Yeremiya 27:1-22, Yeremiya 28:1-17, Yeremiya 29:1-23 CCL

Yeremiya 27:1-22

Yuda Adzatumikira Nebukadinezara

Zedekiya mwana wa Yosiya, mfumu ya ku Yuda, atangoyamba kulamulira, Yehova anawuza Yeremiya kuti, “Tenga zingwe zomangira ndi mitengo ya goli ndipo uzimangirire mʼkhosi mwako. Tsono utumize uthenga kwa mafumu a Edomu, Mowabu, Amoni, Turo ndi Sidoni kudzera mwa amithenga amene abwera ku Yerusalemu kwa Zedekiya, mfumu ya Yuda. Uwapatse uthenga wokapereka kwa ambuye awo ndipo uwawuze kuti: Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti, ‘Mukawuze ambuye anu kuti: Ndi mphamvu zanga ndi dzanja langa lamphamvu ndinalenga dziko lapansi ndi anthu ake onse pamodzi ndi nyama zili mʼmenemo, ndipo ndimalipereka kwa aliyense amene ndikufuna. Tsopano ndidzapereka mayiko anu onse kwa mtumiki wanga Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni. Ndamupatsanso nyama zakuthengo zonse kuti zimutumikire. Anthu a mitundu yonse adzamutumikira iyeyo, mwana wake ndi chidzukulu chake mpaka nthawi itakwana yoti dziko lake liwonongedwe. Pamenepo mitundu yambiri ndi mafumu amphamvu adzamugonjetsa.

“ ‘Koma ngati anthu a mtundu wina uliwonse kapena ufumu wina uliwonse adzakana kutumikira Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni kapena kusenza goli lake, Ine ndidzalanga mtundu umenewo ndi lupanga, ndi njala ndi mliri, akutero Yehova, mpaka nditawapereka mʼmanja mwake kotheratu. Choncho musamvere aneneri anu, owombeza anu, otanthauza maloto anu, amawula anu kapena amatsenga anu akamakuwuzani kuti, ‘Simudzatumikira mfumu ya ku Babuloni.’ Iwo akukuloserani zabodza kotero kuti adani adzakuchotsani mʼdziko lanu nʼkupita nanu ku dziko lakutali. Ndidzakupirikitsani ndi kukuwonongani kotheratu. Koma ngati mtundu wina uliwonse udzagonjera mfumu ya ku Babuloni ndi kuyitumukira, ndidzawusiya kuti ukhale mʼdziko lake kuti uzilima ndi kukhalamo, akutero Yehova.’ ”

Uthenga womwewu ndinawuzanso Hezekiya mfumu ya Yuda. Ndinati, “Gonjerani mfumu ya ku Babuloni. Itumikireni iyoyo pamodzi ndi anthu ake ndipo mudzakhala ndi moyo. Nanga inu ndi anthu anu, muferenji ndi lupanga, ndi njala, ndi mliri, zimene Yehova waopsezera mtundu wina uliwonse umene sudzatumikira mfumu ya ku Babuloni? Musamvere mawu a aneneri akamakuwuzani kuti, ‘Simudzatumikira mfumu ya ku Babuloni,’ chifukwa zimene akukuloseranizo nʼzabodza. Sindinawatume ngakhale iwo akulosera mʼdzina langa. Nʼchifukwa chake, ndidzakupirikitsani ndipo mudzawonongeka kotheratu, inu pamodzi ndi aneneri amene akunenera zabodza kwa inu.”

Kenaka ndinawuza ansembe pamodzi ndi anthu ena onse kuti, “Yehova akuti: Musamvere aneneri amene akumanena kuti, ‘Posachedwapa ziwiya za mʼNyumba ya Yehova zibwera kuchokera ku Babuloni.’ Iwowo akunenera zabodza kwa inu. Musawamvere. Tumikirani mfumu ya ku Babuloni, ndipo mudzakhala ndi moyo. Mzindawu usandukirenji bwinja? Ngati iwo ndi aneneri ndipo ali ndi mawu a Yehova, apempheretu kwa Yehova Wamphamvuzonse kuti ziwiya zimene zatsala mʼNyumba ya Yehova ndi mʼnyumba ya mfumu ya Yuda ndiponso mu Yerusalemu zisatengedwe kupita ku Babuloni. Pakuti Yehova akunena za zipilala, za mbiya ya madzi, maphaka ndi ziwiya zina zimene zatsala mu Yerusalemu. Izi ndi zimene Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni sanatenge pamene anatenga ukapolo Yekoniya mwana wa Yehoyakimu mfumu ya Yuda kupita ku Babuloni kuchokera ku Yerusalemu, pamodzi ndi anthu olemekezeka a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu. Inde, Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, akunena za zinthu zimene zinatsala mʼNyumba ya Yehova ndi mʼnyumba ya mfumu ya Yuda ndi mu Yerusalemu kuti, ‘Zidzatengedwa kupita ku Babuloni ndipo zidzakhala kumeneko mpaka tsiku limene ndidzawakumbukirenso,’ akutero Yehova. ‘Pamenepo ndidzazitenganso ndi kuzibwezanso ku malo ano.’ ”

