Mlaliki 4:1-16, Mlaliki 5:1-20, Mlaliki 6:1-12 CCL

Mlaliki 4:1-16

Matsoka ndi Mavuto a Moyo Uno

Ndinayangʼananso ndi kuona chipsinjo chimene chimachitika pansi pano:

ndinaona misozi ya anthu opsinjika,

ndipo iwo alibe owatonthoza;

mphamvu zinali ndi anthu owapsinjawo

ndipo iwonso analibe owatonthoza.

Ndipo ndinanena kuti akufa,

amene anafa kale,

ndi osangalala kuposa amoyo,

amene akanalibe ndi moyo.

Koma wopambana onsewa

ndi amene sanabadwe,

amene sanaone zoyipa

zimene chimachitika pansi pano.

Ndipo ndinazindikira kuti ntchito zonse zolemetsa ndiponso ntchito zonse zaluso zimachitika chifukwa choti wina akuchitira nsanje mnzake. Izinso ndi zopandapake, nʼkungodzivuta chabe.

Chitsiru chimangoti manja ake lobodo

ndi kudzipha chokha ndi njala.

Nʼkwabwino kukhala ndi dzanja limodzi lodzaza uli pa mtendere,

kuposa kukhala ndi manja awiri odzaza uli pa mavuto,

ndipo uku nʼkungodzivuta chabe.

Ndinaonanso chinthu china chopanda phindu pansi pano:

Panali munthu amene anali yekhayekha;

analibe mwana kapena mʼbale.

Ntchito yake yolemetsa sinkatha,

ndipo maso ake sankakhutitsidwa ndi chuma chake.

Iye anadzifunsa kuti, “Kodi ntchito yosautsayi ndikuyigwirira yani?

Nanga nʼchifukwa chiyani ndikudzimana chisangalalo?”

Izinso ndi zopandapake,

zosasangalatsa!

Kukhala awiri nʼkwabwino kuposa kukhala wekha,

chifukwa ntchito ya anthu awiri ili ndi phindu:

Ngati winayo agwa,

mnzakeyo adzamudzutsa.

Koma tsoka kwa munthu amene agwa

ndipo alibe wina woti amudzutse!

Komanso ngati anthu awiri agona malo amodzi, adzafunditsana.

Koma nanga mmodzi angadzifunditse yekha?

Munthu mmodzi angathe kugonjetsedwa,

koma anthu awiri akhoza kudziteteza.

Chingwe cha maulusi atatu sichidukirapo.

Kutukuka Nʼkopandapake

Wachinyamata wosauka koma wanzeru aposa mfumu yokalamba koma yopusa imene simvanso malangizo. Wachinyamatayo angathe kuchokera ku ndende ndi kudzakhala mfumu, kapena angathe kubadwa wosauka mʼdziko la mfumuyo. Ndipo ndinaona kuti iwo onse amene anakhala ndi moyo ndi kuyenda pansi pano anatsatira wachinyamatayo, amene anatenga malo a mfumu. Mfumu ikhoza kulamulira anthu osawerengeka, komabe itamwalira, palibe amene adzayamikire zomwe mfumuyo inachita. Izinso ndi zopandapake, nʼkungozivuta chabe.

Read More of Mlaliki 4

Mlaliki 5:1-20

Lemekeza Mulungu

Uzisamala mayendedwe ako pamene ukupita ku nyumba ya Mulungu. Upite pafupi kuti ukamvetsere mʼmalo mopereka nsembe ya zitsiru zimene sizizindikira kuti zikuchita zolakwa.

Usamafulumire kuyankhula,

usafulumire mu mtima mwako

kunena chilichonse pamaso pa Mulungu.

Mulungu ali kumwamba

ndipo iwe uli pa dziko lapansi,

choncho mawu ako akhale ochepa.

Kuchuluka kwa mavuto mu mtima kumabweretsa maloto oyipa,

ndipo kuchuluka kwa mawu kumadzetsa uchitsiru.

Pamene ulumbira kwa Mulungu usachedwe kukwaniritsa chimene walumbiracho. Iye sakondweretsedwa ndi chitsiru; kwaniritsa lumbiro lako. Kuli bwino kusalumbira kusiyana ndi kulumbira koma osakwaniritsa lumbirolo. Pakamwa pako pasakuchimwitse. Ndipo usanene kwa mthenga wa mʼNyumba ya Mulungu kuti, “Ndinalakwitsa polumbira.” Chifukwa chiyani ukufuna Mulungu akwiye ndi mawu ako ndiponso ntchito ya manja ako? Maloto ochuluka ndi mawu ochuluka ndi zinthu zopandapake. Kotero lemekeza Mulungu.

