Genesis 11:10-32, Genesis 12:1-20, Genesis 13:1-18 CCL

Genesis 11:10-32

Mibado Kuyambira pa Semu Mpaka Abramu

Nayi mibado yochokera kwa Semu.

Patapita zaka ziwiri chitatha chigumula, Semu ali ndi zaka 100, anabereka Aripakisadi. Atabereka Aripakisadi, Semu anakhala ndi moyo zaka 500 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.

Pamene Aripakisadi anali ndi zaka 35, anabereka Sela. Atabereka Sela, Aripakisadi anakhala ndi moyo zaka zina 403 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.

Pamene Sela anali ndi zaka makumi atatu, anabereka Eberi. Atabereka Eberi, Sela anakhala ndi moyo zaka zina 403 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.

Pamene Eberi anali ndi zaka 34 anabereka Pelegi. Atabereka Pelegi, Eberi anakhala ndi moyo zaka zina 430 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.

Pamene Pelegi anali ndi zaka makumi atatu, anabereka Reu. Atabereka Reu, Pelegi anakhala zaka zina 209 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.

Pamene Reu anali ndi zaka 32, anabereka Serugi. Atabereka Serugi, Reu anakhala ndi moyo zaka zina 207 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.

Pamene Serugi anali ndi zaka makumi atatu, anabereka Nahori. Atabereka Nahori, Serugi anakhala ndi moyo zaka zina 200 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.

Pamene Nahori anali ndi zaka 29, anabereka Tera. Atabereka Tera, Nahori anakhala ndi moyo zaka zina 119 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.

Pamene Tera anali ndi zaka 70, anabereka Abramu, Nahori ndi Harani.

Mibado Yochokera mwa Tera

Nayi mibado yochokera mwa Tera.

Tera anabereka Abramu, Nahori ndi Harani. Ndipo Harani anabereka Loti. Abambo ake a Tera akanali ndi moyo, Harani anamwalira ku Uri wa ku Akaldeya kumene anabadwira. Abramu ndi Nahori onse anakwatira. Dzina la mkazi wa Abramu linali Sarai, ndipo la mkazi wa Nahori linali Milika. Iyeyu ndi Isika abambo awo anali Harani. Sarai analibe ana chifukwa anali wosabereka.

Tera anatenga mwana wake Abramu, mdzukulu wake Loti, ndi mpongozi wake Sarai, mkazi wa Abramu natuluka mzinda wa Uri wa ku Akaldeya kupita ku Kanaani. Pamene anafika ku Harani, anakhazikika kumeneko.

Tera anamwalira ku Harani ali ndi zaka 205.

Read More of Genesis 11

Genesis 12:1-20

Mulungu Ayitana Abramu

Tsiku lina Yehova anamuwuza Abramu kuti, “Tuluka mʼdziko lako. Siya abale ako ndi banja la abambo ako ndipo pita ku dziko limene ndidzakusonyeza.

“Ndidzakusandutsa kholo la mtundu waukulu wa anthu

ndipo ndidzakudalitsa;

ndi kukusandutsa wotchuka kotero kuti

udzakhala dalitso kwa anthu ambiri.

Ndidzadalitsa amene adzadalitsa iwe,

ndi kutemberera amene adzatemberera iwe;

ndipo mafuko onse a pa dziko lapansi

adzadalitsika kudzera mwa iwe.”

Choncho Abramu ananyamuka monga momwe Yehova anamuwuzira, napita pamodzi ndi Loti. Pamene Abramu amachoka ku Harani nʼkuti ali ndi zaka 75. Abramu anatenga mkazi wake Sarai, Loti, mwana wamngʼono wake, pamodzi ndi chuma chawo chimene anapeza ndi antchito amene anali nawo ku Harani. Iwo ananyamuka ulendo mpaka kukafika ku dziko la Kanaani.

Abramu anadutsa mʼdzikomo mpaka kukafika ku Sekemu pa mtengo wa thundu wa ku More. Nthawi imeneyo Akanaani analipobe mʼdzikomo. Yehova anadza kwa Abramu nati, “Kwa zidzukulu zako ndidzapereka dziko limeneli.” Choncho Abramu anamangira Yehova amene anadza kwa iye, guwa lansembe.

Atachoka pamenepo analowera cha ku mapiri a kummawa kwa Beteli namangako tenti yake pakati pa Beteli chakumadzulo ndi Ai chakummawa. Kumeneko anamangira Yehova guwa lansembe napemphera mʼdzina la Yehovayo. Kenaka Abramu ananyamuka kumalowera cha ku Negevi.

