Ezekieli 38:1-23, Ezekieli 39:1-29 CCL

Ezekieli 38:1-23

Za Chilango cha Gogi

Yehova anandiyankhula kuti: “Iwe mwana wa munthu, tembenukira kwa Gogi, wa ku dziko la Magogi, amene ali kalonga wamkulu wa mzinda wa Mesaki ndi Tubala. Umuyimbe mlandu. Umuwuze mawu a Ine Ambuye Yehova akuti, ‘Ine ndikudana nawe, iwe Gogi, kalonga wamkulu wa ku Mesaki ndi Tubala. Ndidzakuzunguza, ndidzakukola ndi mbedza mʼkamwa mwako. Ndidzakutulutsa iweyo pamodzi ndi gulu lako lonse la nkhondo, akavalo ako ndi okwerapo ake. Onse adzakhala atanyamula zida za nkhondo, zishango ndi malihawo ndipo malupanga awo adzakhala osolola. Pamodzi ndi iwowo, padzakhalanso ankhondo a ku Perisiya, ku Kusi, ndi ku Puti. Onsewa adzakhala atanyamula zishango ndi kuvala zipewa zankhondo. Padzakhalanso Gomeri pamodzi ndi ankhondo ake onse ndiponso banja la Togarima ndi gulu lake lonse lankhondo lochokera kutali kumpoto. Padzakhaladi mitundu yambiri ya anthu pamodzi ndi iwe.

“ ‘Konzekani! Mukhaledi okonzeka, iweyo pamodzi ndi gulu lonse la nkhondo limene lakusonkhanira. Iweyo udzawatsogolera pokamenya nkhondo. Pakapita masiku ambiri ndidzakuyitana. Zaka zikubwerazi ndidzakulowetsa mʼdziko limene lapulumuka ku nkhondo. Anthu ake anasonkhanitsidwa kuchokera ku mitundu ya anthu ambiri nʼkukakhazikika pa mapiri a Israeli amene kwa nthawi yayitali anali ngati chipululu. Anthu onsewa tsopano akukhala mwa mtendere. Tsono iwe pamodzi ndi ankhondo ako onse ndiponso mitundu yambiri ya anthu imene ili nawe mudzabwera ngati mphepo yamkuntho. Mudzaphimba dziko lonse ngati mitambo.

“Ine Ambuye Yehova ndikuti: Pa tsiku limenelo mu mtima mwako mudzabwera maganizo ofuna kukonzekera kuchita zoyipa. Iwe udzanena kuti, ‘Ndikukathira nkhondo dziko la midzi yopanda mipanda; ndikathira nkhondo anthu okhala mwamtendere, anthu amene satchinjirizidwa ndi mipanda, zipata kapena mipiringidzo. Ndipita kukalanda chuma chawo ndi kukafunkha zinthu zawo. Ndidzalimbana ndi midzi imene kale inali mabwinja. Ndikathira nkhondo anthu amene anasonkhanitsidwa kuchokera kwa anthu a mitundu ina. Iwowa ali ndi ziweto zambiri, katundu wochuluka ndiponso amakhala pakatikati pa dziko lapansi.’ Anthu a ku Seba, a ku Dedani ndiponso amalonda a ku Tarisisi pamodzi ndi midzi yake yonse adzakufunsa kuti, ‘Kodi wabwera kudzafunkha? Kodi wasonkhanitsa gulu lako la nkhondo kudzalanda chuma, kudzatenga siliva ndi golide, ziweto ndi katundu kuti zikhale zofunkha zochuluka?’ ”

“Nʼchifukwa chake, iwe mwana wa munthu, nenera ndipo uwuze Gogi kuti, ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Pa nthawi imene anthu anga adzakhala pa mtendere, iwe udzanyamuka. Udzabwera kuchokera ku dziko lako kutali kumpoto, iwe pamodzi ndi mitundu yambiri ya anthu imene ili nawe, onse okwera akavalo, gulu lankhondo lalikulu ndi lamphamvu. Udzabwera kudzalimbana ndi anthu anga Aisraeli ngati mtambo wophimba dziko. Masiku amenewo, iwe Gogi, ndidzabwera nawe kuti ulimbane ndi dziko langa, kuti anthu a mitundu ina andidziwe Ine, pamene ndidzaonetsa kuyera kwanga pa zimene ndidzakuchite iweyo.

“ ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Kodi iwe si amene ndinayankhula za iwe masiku amakedzana kudzera mwa atumiki anga aneneri a Israeli? Pa zaka zambiri iwo ankalengeza kuti ndidzawutsa iwe kuti udzalimbane ndi Israeli. Zimene chidzachitika pa tsiku limenelo ndi izi: Gogi akadzathira nkhondo dziko la Israeli, mkwiyo wanga woopsa udzayaka. Ndikutero Ine Ambuye Wamphamvuzonse. Chifukwa cha mkwiyo ndi ukali wanga woyakawo Ine ndikunenetsa kuti pa nthawi imeneyo padzakhala chivomerezi chachikulu mʼdziko la Israeli. Nsomba za mʼnyanja, mbalame zamumlengalenga, zirombo zakuthengo, cholengedwa chilichonse chimene chimakwawa pansi, ndiponso anthu onse okhala pa dziko lapansi, adzanjenjemera pamaso panga. Mapiri adzangʼambika, malo okwera kwambiri adzagumuka ndipo khoma lililonse lidzagwa pansi. Ndidzawutsira Gogi nkhondo kuchokera ku mapiri anga. Ndikutero Ine Ambuye Yehova. Anthu a Gogiyo adzaphana okhaokha ndi malupanga. Ine ndidzamulanga ndi mliri ndi imfa. Ndidzagwetsa mvula yoopsa ya matalala, ndiponso sulufule ndi miyala ya moto pa iye ndi pa asilikali ake ndiponso pa mitundu yambiri ya anthu imene ili naye. Motero ndidzadzionetsa kuti ndine wamphamvu ndi woyera. Ndiponso ndidzadziwika pamaso pa anthu a mitundu ina yambiri. Momwemo adzadziwadi kuti Ine ndine Yehova.’ ”

Read More of Ezekieli 38

Ezekieli 39:1-29

“Iwe mwana wa munthu, nenera modzudzula Gogi ndi kumuwuza kuti Ine Ambuye Yehova ndikuti: ‘Ine ndikudana nawe, iwe Gogi, kalonga wamkulu wa Mesaki ndi Tubala. Ine ndidzakuzunguza ndi kukupirikitsira kutsogolo. Ndidzakutenga kuchokera kutali kumpoto ndi kukutumiza kuti ukalimbane ndi anthu a ku mapiri a Israeli. Kenaka Ine ndidzathyola uta wa mʼdzanja lako lamanzere ndipo ndidzagwetsa mivi ya mʼdzanja lako lamanja. Udzagwa ku mapiri a ku Israeli, iwe ndi magulu ako onse ankhondo ndiponso mitundu ya anthu imene ili nawe. Ndidzakusandutsa chakudya cha mitundu yonse ya mbalame zodya nyama, ndiponso cha zirombo zakuthengo. Udzafera pa mtetete kuthengo, pakuti Ine ndayankhula. Ndikutero Ine Ambuye Yehova. Ndidzatumiza moto pa Magogi ndi pa onse amene amakhala mwamtendere mʼmbali mwa nyanja. Choncho adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.’

“Ndidzachititsa kuti dzina langa loyera lidziwike pakati pa anthu anga Israeli. Sindidzalola kuti dzina langa liyipitsidwenso, ndipo mitundu ya anthu idzadziwa kuti Ine Yehova ndine Woyera mu Israeli. Zikubwera! Ndipo zidzachitikadi, ndikutero Ine Ambuye Yehova. Ndiye tsiku limene ndinanena lija.

“Pamenepo okhala mʼmizinda ya Israeli adzatuluka ndipo adzasonkhanitsa zida zankhondo kuti zikhale nkhuni ndipo adzazitentha; zishango ndi lihawo, mauta ndi mivi, zibonga za nkhondo ndi mikondo. Adzazisonkhera moto kwa zaka zisanu ndi ziwiri. Iwo sadzatolera nkhuni kuthengo kapena kukadula ku nkhalango, chifukwa adzasonkhera moto zidazo. Ndipo iwo adzafunkha amene anawafunkhawo, ndi kulanda chuma cha amene anawalanda, ndikutero Ine Ambuye Yehova.

