Daily Manna for Wednesday, October 9, 2019

Daily Manna is a daily Bible devotional service provided by Biblica. The Scripture is provided in many forms and is new every day. It is a great way to receive the encouragement and hope found in the Word of God.

Verse of the Day

Aefeso 4:17-23

Tsono ine ndikukuwuzani izi, ndipo ndikunenetsa mwa Ambuye, kuti musayendenso monga amachitira anthu a mitundu ina potsata maganizo awo opanda pake. Maganizo awo ndi odetsedwa, ndi osiyanitsidwa ndi moyo wa Mulungu chifukwa cha umbuli umene uli mwa iwo chifukwa cha kuwuma mtima kwawo. Popeza sazindikiranso kanthu kalikonse, adzipereka okha kuti akhumbe zonyansa, kuti achite mtundu uliwonse wa zoyipa ndi zilakolako zosatha.

Koma inu simunadziwe Khristu mʼnjira yotere. Zoonadi munamva za Iye ndipo munaphunzitsidwa mwa Iye molingana ndi choonadi chimene chili mwa Yesu. Inu munaphunzitsidwa molingana ndi moyo wanu wakale, kuchotsa umunthu wakale, umene ukupitirira kuwonongeka ndi zilakolako zachinyengo; kuti mukonzedwe mwatsopano mʼmitima mwanu;