Ezekieli 13:1-23, Ezekieli 14:1-23, Ezekieli 15:1-8 CCL

Ezekieli 13:1-23

Mawu Odzudzula Aneneri Onyenga

Yehova anayankhulanso nane kuti, “Iwe mwana wa munthu unenere modzudzula aneneri a Israeli amene akunenera za kukhosi kwawo. Uwawuze iwowa kuti, ‘Imvani mawu a Yehova!’ Ambuye Yehova akuti, ‘Tsoka kwa aneneri opusa amene amangonenera zopeka ngakhale kuti sanaone kanthu konse!’ Iwe Israeli, aneneri ako ali ngati nkhandwe pa mabwinja. Simunakwere khoma kuti mukakonze mʼmene munagumuka, kuti Aisraeli adziteteze kolimba pa nkhondo pa tsiku la Yehova. Masomphenya awo ndi achabe ndipo kuwombeza kwawo ndi kwabodza. Iwo amati, ‘Yehova akutero,’ pomwe Yehova sanawatume. Komabe iwo amayembekezera kuti zimene ayankhulazo zichitikadi. Koma Ine ndikuti masomphenya anu ngachabechabe ndi zimene mwawombedzazo nʼzabodza. Mumanena kuti, ‘Akutero Yehova,’ pamene sindinayankhule nʼkomwe.

“Tsono Ine Ambuye Wamphamvuzonse ndikukutsutsani chifukwa cha zoyankhula zanu zonama ndi masomphenya anu abodzawo. Ndikutero Ine Yehova. Ndidzalanga aneneri amene amanenera zabodza za zinthu zimene amati anaziona mʼmasomphenya. Sadzakhala nawo mʼbwalo la anthu anga ndipo mayina awo sadzalembedwa mu kawundula wa nzika za Israeli. Sadzalowa nawo mʼdziko la Israeli. Pamenepo mudzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova.

“Popeza kuti aneneri asocheretsa anthu anga pomanena kuti, ‘Kuli mtendere’ pamene mtendere palibe; ndiponso anthu akamanga khoma iwo nʼkumalipaka njereza, choncho ufotokozere amene alipaka njerezawo kuti khomalo lidzagwa. Mvula idzagwa mwamphamvu, kudzagwa matalala akuluakulu, ndipo kudzawomba mphepo yamkuntho. Pamene khomalo lagwa, kodi anthu sadzakufunsani kuti, ‘Kodi njereza yemwe munapaka uja ali kuti?’

“Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova akuti: Mwa ukali ndidzakunthitsa mphepo ya mkuntho. Ndidzagwetsa matalala akuluakulu ndili ndi ukali ndipo ndidzavumbwitsa mvula yamphamvu ndi mkwiyo mpaka khomalo litawonongeka kotheratu. Ndidzagwetsa khoma limene munalipaka njerezalo. Ndidzaligumuliratu mpaka pansi kotero kuti maziko ake adzaoneka. Khomalo likadzagwa, inu mudzawonongekamo; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova. Kotero ndidzagwiritsa ntchito mkwiyo wanga pa khomali ndi pa amene analipaka njereza. Pambuyo pake ndidzakuwuzani kuti, ‘Khoma lagwa pamodzi ndi amene analipaka njereza. Agwanso aneneri a Yerusalemu amene ankalosa za Yerusalemu nʼkumati anaona mʼmasomphenya za mtendere wa Yerusalemu pamene mtendere kunalibe konse, akutero Ambuye Wamphamvuzonse.’

“Tsono iwe mwana wa munthu, yankhulapo pa nkhani za akazi amene ali pakati pa anthu ako. Iwo amanenera zopeka za mʼmutu mwawo. Tsono adzudzule. Uwawuze kuti, ‘Ambuye Yehova akuti: Tsoka kwa akazi amene amasoka zithumwa zapamkono, amenenso amasoka nsalu za kumutu za anthu. Kodi mufuna kukola mitima ya anthu anga, inuyo nʼkupulumutsa moyo wanu? Ponamiza anthu anga amene amamva za mabodza anu, inu mwapha anthu amene sanayenera kufa ndipo mwasiya ndi moyo amene sanayenera kukhala ndi moyo.