Read More of Yeremiya 27

Yeremiya 28:1-17

Hananiya Atsutsana ndi Yeremiya

Chaka chomwecho mwezi wachisanu wa chaka chachinayi, poyambirira pa ulamuliro wa Zedekiya mfumu ya Yuda, mneneri Hananiya mwana wa Azuri, amene amachokera ku Gibiyoni, anandiwuza ine mʼNyumba ya Yehova pamaso pa ansembe ndi anthu onse kuti, “Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, akuti, ‘Ndidzathyola goli la mfumu ya ku Babuloni. Pasanathe zaka ziwiri ndidzabweretsa pa malo ano ziwiya zonse za ku Nyumba ya Yehova zimene Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni anazichotsa pa malo pano ndi kupita nazo ku Babuloni. Ndidzabweretsanso pa malo pano Yekoniya mwana wa Yehoyakimu mfumu ya Yuda pamodzi ndi akapolo ena onse ochokera ku Yuda amene anapita ku Babuloni,’ akutero Yehova, ‘chifukwa ndidzathyola goli la mfumu ya ku Babuloni.’ ”

Pamenepo mneneri Yeremiya anayankha mneneri Hananiya pamaso pa ansembe ndi anthu onse amene anasonkhana mʼNyumba ya Yehova. Anati, “Ameni! Yehova achitedi zomwezo! Yehova akwaniritse mawu amene waloserawo. Iye abweretsenso pa malo pano ziwiya za mʼNyumba ya Yehova ndi akapolo onse kuchokera ku Babuloni. Komabe, tamvera zimene nditi ndikuwuze iweyo pamodzi ndi anthu onse: Kunali aneneri kalelo, ine ndi iwe tisanabadwe. Iwowa analosera za nkhondo, mavuto ndi mliri kuti zidzagwera mayiko ambiri ndi maufumu amphamvu. Koma mneneri amene amalosera zamtendere adzadziwika kuti ndi woona ndi kuti watumidwa ndi Yehova ngati zimene wanenera zachitikadi.”

Pamenepo mneneri Hananiya anachotsa goli mʼkhosi mwa mneneri Yeremiya nalithyola, ndipo anawuza anthu onse kuti, “Yehova akuti, ‘Umu ndi mmene ndidzathyolere goli la Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni mʼkhosi mwa anthu a mitundu yonse pasanathe zaka ziwiri.’ ” Zitatero, mneneri Yeremiya anachoka.

Patapita nthawi pangʼono, mneneri Hananiya atathyola goli mʼkhosi mwa mneneri Yeremiya, Yehova anawuza Yeremiya kuti, “Pita, kawuze mneneri Hananiya kuti, ‘Yehova akuti: Iwe wathyola goli lamtengo, mʼmalo mwake Ine ndidzayika goli lachitsulo. Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti: Ndidzayika goli lachitsulo mʼkhosi mwa anthu a mitundu yonseyi kuti atumikire Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni, ndipo iwo adzamutumikiradi. Ndipo ndamupatsanso ulamuliro ngakhale pa nyama zakuthengo.’ ”

Ndipo mneneri Yeremiya anawuza mneneri Hananiya kuti, “Tamvera, Hananiya! Iweyo Yehova sanakutume, koma iwe wanyenga anthuwa kuti akhulupirire zabodza. Nʼchifukwa chake Yehova akuti, ‘Ndatsala pangʼono kukuchotsa pa dziko lapansi. Iwe ufa chaka chino chisanathe, chifukwa wakhala ukulalikira zowukira Yehova.’ ”

Mʼmwezi wachisanu ndi chiwiri wa chaka chomwecho, mneneri Hananiya anamwaliradi.

