2 Mbiri 16:1-14, 2 Mbiri 17:1-19, 2 Mbiri 18:1-27 CCL

2 Mbiri 16:1-14

Zaka Zotsiriza za Asa

Mʼchaka cha 36 cha ufumu wa Asa, Baasa mfumu ya Israeli inapita kukathira nkhondo dziko la Yuda. Anamangira mpanda mzinda wa Rama kuletsa aliyense kutuluka kapena kulowa mʼdziko la Asa mfumu ya Yuda.

Ndipo Asa anatenga siliva ndi golide ku malo osungirako a mʼNyumba ya Mulungu ndi ku nyumba yake yaufumu ndi kuzitumiza kwa Beni-Hadadi mfumu ya Aramu imene inkakhala mu Damasiko. Iye anati, “Pakhale pangano pakati pa inu ndi ine, monga zinalili pakati pa abambo anu ndi abambo anga. Taonani, ine ndikutumiza kwa inu siliva ndi golide. Tsopano thetsani mgwirizano wanu ndi Baasa mfumu ya Israeli kuti achoke kwa ine.”

Beni-Hadadi anagwirizana ndi mfumu Asa ndipo anatumiza olamulira nkhondo ake kukathira nkhondo mizinda ya Israeli. Iwo anagonjetsa Iyoni, Dani, Abeli-Maimu ndi mizinda yonse yosungira chuma ya Nafutali. Baasa atamva izi, anasiya kumanga Rama ndipo anayimitsa ntchito yakeyo. Ndipo mfumu Asa anabwera ndi Ayuda onse, ndipo anachotsa miyala ndi matabwa ku Rama amene Baasa amagwiritsa ntchito. Ndi zimenezi Asa ankamangira Geba ndi Mizipa.

Nthawi imeneyi mlosi Hanani anabwera kwa Asa mfumu ya Yuda ndipo anati kwa iye, “Chifukwa chakuti munadalira mfumu ya Aramu osati Yehova Mulungu wanu, gulu la ankhondo la mfumu ya ku Aramu lapulumuka mʼmanja mwanu. Kodi Akusi ndi Alibiya sanali gulu lankhondo lamphamvu lokhala ndi magaleta ochuluka ndi okwera magaleta ake? Koma pamene inu munadalira Yehova, Iye anawapereka mʼdzanja lanu. Pakuti Yehova amayangʼana uku ndi uku pa dziko lonse lapansi kuti alimbikitse iwo amene mitima yawo ayipereka kwathunthu kwa Iye. Inu mwachita chinthu chopusa ndipo kuyambira lero mudzakhala pa nkhondo.”

Asa anamupsera mtima mlosi uja chifukwa cha izi mwakuti anakwiya kwambiri namuyika mʼndende. Pa nthawi yomweyonso Asa anazunza mwankhanza anthu ena.

Ntchito zina za mfumu Asa, kuyambira pachiyambi mpaka kumapeto zalembedwa mʼbuku la mafumu a Yuda ndi Israeli. Mʼchaka cha 39 cha ufumu wake, Asa anayamba kudwala nthenda ya mapazi. Ngakhale nthendayo inali yaululu kwambiri, komabe iye sanafunefune Yehova, koma anafuna thandizo kwa asingʼanga. Ndipo mʼchaka cha 41 cha ufumu wake, Asa anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda pamodzi ndi makolo ake. Iye anayikidwa mʼmanda amene anadzisemera yekha mu Mzinda wa Davide. Anagoneka mtembo wake pa chithatha chimene anayikapo zonunkhira zamitundumitundu, ndipo anasonkha chimoto chachikulu pomuchitira ulemu.

Read More of 2 Mbiri 16

2 Mbiri 17:1-19

Yehosafati Mfumu ya Yuda

Yehosafati mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake ndipo anadzilimbitsa pofuna kulimbana ndi Israeli. Iye anayika magulu a asilikali mʼmizinda yonse yotetezedwa ya Yuda, ndipo anamanga maboma mu Yuda ndi mʼmizinda yonse ya Efereimu imene Asa abambo ake analanda.

Yehova anali ndi Yehosafati chifukwa mʼzaka zoyambirira anatsatira makhalidwe a Davide abambo ake. Iye sanafunsire kwa Abaala. Koma anafunafuna Mulungu wa abambo ake ndipo anatsatira malamulo ake osati zochita za Israeli. Yehova anakhazikitsa kolimba ufumuwo mʼmanja mwake ndipo Ayuda onse anabweretsa mphatso kwa Yehosafati, kotero kuti anali ndi chuma ndi ulemu wambiri. Mtima wake anawupereka kutsatira Yehova, kuwonjezera apo, anachotsa malo onse achipembedzo ndi mafano a Asera mu Yuda.