“ ‘Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ine ndikudana ndi zithumwa zanu zimene mumakokera nazo mitima ya anthu ngati mbalame. Ndidzazingʼamba kudzichotsa pa mikono yanu. Choncho ndidzapulumutsa miyoyo ya anthu amene munawakola ngati mbalame. Ndidzangʼamba nsalu zanu za matsengazo ndi kupulumutsa anthu anga mʼmanja mwanu, ndipo simudzakhalanso ndi mphamvu yowakolera. Pamenepo inu mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova. Popeza kuti munatayitsa mtima anthu olungama ngakhale sindinafune kuti ataye mtima; ndipo munalimbitsa anthu oyipa kuti asaleka machimo awo motero sakutha kupulumutsa moyo wawo, choncho inu simudzaonanso masomphenya abodza kapena kuwombeza. Ine ndidzapulumutsa anthu anga mʼmanja mwanu. Ndipo pamenepo inu mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.’ ”

Read More of Ezekieli 13

Ezekieli 14:1-23

Yehova Adzudzula Opembedza Mafano

Tsiku lina ena mwa akuluakulu a Israeli anabwera kwa ine ndipo anakhala pansi pamaso panga. Ndipo Yehova anandipatsa uthenga uwu nati, “Iwe mwana wa munthu, anthu awa ayika mtima pa mafano awo. Ayikanso maso awo pa zinthu zina zoyipa zopunthwitsa. Kodi ayembekezera kuti ndiwayankhe chimene atandifunse? Tsono yankhula nawo ndi kuwawuza kuti zimene akunena Ambuye Yehova: ‘Ngati Mwisraeli aliyense ayika mtima wake pa mafano ndi kuyika maso ake pa zinthu zoyipa zopunthwitsa, kenaka nʼkupita kwa mneneri, Ineyo Yehova mwini wakene ndidzamuyankha molingana ndi kuchuluka kwa mafano ake. Ine ndidzachita zimenezi kuti mwina nʼkukopa mitima ya anthu a Israeli, amene andisiya chifukwa cha mafano awo.’

“Nʼchifukwa chake uwawuze Aisraeli kuti Ine Ambuye Yehova ndikuti: Lapani! Siyani mafano anu ndi ntchito zanu zonse zonyansa!

“ ‘Ngati Mwisraeli wina aliyense kapena mlendo wina aliyense wokhala pakati pa Israeli adzichotsa yekha kwa Ine ndi kuyika mtima pa mafano ake ndi kuyikanso maso ake pa zinthu zopunthwitsa ndipo kenaka nʼkupita kwa mneneri kukafunsa nzeru, Ineyo Yehova mwini wakene ndidzamuyankha. Ine ndidzalimbana naye munthu ameneyo ndipo ndidzamusandutsa chitsanzo ndi chisudzo. Ndidzamuchotsa pakati pa anthu anga. Pamenepo inu mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

“ ‘Ndipo ngati mneneri anyengedwa nanenera, Ine Yehova ndiye ndamunyenga mneneri ameneyo, ndipo ndidzatambasula dzanja langa kumukantha ndi kumuwononga pakati pa anthu anga Aisraeli. Iwo adzalangidwa chifukwa cha kulakwa kwawo. Chilango cha wodzafunsira nzeru kwa mneneri chidzafanana ndi chilango cha mneneriyo. Ndidzachita zimenezi kuti Aisraeli asasocherenso kundisiya Ine ndi kuti asadziyipitsenso ndi machimo awo. Adzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wawo, akutero Ambuye Yehova.’ ”

Chilango Chosathawika

Yehova anayankhula nane kuti, “Iwe mwana wa munthu, ngati dziko lindichimwira posandikhulupirira, Ine ndidzatambasula dzanja langa kulikantha pochepetsa chakudya chake. Ndidzatumiza njala pa dzikolo ndi kuwononga anthu ake ndi nyama zomwe. Ngakhale anthu atatu awa, Nowa, Danieli ndi Yobu akanakhala mʼmenemo, akanangopulumutsa moyo wawo chifukwa cha chilungamo chawo. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.

