Eksodo 33:7-23, Eksodo 34:1-35 CCL

Eksodo 33:7-23

Tenti ya Msonkhano

Tsono Mose ankatenga tenti ndi kukayimanga kunja kwa msasa chapatalipo, ndipo ankayitcha “tenti ya msonkhano.” Aliyense wofuna kukafunsa kanthu kwa Yehova amapita ku tenti ya msonkhano kunja kwa msasa. Ndipo nthawi ina iliyonse imene Mose amapita ku tenti anthu onse amanyamuka ndi kuyimirira pa makomo amatenti awo, kumuyangʼana Mose mpaka atalowa mu tentimo. Mose akamalowa mu tenti, chipilala cha mtambo chimatsika ndi kukhala pa khomo pamene Yehova amayankhula ndi Mose. Nthawi zonse anthu akaona chipilala cha mtambo chitayima pa khomo la tentiyo amayimirira ndi kupembedza, aliyense ali pa khomo la tenti yake. Yehova amayankhula ndi Mose maso ndi maso ngati mmene munthu amayankhulira ndi bwenzi lake. Kenaka Mose amabwerera ku msasa koma womuthandiza wake, Yoswa, mwana wa Nuni samachoka pa tentiyo.

Mose ndi Ulemerero wa Yehova

Mose anati kwa Yehova, “Inu mwakhala mukundiwuza kuti, ‘Tsogolera anthu awa,’ koma simunandiwuze amene mudzamutuma kuti apite pamodzi nane. Inu mwanena kuti, ‘Ndikukudziwa bwino kwambiri ndipo wapeza chisomo pamaso panga.’ Ngati mwakondwera nane ndiphunzitseni njira zanu kuti ndikudziweni ndi kupitiriza kupeza chisomo pamaso panu. Kumbukirani kuti mtundu uwu ndi anthu anu.”

Yehova anayankha kuti, “Ine ndemwe ndidzapita pamodzi ndi iwe, ndipo ndidzakupatsa mpumulo.”

Kenaka Mose anati kwa Yehova, “Ngati inu simupita nafe, musatitumize kuti tipite, kutichotsa pano. Kodi wina adzadziwa bwanji kuti inu mwandikomera mtima pamodzi ndi anthu awa ngati simupita nafe? Kodi nʼchiyani chomwe chidzatisiyanitse pakati pa anthu onse amene ali pa dziko lapansi?”

Ndipo Yehova anati kwa Mose, “Ine ndidzachita zimene iwe wandipempha chifukwa Ine ndikukondwera nawe, ndikukudziwa bwino lomwe.”

Kenaka Mose anati, “Tsopano ndionetseni ulemerero wanu.”

Ndipo Yehova anati, “Ine ndidzakuonetsa ulemerero wanga wonse ndipo ndidzatchula dzina langa lakuti Yehova pamaso pako. Ine ndidzachitira chifundo amene ndikufuna kumuchitira chifundo ndipo ndidzakomera mtima amene ndikufuna kumukomera mtima.” Iye anati, “Koma iwe sungaone nkhope yanga, pakuti palibe munthu amene amaona Ine nakhala ndi moyo.”

Ndipo Yehova anati, “Pali malo pafupi ndi ine pomwe ungathe kuyima pa thanthwe. Pamene ulemerero wanga udutsa, ndidzakuyika mʼphanga la thanthwe ndi kukuphimba ndi dzanja langa mpaka nditadutsa. Kenaka ine ndidzachotsa dzanja langa ndipo iwe udzaona msana wanga, koma nkhope yanga sidzaoneka.”

Read More of Eksodo 33

Eksodo 34:1-35

Miyala ina Yatsopano

Yehova anati kwa Mose, “Sema miyala iwiri yofanana ndi yoyamba ija, ndipo Ine ndidzalembapo mawu amene anali pa miyala yoyamba ija, imene unayiphwanya. Ukonzeke mmamawa, ndipo ubwere ku Phiri la Sinai. Udzaonekera pamaso panga pamwamba pa phiri. Palibe amene abwere nawe kapena kuoneka pena paliponse pafupi ndi phiri. Ndipo ngakhale nkhosa kapena ngʼombe zisadye mʼmbali mwa phirilo.”

Choncho Mose anasema miyala iwiri yofanana ndi yoyamba ija ndipo anapita ku Phiri la Sinai mmawa atanyamula miyala iwiri mʼmanja mwake monga momwe Yehova anamulamulira. Ndipo Yehova anatsika mu mtambo ndi kuyima pamodzi ndi Mose ndi kulengeza dzina lake lakuti Yehova. Ndipo Iye anadutsa kutsogolo kwa Mose akulengeza kuti, “Yehova, Yehova, Mulungu wachifundo ndi wokoma mtima, wosapsa mtima msanga, wodzaza ndi chikondi chosasinthika ndi kukhulupirika, waonetsa chikondi chosasinthika kwa anthu miyandamiyanda, wokhululukira zoyipa, kuwukira, ndiponso tchimo, komatu salekerera ochimwa kuti asalangidwe. Iye amalanga ana ndi zidzukulu chifukwa cha machimo a makolo awo mpaka mʼbado wachitatu ndi wachinayi.”

Pamenepo Mose anawerama pansi napembedza. Iye anati, “Chonde Ambuye, ngati ndapeza chisomo pamaso panu, lolani Ambuye kuti mupite nafe pamodzi. Ngakhale kuti anthuwa ndi nkhutukumve, khululukirani zoyipa ndi machimo athu, ndipo mutenge ife kukhala anthu anu.”