Abramu ku Igupto

Kunagwa njala yayikulu mʼdzikomo, ndipo Abramu anapita ku Igupto kukakhala ngati mlendo kwa kanthawi kochepa popeza njalayo inakula kwambiri. Atatsala pangʼono kulowa mu Igupto, Abramu anamuwuza mkazi wake Sarai kuti, “Ndimadziwa kuti ndiwe mkazi wokongola kwambiri. Tsono Aigupto akakuona adzanena kuti ‘Ameneyu ndi mkazi wake.’ Tsono adzandipha ine nakusiya iwe ndi moyo. Tsono udzikawawuza kuti iwe ndiwe mlongo wanga. Ukatero zidzandiyendera bwino ndipo ndidzapulumuka chifukwa cha iwe.”

Pamene Abramu anafika ku Igupto, Aigupto aja anaona kuti Sarai anali mkazi wokongoladi. Pamene akuluakulu a ku nyumba ya Farao anamuona, anakamuyamikira pamaso pa Farao ndipo ananka naye ku nyumba ya Farao. Abramu naye zinthu zinkamuyendera bwino chifukwa cha Sarai. Farao anamupatsa nkhosa, ngʼombe, abulu aamuna ndi abulu aakazi, antchito aakazi pamodzi ndi ngamira.

Koma Yehova anabweretsa matenda owopsa pa Farao pamodzi ndi banja lake lonse chifukwa cha Sarai mkazi wa Abramu. Choncho Farao anayitanitsa Abramu namufunsa kuti, “Nʼchiyani wandichitirachi? Nʼchifukwa chiyani sunandiwuze kuti ameneyu ndi mkazi wako? Nʼchifukwa chiyani unati ndi mlongo wako, mpaka ine ndinamutenga kukhala mkazi wanga? Eko mkazi wako. Mutenge uzipita!” Farao analamula asilikali ake ndipo iwo anamutulutsa Abramu pamodzi ndi mkazi wake ndi zonse anali nazo.

Read More of Genesis 12

Genesis 13:1-18

Abramu Asiyana ndi Loti

Choncho Abramu pamodzi ndi mkazi wake ndi zonse anali nazo, anachoka ku Igupto kupita ku Negevi. Loti naye anapita nawo. Abramu anali wolemera kwambiri; anali ndi ziweto ndiponso siliva ndi golide.

Atachoka ku Negevi, anayenda malo osiyanasiyana mpaka anafika ku Beteli, ku malo a pakati pa Beteli ndi Ai, kuja kumene anamanga tenti poyamba, ndiponso kumene Abramu anamangira Yehova guwa lansembe kwa nthawi yoyamba ndi kupemphera mʼdzina la Yehova.

Loti amene ankayendayenda ndi Abramu nayenso anali ndi ziweto zosiyanasiyana ndi matenti. Motero dziko linayamba kuwachepera kuti onse nʼkukhala pamodzi, popeza katundu wawo anali wochuluka kwambiri moti sakanatha kukhala pamodzi. Mikangano inayambika pakati pa abusa a Abramu ndi abusa a Loti. Nthawi imeneyo nʼkuti Akanaani ndi Aperezi akukhalanso mʼdziko lomwelo.

Tsono Abramu anati kwa Loti, “Pasakhale mikangano pakati pa iwe ndi ine kapena pakati pa abusa ako ndi anga, popeza ndife abale. Kodi dziko lonseli silili pamaso pako? Tiye tisiyane. Iwe ukalowera kumanzere, ine ndilowera kumanja; ukalowera kumanja, ine ndipita kumanzere.”

Loti atamwazamwaza maso anaona kuti chigwa chonse cha mtsinje wa Yorodani chinali chothiriridwa bwino ngati munda wa Yehova, kapena ngati dziko la ku Igupto mpaka ku Zowari. (Nthawi iyi nʼkuti Yehova asanawononge Sodomu ndi Gomora). Choncho Loti anadzisankhira yekha chigwa chonse cha Yorodani nanyamuka kulowera cha kummawa. Choncho anthu awiriwa anasiyana. Abramu anakhala mʼdziko la Kanaani, pamene Loti anakakhala pakati pa mizinda ikuluikulu ya mʼchigwamo. Anamanga tenti yake pafupi ndi Sodomu. Tsono anthu a ku Sodomu anali oyipa ndiponso ankachimwira Yehova kwambiri.

Loti atachoka, Yehova anati kwa Abramu, “Kuchokera pamene ulipo tayangʼanayangʼana cha kumpoto, kummwera, kummawa ndi kumadzulo. Dziko lonse ukulionalo ndidzalipereka kwa iwe ndi zidzukulu zako mpaka muyaya. Ndidzakupatsa zidzukulu zochuluka ngati fumbi lapansi moti amene angathe kuwerenga fumbilo ndiye kuti angathenso kuwerenga zidzukulu zako. Dzuka ndipo uyendere dziko lonseli mulitali ndi mulifupi pakuti ndalipereka kwa iwe.”

Choncho Abramu anasamutsa tenti yake napita kukakhala pafupi ndi mitengo ikuluikulu ija ya thundu ya ku Mamre ku Hebroni, kumene anamangira Yehova guwa lansembe.

Read More of Genesis 13