“Kapena ndikanatumiza zirombo mʼdziko monse ndi kulisiya lopanda anthu, ndipo dzikolo nʼkukhala chipululu chakuti munthu sangadutse chifukwa cha zirombo. Apanso, ndikunenetsa Ine Ambuye Yehova kuti, ‘Ngakhale anthu atatu awa akanakhalamo, sakanatha kupulumutsa ana awo aamuna ndi aakazi. Iwo okha akanapulumuka, koma dziko likanasanduka chipululu.’

“Kapena ndikanatumiza lupanga mʼdzikolo ndi kunena kuti, ‘Lupanga lipite mʼdziko monse,’ ndi kuwononga anthu ake ndi nyama zomwe. Apanso ndikunenetsa Ine Ambuye Yehova kuti, ‘Ngakhale anthu atatu awa akanakhalamo, sakanatha kupulumutsa ana awo aamuna kapena ana aakazi. Iwo okha akanapulumuka.’

“Kapena ndikanatumiza mliri mʼdzikomo ndi kuonetsa ukali wanga pokhetsa magazi, kuwononga anthu ake ndi nyama zomwe. Apanso ndikunenetsa Ine Ambuye Yehova kuti ngakhale Nowa, Danieli ndi Yobu akanakhala mʼmenemo, sakanatha ngakhale kupulumutsa mwana wamwamuna kapena wamkazi. Akanangodzipulumutsa okha chifukwa cha chilungamo chawo.

“Pakuti Ambuye Yehova akuti: Kudzakhala zoopsa kwambiri pamene ndidzatumiza pa Yerusalemu zilango zanga zinayi izi: lupanga, njala, zirombo ndi mliri kuti ziwononge anthu ake ndi nyama zomwe! Komabe padzakhala ena opulumuka, ana aamuna ndi ana aakazi amene adzatulutsidwa mʼdzikomo. Iwo adzabwera kwa inu, ndipo mukadzaona makhalidwe awo ndi zochita zawo, mitima yanu idzakhala pansi mukadzakumbukira chilango chimene ndinachita pa Yerusalemu. Mitima yanu idzakhala pansi mukadzaona makhalidwe awo ndi zochita zawo. Tsono mudzadziwa kuti Yerusalemu sindinamuchite zimenezi popanda chifukwa, akutero Ambuye Yehova.”

Read More of Ezekieli 14

Ezekieli 15:1-8

Yerusalemu, Mtengo Wamphesa Wosabereka

Yehova anayankhulanso nane kuti, “Iwe mwana wa munthu, kodi mtengo wamphesa umapambana bwanji mtengo wina uliwonse? Nthambi zake zimapambana bwanji nthambi ina iliyonse. Mtengo umene uja nʼkupangira chiyani? Kodi anthu angathe kupangira chikhomo chokolekapo zinthu zawo? Taonani, ndi nkhuni chabe zosonkhera moto. Ukaponyedwa pa moto monga nkhuni ndi kuyaka mbali zonse ndi kusanduka makala, kodi ungagwiritsidwe ntchito ina iliyonse? Ngati pamene unali wosapsa sukanatheka kuwugwiritsa ntchito, nanga bwanji utapserera ndi moto, adzawugwiritsa ntchito bwanji?

“Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova akuti, ‘Mtengo wamphesa ndidzawuponya mʼmoto monga ndimachitira ndi mitengo ina ya ku nkhalango. Momwemonso ndidzachita ndi anthu a ku Yerusalemu. Ndidzawalanga pamenepo ngakhale iwo atuluka pa moto, motowo udzawatenthabe. Ndipo pamene ndidzatsutsana nawo, mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova. Ine ndidzasandutsa dziko kukhala chipululu chifukwa anthu akhala osakhulupirika, akutero Ambuye Yehova.’ ”

Read More of Ezekieli 15