Daily Manna for Wednesday, April 7, 2021

Daily Manna is a daily Bible devotional service provided by Biblica. The Scripture is provided in many forms and is new every day. It is a great way to receive the encouragement and hope found in the Word of God.

Verse of the Day

2 Samueli 22:1-7

Davide anayimbira Yehova nyimbo iyi pamene Yehovayo anamupulumutsa mʼdzanja la adani ake onse ndiponso mʼdzanja la Sauli. Iye anati,

“Yehova ndiye thanthwe langa, chitetezo changa ndi mpulumutsi wanga.

Mulungu wanga ndiye thanthwe langa, mʼmene ndimathawiramo,

chishango changa ndi ndodo yachipulumutso changa.

Iye ndi linga langa, pothawirapo panga ndi mpulumutsi wanga.

Munandipulumutsa mʼmanja mwa anthu ankhanza.

“Ndimayitana Yehova amene ndi woyenera matamando,

ndipo ndapulumutsidwa kwa adani anga.

“Mafunde a imfa anandizinga;

mitsinje yothamanga yachiwonongeko inandiopsa kwambiri.

Anandimanga ndi zingwe za ku manda;

misampha ya imfa inalimbana nane.

“Mʼmasautso anga ndinapemphera kwa Yehova;

ndinapemphera kwa Mulungu wanga.

Iye ali mʼnyumba yake, anamva mawu anga;

kulira kwanga kunafika mʼmakutu ake.