Mʼchaka chachitatu cha ufumu wake, iye anatuma akuluakulu ake Beni-Haili, Obadiya, Zekariya, Netaneli ndi Mikaya kukaphunzitsa mʼmizinda ya Yuda. Pamodzi ndi iwo panali Alevi ena: Semaya, Netaniya, Zebadiya, Asaheli, Semiramoti, Yonatani, Adoniya, Tobiya ndi Tobu-Adoniya ndiponso ansembe Elisama ndi Yehoramu. Iwo anaphunzitsa mu Yuda monse atatenga Buku la Malamulo a Yehova iwo anayenda mʼmizinda yonse ya ku Yuda ndipo anaphunzitsa anthu.

Kuopsa kwa Yehova kunali pa maufumu onse a mayiko oyandikana ndi Yuda, kotero kuti sanachite nkhondo ndi Yehosafati. Afilisti ena anabweretsa kwa Yehosafati mphatso ndi siliva ngati msonkho, ndipo Aarabu anabweretsa ziweto: nkhosa zazimuna 7,700 ndi mbuzi 7,700.

Mphamvu za Yehosafati zinkakulirakulira. Iye anamanga malo otetezedwa ndi mizinda yosungiramo chuma mu Yuda ndipo anali ndi katundu wambiri mʼmizinda ya Yuda. Iye anayikanso asilikali odziwa bwino nkhondo mu Yerusalemu. Chiwerengero chawo potsata mabanja awo chinali chotere:

kuchokera ku Yuda, atsogoleri a magulu 1,000;

mtsogoleri Adina, anali ndi anthu 300,000 odziwa nkhondo;

otsatana naye, mtsogoleri Yehohanani, anali ndi anthu 280,000;

otsatana naye, Amasiya mwana wa Zikiri amene anadzipereka yekha kutumikira Yehova, anali ndi anthu 200,000.

Kuchokera ku Benjamini:

Eliada, msilikali wolimba mtima, anali ndi anthu 200,000 amene anali ndi mauta ndi zishango;

otsatana naye, Yehozabadi, anali ndi anthu 180,000 okonzekera nkhondo.

Awa ndi anthu amene ankatumikira mfumu osawerengera amene anawayika mʼmizinda yotetezedwa mʼdziko lonse la Yuda.

Read More of 2 Mbiri 17

2 Mbiri 18:1-27

Mikaya Anenera Motsutsa Ahabu

Tsono Yehosafati anali ndi chuma chambiri ndi ulemu, ndipo iye anachita mgwirizano wa ukwati ndi Ahabu. Patapita zaka zina, iye anapita kukacheza kwa Ahabu mu Samariya. Ahabu anaphera iye pamodzi ndi anthu amene anali naye, nkhosa zambiri ndi ngʼombe ndipo anamuwumiriza kuti akathire nawo nkhondo Ramoti Giliyadi Ahabu mfumu ya Israeli anafunsa Yehosafati mfumu ya Yuda kuti, “Kodi mudzapita nane kukalimbana ndi Ramoti Giliyadi?”

Yehosafati anayankha kuti, “Ine ndili ngati inu nomwe, ndi anthu anga ngati anthu anu. Ife tikhala nanu limodzi pa nkhondoyi.” Koma Yehosafati anatinso kwa mfumu ya Israeli, “Choyamba mupemphe nzeru kwa Yehova.”

Tsono mfumu ya Israeli inasonkhanitsa aneneri 400 ndipo inawafunsa kuti, “Kodi tipite kukalimbana ndi Ramoti Giliyadi kapena tileke?”

Iwo anayankha kuti, “Pitani, pakuti Mulungu adzawupereka mʼdzanja la mfumu.”

Koma Yehosafati anafunsanso kuti, “Kodi kuno kulibe mneneri wina wa Yehova amene ife tingafunsireko?”

Mfumu ya Israeli inayankha Yehosafati kuti, “Alipo munthu mmodzi amene ife kudzera mwa iye titha kufunsira kwa Yehova, koma ndimadana naye chifukwa sandilosera zabwino koma zoyipa nthawi zonse. Iyeyu ndi Mikaya mwana wa Imula.”

Yehosafati anayankha kuti, “Mfumu isanene motero.”

Choncho mfumu ya Israeli inayitana mmodzi mwa akuluakulu ake ndipo inati, “Kamutengeni Mikaya mwana wa Imula, abwere msanga.”

