Luka 16:1-18 CCL

Luka 16:1-18

Fanizo la Kapitawo Wosakhulupirika

Yesu anawuza ophunzira ake kuti, “Panali munthu wina wachuma amene kapitawo wake anzake anamuneneza kuti amawononga chuma chakecho. Choncho anamuyitana ndi kumufunsa kuti, ‘Kodi nʼchiyani chimene ndikumva za iwe? Pereka tsatanetsatane wa ntchito yako, pakuti supitirizanso kukhala kapitawo wanga.’

“Kapitawoyo analingalira kuti, ‘Kodi tsopano ndidzachita chiyani? Bwana wanga andichotsa ntchito. Ine ndilibe mphamvu zokwanira zolimira, komanso ine ndimachita manyazi kupempha. Ine ndikudziwa chimene ndidzachita kotero kuti, pamene ntchito yanga yatha pano, anthu adzandilandire mʼnyumba zawo.’

“Choncho iye anayitana aliyense amene anali ndi ngongole kwa bwana wake. Iye anafunsa woyamba, ‘Kodi uli ndi ngongole yotani kwa bwana wanga?’

“Iye anayankha kuti, ‘Migolo yamafuta a olivi 800.’

“Kapitawo uja anamuwuza iye, ‘Tenga pamene unalemba ngongole yakoyo, khala pansi msanga ndipo lemba kuti ndi migolo 400.’

“Kenaka iye anafunsa wachiwiri kuti, ‘Nanga iwe uli ndi ngongole yotani?’

“Iye ayankha kuti madengu a tirigu 1,000.

“Iye anati, ‘Tenga pamene unalemba ngongole yakoyo ndipo ulembepo 800.’

“Bwana anayamikira kapitawo wosakhulupirikayo popeza anachita mochenjera. Pakuti anthu a dziko lino lapansi ndi ochenjera kwambiri akamachita zinthu ndi anthu ofanana nawo kuposa anthu a kuwunika. Ine ndikukuwuzani inu, gwiritsani ntchito chuma cha dziko lapansi kuti mudzipezere nokha abwenzi, kuti pamene chatha mudzalandiridwe mʼmalo okhala amuyaya.

“Amene akhulupirika pa zinthu zochepa akhoza kukhulupirikanso pa zinthu zambiri, ndipo amene sakhulupirika pa zinthu zochepa adzakhala wosakhulupirika pa zinthu zambiri. Ndipo ngati simunakhale okhulupirika pogwiritsa ntchito chuma cha dziko lapansi, ndani amene adzakusungitsani chuma chenicheni? Ndipo ngati simunakhale okhulupirika ndi chuma cha mwini wake, ndani amene adzakupatsani katundu wanuwanu?

“Palibe wantchito amene angatumikire mabwana awiri. Mwina iye adzadana ndi wina ndi kukonda winayo, kapena adzakhala wodzipereka kwa wina ndi kumunyoza winayo. Inu simungathe kutumikira Mulungu komanso ndalama nthawi imodzi.”

Afarisi amene ankakonda ndalama atamva zimenezi anamuseka Yesu. Yesu anawawuza kuti, “Inu ndi amene mumadzilungamitsa nokha pamaso pa anthu, koma Mulungu amadziwa mitima yanu. Zinthu zimene anthu amaziyesa zopambana, ndi zonyansa pamaso pa Mulungu.

Ziphunzitso Zina

“Malamulo ndi Aneneri zinagwira ntchito mpaka nthawi ya Yohane. Kuyambira nthawi imeneyo, Uthenga Wabwino wa ufumu wa Mulungu ukulalikidwa, ndipo aliyense akuyesetsa mwamphamvu kuti alowemo. Nʼkwapafupi kuti kumwamba ndi dziko lapansi zichoke kulekana ndi kuti kalemba kakangʼono kachoke mʼMalamulo.

“Aliyense amene asiya mkazi wake ndi kukakwatira mkazi wina akuchita chigololo, ndipo mwamuna amene akwatira mkazi wosiyidwayo akuchitanso chigololo.”

Read More of Luka 16