Genesis 2:18-25, Genesis 3:1-24, Genesis 4:1-16 CCL

Genesis 2:18-25

Ndipo Yehova Mulungu anati, “Sibwino kuti munthu akhale yekha. Ndidzamupangira mnzake womuthandiza.”

Kenaka Yehova Mulungu anawumba ndi dothi nyama zonse zakuthengo ndi mbalame zonse zamlengalenga. Ndipo Iye anapita nazo kwa munthu uja kuti akazipatse mayina; ndipo dzina lililonse limene Adamu anapereka ku chamoyo chilichonse, lomwelo linakhala dzina lake. Choncho Adamu anazitcha mayina ziweto zonse, mbalame zamlengalenga ndi nyama zakuthengo zonse.

Komabe munthu uja analibe mnzake womuthandiza. Tsono Yehova Mulungu anamugonetsa munthu uja tulo tofa nato; ali mtulo chomwecho, Mulungu anachotsa imodzi mwa nthiti zake ndi kutseka pamalopo ndi mnofu. Motero Yehova Mulungu anapanga mkazi ndi nthiti ija imene anatenga kwa munthu uja nabwera naye kwa iye.

Munthu uja anati,

“Uyu ndiye fupa lochokera ku mafupa anga

ndi mnofu wochokera ku mnofu wanga;

adzatchedwa ‘mkazi,’

popeza wachokera mwa mwamuna.”

Nʼchifukwa chake, mwamuna amasiya abambo ndi amayi ake nakaphatikana ndi mkazi wake ndipo awiriwo amakhala thupi limodzi.

Munthu uja ndi mkazi wakeyo, onse awiri anali maliseche ndipo analibe manyazi.

Read More of Genesis 2

Genesis 3:1-24

Kuchimwa kwa Munthu

Ndipo njoka inali yochenjera kuposa nyama yakuthengo iliyonse imene Yehova Mulungu anapanga. Njokayo inati kwa mkaziyo, “Kodi Mulungu ananenadi kuti, ‘Inu musadye zipatso za mtengo uliwonse mʼmundamu?’ ”

Mkaziyo anati kwa njokayo, “Tikhoza kudya zipatso za mʼmitengo ya mʼmundawu, koma Mulungu anati, ‘Musadye zipatso za mu mtengo umene uli pakati pa munda, ndipo musadzawukhudze kuti mungadzafe.’ ”

“Ndithudi simudzafa,” inatero njokayo kwa mkaziyo. “Pakuti Mulungu akudziwa kuti tsiku limene mudzadye zipatso za mu mtengowo, maso anu adzatsekuka, ndipo mudzakhala ngati Mulungu, wodziwa zabwino ndi zoyipa.”

Pamene mkaziyo anaona kuti mtengowo unali wabwino kudya ndi wokongola ndi kuti unali wopatsa nzeru, anatengako zipatso zake nadya. Zina anamupatsako mwamuna wake amene anali naye pomwepo ndipo naye anadyanso. Kenaka maso awo anatsekuka, ndipo anazindikira kuti anali maliseche. Choncho anasoka masamba a mkuyu nadzipangira zovala.

Kenaka munthu uja ndi mkazi wake anamva mtswatswa wa Yehova Mulungu akuyendayenda mʼmundamo madzulo a tsikulo, ndipo iwo anabisala pamaso pa Yehova Mulungu pakati pa mitengo ya mʼmundamo. Yehova Mulungu anayitana munthu uja kuti, “Uli kuti?”

Iye anayankha, “Ndinakumvani mʼmundamo, ndipo ndimaopa chifukwa ndinali maliseche; choncho ndinabisala.”

Ndipo anamufunsa, “Ndani anakuwuza kuti uli maliseche? Kodi wadya zipatso za mtengo umene ndinakulamulira kuti usadye?”

Koma munthu uja anati, “Mkazi amene munandipatsa kuti ndizikhala nayeyu anandipatsako chipatso cha mtengowo ndipo ndinadya.”

Tsono Yehova Mulungu anati kwa mkaziyo, “Wachitachi nʼchiyani?”

Mkaziyo anati, “Njoka inandinamiza, ndipo ndinadya.”

Choncho Yehova Mulungu anati kwa njokayo, “Popeza wachita zimenezi,

“Ndiwe wotembereredwa kuposa ziweto zonse

ndi nyama zakuthengo zonse.

Udzayenda chafufumimba

ndipo udzadya fumbi

masiku onse a moyo wako.

Ndipo ndidzayika chidani

pakati pa iwe ndi mkaziyo,

pakati pa mbewu yako ndi mbewu yake;

Iye adzaphwanya mutu wako

ndipo iwe udzaluma chidendene chake.”