Chuma Nʼchopandapake

Ngati uwona anthu osauka akuzunzika mʼdziko, ndiponso anthu ena akupsinja anzawo ndi kuwalanda ufulu wawo, usadabwe ndi zinthu zimenezi; pakuti woyangʼanira ali naye wina womuyangʼanira wamkulu, ndipo pamwamba pa awiriwa pali ena akuluakulu owaposa. Anthu onse amatengako zokolola za mʼminda: koma ndi mfumu yokha imene imapeza phindu la mindayi.

Aliyense amene amakonda ndalama sakhutitsidwa ndi ndalamazo;

aliyense amene amakonda chuma sakhutitsidwa ndi zimene amapeza.

Izinso ndi zopandapake.

Chuma chikachuluka

akudya nawo chumacho amachulukanso.

Nanga mwini wake amapindulapo chiyani

kuposa kumangochiyangʼana ndi maso ake?

Wantchito amagona tulo tabwino

ngakhale adye pangʼono kapena kudya kwambiri,

koma munthu wolemera, chuma

sichimulola kuti agone.

Ine ndinaona choyipa chomvetsa chisoni pansi pano:

chuma chokundikidwa chikupweteka mwini wake yemwe,

kapena chuma chowonongedwa pa nthawi yatsoka,

kotero kuti pamene wabereka mwana

alibe kanthu koti amusiyire.

Munthu anabadwa wamaliseche kuchokera mʼmimba mwa amayi ake,

ndipo monga iye anabadwira, adzapitanso choncho.

Pa zonse zimene iye anakhetsera thukuta

palibe nʼchimodzi chomwe chimene adzatenge mʼmanja mwake.

Izinso ndi zoyipa kwambiri:

munthu adzapita monga momwe anabwerera,

ndipo iye amapindula chiyani,

pakuti amagwira ntchito yolemetsa yopanda phindu?

Masiku ake onse ndi odzaza ndi mdima,

kukhumudwa kwakukulu, masautso ndi nkhawa.

Tsono ndinazindikira kuti nʼchabwino ndi choyenera kuti munthu azidya ndi kumwa, ndi kukhutitsidwa ndi ntchito yake yolemetsa imene amayigwira pansi pano pa nthawi yake yochepa imene Mulungu amamupatsa, poti ichi ndiye chake. Komatu pamene Mulungu apereka chuma kwa munthu aliyense ndi zinthu zina, ndi kulola kuti akondwere ndi chumacho, munthuyo alandire chumacho ndi kusangalala ndi ntchito yake, imene ndi mphatso yochokera kwa Mulungu. Munthu wotereyu saganizirapo za masiku a moyo wake, chifukwa Mulungu amamutanganidwitsa ndi chisangalalo cha mu mtima mwake.

Read More of Mlaliki 5

Mlaliki 6:1-12

Ine ndinaona choyipa china pansi pano, ndipo chimasautsa anthu kwambiri: Mulungu amapereka chuma, zinthu ndi ulemu kwa munthu, kotero kuti munthuyo sasowa kanthu kalikonse kamene akukalakalaka, koma Mulungu samulola kuti adyerere zinthuzo, ndipo mʼmalo mwake amadyerera ndi mlendo. Izi ndi zopandapake, ndi zoyipa kwambiri.

Ngakhale munthu atabereka ana 100 ndi kukhala ndi moyo zaka zambiri; komatu ngakhale atakhala zaka zambiri chotani, ngati iye sangadyerere chuma chake ndi kuyikidwa mʼmanda mwaulemu, ine ndikuti mtayo umamuposa iyeyo. Mtayo umangopita pachabe ndipo umapita mu mdima, ndipo mu mdimamo dzina lake limayiwalika. Ngakhale kuti mtayowo sunaone dzuwa kapena kudziwa kanthu kalikonse, koma umapumula kuposa munthu uja, ngakhale munthuyo atakhala ndi moyo zaka 2,000, koma ndi kulephera kudyerera chuma chake. Kodi onsewa sapita malo amodzi?

Ntchito yonse ya munthu imathera pakamwa pake,

komatu iye sakhutitsidwa ndi pangʼono pomwe.

Kodi munthu wanzeru

amaposa motani chitsiru?

Kodi munthu wosauka amapindula chiyani

podziwa kukhala bwino pamaso pa anthu ena?

Kuli bwino kumangoona zinthu ndi maso

kusiyana ndi kumangozilakalaka mu mtima.

Izinso ndi zopandapake,

nʼkungodzivuta chabe.

Chilichonse chimene chilipo anachitchula kale dzina,

za mmene munthu alili nʼzodziwika;

sangathe kutsutsana ndi munthu

amene ali wamphamvu kupambana iyeyo.

Mawu akachuluka

zopandapake zimachulukanso,

nanga munthu zimamupindulira chiyani?

Pakuti ndani amene amadziwa chomwe ndi chabwino pa moyo wa munthu, pakuti moyo wake ndi wa masiku ochepa ndi opandapake, umangopitira ngati mthunzi. Ndani amene angamufotokozere zimene zidzachitika pansi pano iye atapita?

Read More of Mlaliki 6