Daily Manna for Wednesday, February 12, 2020

Daily Manna is a daily Bible devotional service provided by Biblica. The Scripture is provided in many forms and is new every day. It is a great way to receive the encouragement and hope found in the Word of God.

Verse of the Day

1 Mbiri 16:23-31

Imbirani Yehova, dziko lonse lapansi;
    lalikani za chipulumutso chake tsiku ndi tsiku.
Lengezani za ulemerero wake kwa mitundu yonse,
    ntchito zake zonse zodabwitsa kwa anthu onse.
Pakuti Yehova ndi wamkulu ndi woyenera kwambiri kumutamanda;
    Iyeyo ayenera kuopedwa kuposa milungu yonse.
Pakuti milungu yonse ya anthu a mitundu ina ndi mafano wopanda pake,
    koma Yehova analenga kumwamba.
Ulemerero ndi ufumu zili pamaso pake;
    mphamvu ndi chimwemwe zili pa malo pokhala Iye.
Perekani kwa Yehova, Inu mabanja a anthu a mitundu ina,
    perekani kwa Yehova ulemerero ndi mphamvu,
    perekani kwa Yehova ulemerero woyenera dzina lake.
Bweretsani chopereka ndipo mufike pamaso pake;
    pembedzani Yehova mu ulemerero wachiyero chake.
Njenjemerani pamaso pake, dziko lonse lapansi!
    Dziko linakhazikika kolimba; silingasunthidwe.
Zakumwamba zisangalale, dziko lapansi likondwere;
    anene anthu a mitundu ina, “Yehova ndi mfumu!”