Read More of Yeremiya 28

Yeremiya 29:1-23

Kalata Yolembera Anthu a ku Ukapolo

Yeremiya anatumiza kalata kuchokera ku Yerusalemu kupita kwa akuluakulu amene anali ku ukapolo, ndiponso kwa ansembe, aneneri pamodzi ndi anthu onse amene Nebukadinezara anawatenga ku Yerusalemu kupita nawo ku ukapolo ku Babuloni. Zimenezi zinachitika mfumu Yekoniya, amayi a mfumu, nduna za mfumu ndiponso atsogoleri a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu, anthu aluso ndi amisiri atatengedwa ku Yerusalemu kupita ku ukapolo. Yeremiya anapatsira kalatayo Eleasa mwana wa Safani ndi Gemariya mwana wa Hilikiya, amene Zedekiya mfumu ya Yuda anawatumiza kwa Mfumu Nebukadinezara ku Babuloni. Mʼkalatamo analembamo kuti:

Anthu onse amene anatengedwa ukapolo kuchokera ku Yerusalemu kupita ku Babuloni, Yehova akuwawuza kuti, “Mangani nyumba ndipo muzikhalamo. Limani minda ndipo mudye zipatso zake. Kwatirani ndipo mubereke ana aamuna ndi aakazi. Ana anu aamuna muwasankhire akazi ndipo muwasankhire amuna ana anu aakaziwo, kuti nawonso abale ana aamuna ndi aakazi. Muchulukane kumeneko. Chiwerengero chanu chisachepe. Ndiponso muzifunafuna mtendere ndi ubwino wa mzinda umene ndinakupirikitsirani ku ukapoloko. Muzipempherera mzindawo kwa Yehova, kuti zikuyendereni bwino.” Inde, Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akunena kuti, “Musalole kuti aneneri ndi owombeza amene ali pakati panu akunyengeni. Musamvere maloto awo. Iwo akunenera zabodza kwa inu mʼdzina langa ngakhale Ine sindinawatume,” akutero Yehova.

Yehova akuti, “Zaka 70 za ku Babuloni zikadzatha, ndidzabwera kudzakuchitirani zabwino zonse zimene ndinakulonjezani zija, ndipo ndidzakubwezerani ku malo ano. Pakuti Ine ndikudziwa zimene ndinakukonzerani,” akutero Yehova, “ndimalingalira zabwino zokhazokha za inu osati zoyipa, ayi. Ndimalingalira zinthu zokupatsani chiyembekezo chenicheni pa za mʼtsogolo. Nthawi imeneyo mudzandiyitana, ndi kunditama mopemba ndipo ndidzakumverani. Mudzandifunafuna ndipo mudzandipeza. Mukadzandifuna ndi mtima wanu wonse mudzandipezadi,” akutero Yehova, “ndipo ndidzakubwezerani zabwino zanu. Ndidzakusonkhanitsani kuchokera ku mayiko onse ndi kumalo konse kumene munali,” akutero Yehova, “ndipo ndidzakubweretsani kumalo kumene munali ndisanakuchotseni kukupititsani ku ukapolo.”

Inu mumati, “Yehova watiwutsira aneneri athu ku Babuloni,” koma zimene Yehova akunena za mfumu imene ikukhala pa mpando waufumu wa Davide pamodzi ndi anthu onse amene anatsala mu mzinda muno, abale anu amene sanapite nanu ku ukapolo ndi izi, Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Ndidzawapha ndi nkhondo, njala ndi mliri ndipo ndidzawasandutsa ngati nkhuyu zowola kwambiri, zosati nʼkudya. Ndidzawalondola ndi lupanga, njala ndi mliri ndipo ndidzawasandutsa chinthu chonyansa kwa anthu amayiko onse a pa dziko lapansi. Adzakhala otembereredwa, ochititsa mantha, onyozeka ndiponso ochitidwa chipongwe pakati pa anthu a mitundu yonse kumene ndawapirikitsirako. Zidzatero chifukwa sanamvere mawu anga amene ndinkawatumizira kudzera mwa atumiki anga, aneneri. Ngakhale inu amene muli ku ukapolo simunamverenso,” akutero Yehova.

Choncho, imvani mawu a Yehova, inu akapolo nonse amene ndinakuchotsani mu Yerusalemu ndi kukupititsani ku Babuloni. Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti zokhudza Ahabu mwana wa Kolaya ndi Zedekiya mwana wa Maseya, amene akulosera zabodza kwa inu mʼdzina langa: “Taonani ndidzawapereka kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni, ndipo adzawapha inu mukupenya. Chifukwa cha anthu awiriwo, akapolo onse ochokera ku Yuda amene ali ku Babuloni adzagwiritsa ntchito mawu awa potemberera: ‘Yehova achite nawe monga mmene anachitira ndi Zedekiya ndi Ahabu, amene mfumu ya ku Babuloni inawatentha.’ Pakuti anthu amenewa achita zoyipa kwambiri mu Israeli; achita chigololo ndi akazi a eni ake ndipo mʼdzina langa ankayankhula zabodza zimene sindinawawuze kuti atero. Ine ndikuzidziwa ndipo ndine mboni ya zimenezi,” akutero Yehova.

Read More of Yeremiya 29