Mfumu ya Israeli ndi Yehosafati mfumu ya Yuda, atavala mikanjo yawo yaufumu anali atakhala pa mipando yawo yaufumu pabwalo lopunthira tirigu pa khomo la chipata cha Samariya, pamodzi ndi aneneri onse akunenera pamaso pawo. Tsono Zedekiya mwana wa Kenaana anapanga nyanga zachitsulo ndipo analengeza kuti, “Yehova akuti, ‘Ndi nyanga izi udzagunda Aaramu mpaka atawonongedwa!’ ”

Aneneri ena onse amanenera chimodzimodzi kuti, “Kathireni nkhondo Ramoti Giliyadi ndipo kapambaneni, pakuti Mulungu adzamupereka mʼdzanja la mfumu.”

Wauthenga amene anapita kukayitana Mikaya anati kwa iye, “Taonani aneneri ena onse ngati munthu mmodzi akulosera za chipambano cha mfumu. Mawu anunso agwirizane ndi awo ndipo muyankhule zabwino.”

Koma Mikaya anati, “Pali Yehova wamoyo, ine ndidzanena zimene Mulungu wanga andiwuze.”

Iye atafika mfumu inamufunsa kuti, “Mikaya, kodi tipite ku nkhondo kukalimbana ndi Ramoti Giliyadi kapena tileke?”

Iye anayankha kuti, “Kathireni nkhondo ndipo kapambaneni, pakuti mzindawo udzaperekedwa mʼdzanja lanu.”

Mfumu inati kwa iye, “Kodi ndikuwuze kangati kuti ulumbire kuti usandiwuze chilichonse koma zoonadi mʼdzina la Yehova?”

Ndipo Mikaya anayankha kuti, “Ine ndinaona Aisraeli atabalalika mʼmapiri monga nkhosa zopanda mʼbusa, ndipo Yehova anati, ‘Anthu awa alibe mbuye wawo. Aliyense apite kwawo mu mtendere!’ ”

Mfumu ya Israeli inati kwa Yehosafati, “Kodi ine sindinakuwuzeni kuti sandinenera zabwino koma zoyipa zokhazokha?”

Mikaya anapitiriza ndi kunena kuti, “Imvani tsono mawu a Yehova: Ine ndinaona Yehova atakhala pa mpando wake waufumu ndi gulu lonse lakumwamba litayima ku dzanja lake lamanja ndi lamanzere. Ndipo Yehova anati, ‘Ndani amene adzamunyengerere Ahabu mfumu ya Israeli kuti akathire nkhondo Ramoti Giliyadi ndi kukafera komweko?’

“Wina ananena zina, winanso ananena zina.” Pomaliza mzimu wina unatuluka ndi kuyima pamaso pa Yehova ndipo unati, “Ine ndikamunyengerera!”

Yehova anafunsa kuti, “Ukagwiritsa ntchito njira yanji?”

Mzimuwo unati, “Ine ndidzapita ndi kukhala mzimu wabodza mʼkamwa mwa aneneri ake onse!”

Yehova anati, “ ‘Iwe ukamunyengadi iyeyo. Pita kachite zimenezo.’

“Choncho Yehova wayika mzimu wabodza mʼkamwa mwa aneneri anuwa. Yehova waneneratu kuti inu mukaona tsoka.”

Ndipo Zedekiya mwana wa Kenaana anapita pafupi ndi kumenya khofi Mikaya. Zedekiya anafunsa kuti, “Kodi mzimu wochokera kwa Yehova unadzera njira iti pamene unachoka kwa ine kupita kwa iwe?”

Mikaya anayankha kuti, “Udzadziwa pa tsiku limene uzikalowa mʼchipinda chamʼkati kuti ukabisale.”

Pamenepo mfumu ya Israeli inalamula kuti, “Tengani Mikaya ndipo mupite naye kwa Amoni, wolamulira mzindawo ndi kwa Yowasi mwana wa mfumu, ndipo mukanene kuti, ‘Chimene mfumu ikunena ndi ichi; Muyike munthu uyu mʼndende ndipo musamupatse kanthu kalikonse koma buledi ndi madzi pangʼono mpaka nditabwera mwamtendere.’ ”

Mikaya anayankhula kuti, “Ngati inu mukabwera mwamtendere, Yehova sanayankhule kudzera mwa ine.” Ndipo anawonjeza kuti, “Anthu nonsenu, mumve zimene ndanenazi.”

Read More of 2 Mbiri 18