Daily Manna for Thursday, February 13, 2020

Daily Manna is a daily Bible devotional service provided by Biblica. The Scripture is provided in many forms and is new every day. It is a great way to receive the encouragement and hope found in the Word of God.

Verse of the Day

Zefaniya 3:14-17

Imba, iwe mwana wamkazi wa Ziyoni;
    fuwula mokweza, iwe Israeli!
Sangalala ndi kukondwera ndi mtima wako wonse,
    iwe mwana wamkazi wa Yerusalemu!
Yehova wachotsa chilango chako,
    wabweza mdani wako.
Yehova, Mfumu ya Israeli, ali pakati pako;
    sudzaopanso chilichonse.
Pa tsiku limenelo adzanena kwa Yerusalemu kuti,
    “Usaope, iwe Ziyoni;
    usafowoke.
Yehova Mulungu wako ali pakati pako,
    ali ndi mphamvu yopulumutsa.
Adzakondwera kwambiri mwa iwe,
    adzakukhalitsa chete ndi chikondi chake,
    adzayimba mokondwera chifukwa cha iwe.”