Kwa mkaziyo Iye anati,

“Ndidzachulukitsa ululu wako kwambiri pamene uli ndi pakati;

ndipo udzamva ululu pa nthawi yako yobereka ana.

Udzakhumba mwamuna wako,

ndipo adzakulamulira.”

Ndipo kwa Adamu Mulungu anati, “Chifukwa wamvera mkazi wako ndipo wadya zipatso za mu mtengo umene ndinakulamulira kuti, ‘Usadye.’

“Nthaka yatembereredwa chifukwa cha iwe,

movutikira udzadya zochokera mʼnthakamo

masiku onse a moyo wako.

Mʼnthakamo mudzamera minga ndi nthula

ndipo udzadya zomera zakuthengo.

Kuti upeze chakudya udzayenera

kukhetsa thukuta,

mpaka utabwerera ku nthaka

pakuti unachokera kumeneko;

pakuti ndiwe fumbi

ku fumbi komweko udzabwerera.”

Munthu uja anatcha mkazi wake Hava, chifukwa iyeyu adzakhala mayi wa anthu onse amoyo.

Yehova Mulungu anapangira Adamu ndi mkazi wake zovala zachikopa ndipo anawaveka. Ndipo Yehova Mulungu anati, “Tsopano munthu uyu wasanduka mmodzi wa ife, wodziwa zabwino ndi zoyipa. Iyeyu asaloledwe kutambasula dzanja ndi kutengako zipatso za mu mtengo wopatsa moyo uja kuti angakhale ndi moyo mpaka muyaya.” Kotero Yehova Mulungu anatulutsa Adamu Mʼmunda wa Edeni kuti azilima mʼnthaka imene anachokera. Atamuthamangitsa munthu uja, Yehova anayika Akerubi mbali ya kummawa kwa Munda wa Edeni ndi lupanga lamoto limene limayendayenda ponsepo, kuteteza njira ya ku mtengo wopatsa moyo.

Read More of Genesis 3

Genesis 4:1-16

Kaini ndi Abele

Adamu anagona malo amodzi ndi Hava mkazi wake ndipo mkaziyo anakhala woyembekezera nabala Kaini, ndipo anati, “Ndi thandizo la Yehova ndapeza mwana wamwamuna.” Kenaka anabereka mʼbale wake Abele.

Abele anali woweta nkhosa ndipo Kaini anali mlimi. Patapita nthawi, Kaini anatenga zipatso za ku munda nakazipereka kwa Yehova monga nsembe. Nayenso Abele anatenga ana ankhosa oyamba kubadwa pamodzi ndi mafuta ake nakazipereka ngati nsembe kwa Yehova. Yehova anakondwera ndi Abele ndi nsembe yake. Koma sanakondwere ndi Kaini ndi nsembe yake. Kotero Kaini anakwiya kwambiri ndipo nkhope yake inagwa.

Choncho Yehova anati kwa Kaini, “Chifukwa chiyani wakwiya ndipo bwanji nkhope yako yagwa? Ukanachita zabwino sindikanakulandira kodi? Koma tsopano wachita zoyipa ndipo tchimo likukudikira pa khomo pako, likufuna kukugwira; koma iwe uyenera kugonjetsa tchimolo.”

Tsiku lina Kaini anati kwa mʼbale wake Abele, “Tiye tipite ku munda.” Ndipo ali ku mundako, Kaini anawukira mʼbale wake namupha.

Ndipo Yehova anamufunsa Kaini kuti, “Ali kuti mʼbale wako Abele?”

Iye anayankha kuti, “Sindikudziwa. Kodi ine ndine wosunga mʼbale wanga?”

Yehova anati, “Kodi wachita chiyani? Tamvera! Magazi a mʼbale wako akulirira kwa Ine kuchokera mʼnthaka. Ndipo tsopano ndiwe wotembereredwa ndipo wachotsedwa mʼdziko limene nthaka yake inatsekula pakamwa pake kulandira magazi a mʼbale wako amene unakhetsa. Udzalima munda koma nthakayo sidzakupatsanso zokolola zake. Udzakhala wosakhazikika; womangoyendayenda pa dziko lapansi.”

Kaini anati kwa Yehova, “Chilango changa ndi chachikulu kuposera mphamvu zanga. Lero mukundipirikitsa pa dziko ndi pamaso panu; ndidzakhala wosakhazikika, woyendayenda, ndipo aliyense amene adzandipeze adzandipha.”

Koma Yehova anamuwuza kuti, “Sizidzatero ayi; aliyense amene adzaphe Kaini adzalangidwa ndi kulipiritsidwa kasanu ndi kawiri.” Pamenepo Yehova anayika chizindikiro pa Kaini kuti aliyense womupeza asamuphe. Ndipo Kaini anachoka pamaso pa Yehova nakakhala ku dziko la Nodi, kummawa kwa Edeni.

Read More of Genesis 4