Daily Manna for Wednesday, September 11, 2019

Daily Manna is a daily Bible devotional service provided by Biblica. The Scripture is provided in many forms and is new every day. It is a great way to receive the encouragement and hope found in the Word of God.

Verse of the Day

Miyambo 1:7-19

Kuopa Yehova ndiye chiyambi cha nzeru.
    Zitsiru zimanyoza nzeru ndi malangizo.

Mwana wanga, mvera malangizo a abambo ako
    ndipo usakane mawu okuwongolera a amayi ako.
Ali ngati sangamutu yokongola ya maluwa pamutu pako
    ndiponso ali ngati mkanda mʼkhosi mwako.

Mwana wanga, ngati anthu oyipa afuna kukukopa
    usamawamvere.
Akadzati, “Tiye kuno;
    tikabisale kuti tiphe anthu,
    tikabisalire anthu osalakwa;
tiwameze amoyo ngati manda,
    ndi athunthu ngati anthu otsikira mʼdzenje.
Motero tidzapeza zinthu zosiyanasiyana zamtengowapatali
    ndi kudzaza nyumba zathu ndi zolanda;
Bwera, chita nafe maere,
    ndipo tidzagawana chuma chathu tonse.”
Mwana wanga, usayende nawo pamodzi,
    usatsagane nawo mʼnjira zawozo.
Iwowatu amangofuna zoyipa zokhazokha,
    amathamangira kukhetsa magazi.
Nʼkopanda phindu kutchera msampha
    mbalame zikuona!
Koma anthu amenewa amangobisalira miyoyo yawo yomwe;
    amangodzitchera okha msampha!
Awa ndiwo mathero a anthu opeza chuma mwankhanza;
    chumacho chimapha mwiniwake.