Ine ndili nawo pomwepo.”

Fanizo la Wantchito Wopanda Chifundo

Kenaka Petro anabwera kwa Yesu ndi kumufunsa kuti, “Ambuye, kodi mʼbale wanga akandichimwira ndimukhululukire kokwanira kangati? Mpaka kasanu nʼkawiri?”

Yesu anayankha kuti, “Ine ndikukuwuza iwe kuti osati kasanu nʼkawiri, koma ka 70 kuchulukitsa ndi kasanu nʼkawiri.

“Nʼchifukwa chake, ufumu wakumwamba ukufanana ndi mfumu imene inafuna kuti antchito ake abweze ngongole. Atangoyamba kulandira, anamubweretsa munthu kwa iye amene anakongola ndalama 10,000. Popeza sakanatha kubweza, bwanayo analamula kuti iye, mkazi wake, ana ake ndi zonse anali nazo zigulitsidwe kuti zibweze ngongoleyo.

“Wantchitoyo anagwada pamaso pake namupempha iye kuti, ‘Lezereni mtima ndipo ndidzabweza zonse.’ Bwana wakeyo anamuchitira chifundo, namukhululukira ngongoleyo ndipo anamulola apite.

“Koma wantchito uja atatuluka, anakumana ndi wantchito mnzake amene anakongola kwa iye madinari 100. Anamugwira, nayamba kumukanyanga pa khosi, namuwumiriza nati, ‘Bwezere zimene unakongola kwa ine!’

“Wantchito mnzakeyo anagwada namupempha iye kuti, ‘Lezere mtima ine, ndipo ndidzakubwezera.’

“Koma iye anakana. Mʼmalo mwake, anachoka nakamumangitsa kufikira atabweza ngongoleyo. Pamene antchito ena anaona zomwe zinachitikazo, anamva chisoni kwambiri ndipo anapita nakawuza bwana wawo zonse zimene zinachitika.

“Pamenepo bwanayo anayitana wantchitoyo nati, ‘Iwe wantchito woyipa mtima, ndinakukhululukira ngongole yako yonse chifukwa unandipempha. Kodi iwe sukanamuchitira chifundo wantchito mnzako monga momwe ine ndinakuchitira iwe?’ Ndi mkwiyo, bwana wakeyo anamupereka kwa oyangʼanira ndende kuti amuzuze mpaka atabweza zonse zimene anakongola.

“Umu ndi mmene Atate anga akumwamba adzachitira ndi aliyense wa inu ngati simukhululukira mʼbale wanu ndi mtima wonse.”

Read More of Mateyu 18