Machitidwe a Atumwi 4:23-37, Machitidwe a Atumwi 5:1-11 CCL

Machitidwe a Atumwi 4:23-37

Okhulupirira Apemphera

Atamasulidwa Petro ndi Yohane anapita kwa anzawo ndipo anawafotokozera zonse zimene akulu a ansembe ndi akulu anawawuza. Anthu atamva zimenezi anafuwula ndi mtima umodzi napemphera kwa Mulungu. Iwo anati, “Ambuye wolamulira zonse, Inu munalenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi nyanja ndiponso zonse zili mʼmenemo. Inu munayankhula mwa Mzimu Woyera kudzera pakamwa pa Davide kholo lathu, mtumiki wanu kuti,

“ ‘Nʼchifukwa chiyani anthu a mitundu ina akufuna kuchita chiwembu,

ndipo akonzekera kuchita zopandapake?

Mafumu a dziko lapansi akugwirizana nazo;

ndipo olamulira asonkhana pamodzi

kulimbana ndi Ambuye

ndi wodzozedwa wakeyo.’

Zoonadi, Herode ndi Pontiyo Pilato anasonkhana pamodzi ndi amitundu ndiponso Aisraeli, mu mzinda muno, kupanga zolimbana ndi mtumiki wanu woyera Yesu, amene Inu munamudzoza. Iwo anachita zimene munakonzeratu mwachifuniro chanu ndi mphamvu yanu kuti zichitike. Tsopano, Ambuye taonani kuti atiopseza, tithandizeni ife atumiki anu, kuti tiyankhule mawu anu molimba mtima. Tambasulani dzanja lanu kuchiritsa anthu ndipo kuti, zizindikiro zodabwitsa zichitike mʼdzina la mtumiki wanu woyera Yesu.”

Iwo atatha kupemphera, malo amene anasonkhanapo anagwedezeka. Ndipo iwo onse anadzazidwa ndi Mzimu Woyera ndipo anayankhula Mawu a Mulungu molimba mtima.

Okhulupirira Agawana Zinthu Zawo

Okhulupirira onse anali a mtima umodzi, ndi maganizo amodzi. Palibe munthu amene amati zomwe anali nazo zinali zake zokha, koma amagawana chilichonse chimene anali nacho. Atumwi anapitirira kuchitira umboni mwa mphamvu zakuuka kwa Ambuye Yesu, ndipo pa iwo panali chisomo chochuluka. Panalibe anthu osowa kanthu pakati pawo. Pakuti amene anali ndi malo, kapena nyumba amagulitsa ndi kubweretsa ndalamazo ndi kuzipereka kwa atumwi, ndipo zimagawidwa kwa aliyense amene anali ndi chosowa.

Yosefe, wa fuko la Levi, wochokera ku Kupro amene atumwi anamutcha Barnaba, kutanthauza kuti mwana wachilimbikitso, anagulitsa munda wake ndipo anadzapereka ndalamazo kwa atumwi.

Read More of Machitidwe a Atumwi 4

Machitidwe a Atumwi 5:1-11

Hananiya ndi Safira

Koma munthu wina dzina lake Hananiya, pamodzi ndi mkazi wake Safira, anagulitsanso munda wawo. Mogwirizana ndi mkazi wakeyo anapatulapo pa ndalamazo nazisunga, ndipo anatenga zotsalazo ndi kukapereka kwa atumwi.

Koma Petro anamufunsa kuti, “Hananiya, chifukwa chiyani Satana anadzaza chotere mu mtima wako kuti unamize Mzimu Woyera ndipo wapatula ndi kusunga ndalama? Kodi sunali wako usanagulitse? Ndipo utagulitsa ndalamazo sizinali mʼmanja mwako kodi? Nʼchiyani chinakuchititsa zimenezi? Iwe sunanamize anthu koma Mulungu.”

Hananiya atamva mawu amenewa anagwa pansi namwalira. Onse amene anamva zimene zinachitikazi anachita mantha kwambiri. Kenaka anyamata anafika, nakulunga thupi lake, ndipo anamunyamula ndi kukamuyika mʼmanda.

Patapita maora atatu mkazi wake analowa, wosadziwa zimene zinachitika. Petro anamufunsa iye kuti, “Tandiwuza, kodi izi ndi ndalama zonse zimene iwe ndi Hananiya munalandira mutagulitsa munda?”

Mkaziyo anati, “Inde ndi zimenezo.”

Petro anati kwa iye, “Bwanji inu munapangana kuyesa Mzimu wa Ambuye? Taona! Anthu amene anakayika mwamuna wako mʼmanda ali pa khomo, ndipo adzakunyamula iwenso.”

Nthawi yomweyo anagwa pansi pa mapazi a Petro ndipo anamwalira. Ndipo anyamata aja analowa, napeza kuti wafa kale, anamunyamula ndi kukamuyika pafupi ndi mwamuna wake. Mpingo wonse ndi anthu onse amene anamva zimenezi anachita mantha kwambiri.

Read More of Machitidwe a Atumwi 5