Mateyu 12:22-45 CCL

Mateyu 12:22-45

Mwano wa Afarisi

Pomwepo anthu anabwera naye kwa Yesu munthu wogwidwa ndi chiwanda amene anali wosaona ndi wosamva ndipo Yesu anamuchiritsa kotero kuti atatha anayamba kumva ndi kuona. Anthu onse anadabwa ndipo anati, “Kodi uyu ndi kukhala mwana wa Davide?”

Koma Afarisi atamva zimenezi, anati, “Uyu amatulutsa ziwanda ndi mphamvu ya Belezebabu mkulu wa ziwandazo.”

Yesu anadziwa maganizo awo ndipo anawawuza kuti, “Ufumu uliwonse ukagawanika mwa iwo udzawonongeka ndi mzinda uliwonse kapena banja likagawanika, mwa izo zokha sizidzayima. Ngati Satana atulutsa Satana, iye adzigawa yekha. Nanga ufumu wake ungayime bwanji? Ndipo ngati Ine nditulutsa ziwanda ndi Belezebule, anthu anu amatulutsa ziwandazo ndi chiyani? Potero tsono adzakhala oweruza anu. Koma ngati Ine ndimatulutsa ziwanda ndi Mzimu wa Mulungu, pamenepo ufumu wa Mulungu wafika pa inu.

“Kapenanso wina aliyense angathe bwanji kulowa mʼnyumba ya munthu wamphamvu ndi kunyamulamo zinthu zake, sipokhapo atayamba wamanga munthu wa mphamvuyo? Pamenepo iye akhoza kuba mʼnyumbamo.

“Iye amene sali ndi Ine atsutsana nane ndipo iye amene sasonkhanitsa pamodzi ndi Ine amamwaza. Ndipo potero Ine ndikuwuzani inu, tchimo lililonse ndi cha mwano chilichonse zidzakhululukidwa kwa anthu koma chamwano cha pa Mzimu Woyera, sichidzakhululukidwa. Aliyense amene anena mawu otsutsana ndi Mwana wa Munthu adzakhululukidwa koma aliyense wonena motsutsana ndi Mzimu Woyera sadzakhululukidwa mu mʼbado uno kapena umene ukubwerawo.

Mtengo ndi Zipatso Zake

“Mtengo wabwino umabala zipatso zabwino ndipo mtengo woyipa umabalanso zipatso zoyipa, pajatu mtengo umadziwika ndi zipatso zake. Ana anjoka inu, woyipa inu, mungathe bwanji kuyankhula kanthu kalikonse kabwino? Pakuti pakamwa pamayankhula zosefuka kuchokera mu mtima. Munthu wabwino amatulutsa zinthu zabwino zomwe zili mumtima mwake ndipo munthu woyipa amatulutsanso zinthu zoyipa zomwe zili mwa iye. Ine ndikukuwuzani kuti pa tsiku la chiweruziro munthu adzazengedwa mlandu chifukwa cha mawu aliwonse wopanda pake amene anayankhula. Pakuti ndi mawu anu mudzapezeka osalakwa ndiponso ndi mawu anu mudzapezeka olakwa.”

Chizindikiro cha Yona

Pamenepo ena mwa Afarisi ndi aphunzitsi amalamulo anati kwa Iye, “Aphunzitsi, tikufuna tione chizindikiro chodabwitsa kuchokera kwa Inu.”

Iye anayankha kuti, “Mʼbado woyipa ndi wachigololo ufunsa za chizindikiro chodabwitsa! Koma ndi chimodzi chomwe sichidzapatsidwa kwa inu kupatula chizindikiro cha mneneri Yona. Pakuti monga Yona anali mʼmimba mwa nsomba yayikulu masiku atatu, usana ndi usiku, momwemonso Mwana wa Munthu adzakhala masiku atatu, usana ndi usiku, mʼkati mwa nthaka. Anthu a ku Ninive adzayimirira pachiweruzo ndi mʼbado uwu ndi kuwutsutsa pakuti iwo analapa Yona atalalikira ndipo tsopano wamkulu kuposa Yona ali pano. Mfumu yayikazi yakummwera idzayimirira pa tsiku lachiweruzo ndi mʼbado uwu ndipo idzawutsutsa pakuti inachokera kumathero a dziko lapansi kudzamva nzeru za Solomoni, ndipo pano pali woposa Solomoni.

Za Mzimu Woyipa

“Pamene mzimu woyipa utuluka mwa munthu, umadutsa malo wopanda madzi kufunafuna malo opumulira ndipo suwapeza. Pamenepo umati, ‘Ndidzabwerera ku nyumba yanga komwe ndinatuluka.’ Pamene ufika, upeza mopanda kanthu, mosesedwa ndi mokonzedwa bwino. Kenaka umapita kukatenga mizimu ina isanu ndi iwiri yoyipa kwambiri kuposa uwowo ndipo imapita ndi kukakhala mʼmenemo. Choncho khalidwe lotsiriza la munthu uyu limakhala loyipa kwambiri kuposa loyambalo. Umo ndi mmene zidzakhalire ndi mʼbado oyipawu.”

Read More of Mateyu 12