“Pa tsiku limenelo ndidzamupatsa Gogi manda mu Israeli, mʼchigwa cha apaulendo, kummawa kwa Nyanja Yakufa. Mandawo adzatseka njira ya apaulendo, chifukwa Gogi ndi gulu lake lankhondo adzayikidwa kumeneko. Ndipo chigwacho chidzatchedwa chigwa cha gulu lankhondo la Gogi.

“Nyumba ya Israeli idzakhala ikukwirira mitembo kwa miyezi isanu ndi iwiri ndi cholinga choyeretsa dziko. Anthu onse a mʼdzikomo adzakwirira nawo mitembo. Ntchito imeneyo adzatchuka nayo pa tsiku limene ndidzaonetsa ulemerero wanga. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.

“Patapita miyezi isanu ndi iwiri adzalemba ntchito anthu ena odzayenda mʼdziko lonse kufunafuna mitembo imene inatsalira nʼkumayikwirira. Choncho adzayeretseratu dzikolo. Poyenda mʼdzikomo azidzati akaona fupa la munthu azidzayikapo chizindikiro pambali pake mpaka okumba manda atakalikwirira fupalo ku chigwa cha gulu lankhondo la Gogi. (Komwekonso kudzakhala mzinda wotchedwa Gulu la nkhondo). Ndipo potero adzayeretsa dziko.

“Tsono iwe mwana wa munthu, Ine Ambuye Yehova ndikuti: Itana mbalame za mitundu yonse ndi zirombo zonse zakuthengo ndipo uziwuze kuti, ‘Sonkhanani ndipo bwerani kuchokera ku mbali zonse ku nsembe imene ndikukonzerani inu, nsembe yayikulu pa mapiri a Israeli. Kumeneko inu mudzadya mnofu ndi kumwa magazi. Mudzadya mnofu wa anthu ankhondo amphamvu ndi kumwa magazi a akalonga a dziko lapansi. Onsewo anaphedwa ngati nkhosa zazimuna, ana ankhosa onenepa, mbuzi ndiponso ngati ngʼombe zazimuna zonenepa za ku Basani. Ku phwando lansembe limene ndikukonzera inulo, mudzadya zonona mpaka kukhuta ndi kumwa magazi mpaka kuledzera. Pa tebulo langa mudzakhuta pakudya akavalo ndi okwerapo ake, anthu amphamvu ndi asilikali amitundumitundu,’ ndikutero Ine Ambuye Yehova.

“Ine ndidzaonetsa ulemerero wanga pakati pa anthu a mitundu ina, ndipo adzaona mmene ndidzawalangire ndikadzayika dzanja langa pa iwo. Kuyambira tsiku limenelo mpaka mʼtsogolo Aisraeli adzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wawo. Ndipo anthu a mitundu ina adzadziwa kuti anthu a Israeli anatengedwa ukapolo chifukwa cha tchimo lawo, chifukwa anali osakhulupirika kwa Ine. Choncho Ine ndinawabisira nkhope yanga ndi kuwapereka kwa adani awo. Motero anaphedwa pa nkhondo. Ndinawachita zimenezi chifukwa cha kunyansa kwawo ndi zolakwa zawo, ndipo ndinawabisira nkhope yanga.

“Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: Tsopano ndidzakhazikanso pa bwino banja la Yakobo. Ndidzachitira chifundo Aisraeli onse, ndipo ndidzateteza dzina langa loyera. Anthuwo akadzakhala mwamtendere mʼdziko lawo popanda wina wowaopseza, pamenepo adzayiwala zamanyazi zawo zimene zinawachitikira chifukwa chosandikhulupirira Ine. Ndidzawabwezeranso kwawo kuchokera pakati pa anthu a mitundu ina ndipo ndidzawasonkhanitsa kuchokera ku mayiko a adani awo. Poteropo ndidzaonetsa pamaso pa anthu a mitundu yambiri kuti ndine Woyera. Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wawo, ngakhale kuti ndinawapereka ku ukapolo pakati pa anthu a mitundu ina. Ine ndidzawasonkhanitsanso ku dziko lawo osasiyako wina mʼmbuyo. Ine sindidzawabisiranso nkhope yanga, pakuti ndidzathira Mzimu wanga pa Aisraeli. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.”

Read More of Ezekieli 39