Choncho Yehova anati: “Ine ndikuchita nanu pangano. Ndidzachita zodabwitsa pamaso pa anthu onse zimene sizinachitikenso ndi mtundu wina uliwonse wa anthu pa dziko lonse lapansi. Anthu amene mudzakhala pakati pawo adzaona kuopsa kwa ntchito imene Ine Yehova ndidzakuchitireni. Mverani zimene ndikukulamulirani lero. Ine ndidzathamangitsa pamaso panu Aamori, Akanaani, Ahiti, Aperezi, Ahivi, ndi Ayebusi. Musamale kuti musakachite mgwirizano ndi anthu amene akukhala mʼdziko limene mukupitalo, chifukwa mukadzatero iwo adzakhala ngati msampha pakati panu. Mukagumule maguwa awo ansembe, mukaswe miyala yawo yachipembedzo, ndipo mukadule mitengo yawo ya Asera. Musapembedze mulungu wina, pakuti Yehova amene dzina lake ndi Nsanje, ndi Mulungu wa nsanje.

“Musamale kuti musakachite mgwirizano ndi anthu amene akukhala mʼdziko limene mukupitalo, chifukwa iwo akamakachita zadama ndi milungu yawo ndi kupereka nsembe, adzakuyitanani ndipo inu mudzadya nsembe zawo. Ndipo inu mukasankha ena mwa ana awo aakazi kukhala akazi a ana anu, akaziwo akakachita zadama ndi milungu yawo, akatsogolera ana anu aamuna kuchita chimodzimodzi.

“Musadzipangire milungu yosungunula.

“Muzichita chikondwerero cha buledi wopanda yisiti. Kwa masiku asanu ndi awiri muzidya buledi wopanda yisiti monga momwe ndinakulamulirani. Muzichita zimenezi pa nthawi yoyikika mwezi wa Abibu, pakuti mwezi umenewu inu munatuluka mʼdziko la Igupto.

“Mwana aliyense woyamba kubadwa ndi wanga, pamodzi ndi ziweto zoyamba kubadwa zazimuna kuchokera ku ngʼombe kapena nkhosa. Muziwombola mwana woyamba kubadwa wa bulu popereka mwana wankhosa. Mukapanda kumuwombola mupheni. Muziwombola ana anu onse aamuna.

“Palibe ndi mmodzi yemwe adzaonekere pamaso panga wopanda kanthu mʼdzanja lake.

“Muzigwira ntchito masiku asanu ndi limodzi, koma tsiku lachisanu ndi chiwiri, musagwire ntchito ina iliyonse, Ngakhale nthawi yolima ndi yokolola muyenera kupuma.

“Muzichita Chikondwerero cha Masabata, chifukwa ndi chikondwerero cha tirigu woyambirira kucha, ndiponso ndi chikondwerero cha kututa zokolola pakutha pa chaka. Amuna onse azionekera pamaso pa Yehova Mulungu wa Israeli, katatu pa chaka. Ine ndidzapirikitsa mitundu inayo pamene inu mukufikako ndi kukulitsa malire anu. Palibe ndi mmodzi yemwe adzafune kulanda dziko lanu ngati inu muzidzapita katatu pa chaka pamaso pa Yehova Mulungu wanu, chaka chilichonse.

“Musapereke magazi anyama ngati nsembe kwa Ine pamodzi ndi chilichonse chimene chili ndi yisiti, ndipo musasunge nsembe ya pa Chikondwerero cha Paska mpaka mmawa.

“Muzibwera ndi zipatso zoyambirira kucha zabwino kwambiri ku nyumba ya Yehova Mulungu wanu.

“Musamaphike kamwana kambuzi mu mkaka wa mayi wake.”

Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Lemba mawu awa pakuti potsatira mawuwa, ine ndipangana pangano ndi iwe ndi Israeli.” Mose anakhala kumeneko pamodzi ndi Yehova masiku 40, usana ndi usiku, wosadya kanthu kapena kumwa madzi. Ndipo iye analemba pa miyala ija mawu a pangano, malamulo khumi.

Nkhope ya Mose Inyezimira

Mose anatsika kuchokera mʼPhiri la Sinai pamodzi ndi miyala iwiri ija ya pangano mʼmanja mwake. Iye sanazindikire kuti nkhope yake imanyezimira pakuti anayankhula ndi Yehova. Aaroni ndi Aisraeli ataona kuti nkhope ya Mose imanyezimira anaopa kumuyandikira. Koma Mose anawayitana. Kotero Aaroni ndi atsogoleri onse a gululo anabwera kwa iye, ndipo anawayankhula. Kenaka Aisraeli onse anamuyandikira, ndipo anawapatsa malamulo onse omwe Yehova anamupatsa pa Phiri la Sinai.

Mose atamaliza kuyankhula nawo anaphimba nkhope yake. Koma nthawi zonse popita pamaso pa Yehova kukayankhula naye amachotsa chophimbacho mpaka atatuluka. Ndipo akatuluka kudzawuza Aisraeli zimene walamulidwa, iwo amaona nkhope yake ikunyezimira. Choncho Mose amaphimba nkhope yake ngakhale pamene amapita kukayankhula ndi Yehova.

Read More of Eksodo 34