2 Kungaboken 24 – NUB & CCL

Swedish Contemporary Bible

2 Kungaboken 24:1-20

1Under kung Jojakims regering anföll kung Nebukadnessar från Babylonien. Jojakim fick underkasta sig honom i tre år, men sedan gjorde han uppror. 2Herren skickade då rövarband från kaldéerna, araméerna, moabiterna och ammoniterna mot Juda för att krossa det, precis som han förutsagt genom sina tjänare profeterna. 3Dessa olyckor drabbade Juda på Herrens direkta befallning. Han ville fördriva dem på grund av Manasses synder och allt han gjort 4och utgjutit oskyldigt blod, så mycket att han hade fyllt Jerusalem med det oskyldiga blodet. Herren ville inte förlåta detta.

5Jojakims historia i övrigt, vad han gjorde, finns nedtecknat i Juda kungars krönika.

Jojakin regerar i Juda

(2 Krön 36:9-10)

6När Jojakim dog och gick till vila hos sina förfäder, blev hans son Jojakin kung efter honom. 7Den egyptiske kungen kom inte tillbaka mer från sitt land, för kungen i Babylonien hade intagit det område som tillhört Egypten, från Egyptens gränsflod till floden Eufrat.

8Jojakin var arton år när han blev kung, och han regerade i tre månader i Jerusalem. Hans mor hette Nechushta och var dotter till Elnatan från Jerusalem. 9Han gjorde det som var ont i Herrens ögon, precis som hans far hade gjort.

10Vid denna tid drog den babyloniske kungen Nebukadnessars arméer mot Jerusalem och belägrade staden. 11Nebukadnessar kom själv dit medan hans trupper belägrade staden. 12Kung Jojakin av Juda, hans mor, alla hans ämbetsmän och hovmän kapitulerade för honom. Kungen av Babylonien tillfångatog Jojakin i sitt åttonde regeringsår.

13Nebukadnessar förde bort alla skatter från Herrens tempel och det kungliga palatsets skattkammare, och alla guldföremål som Israels kung Salomo hade låtit tillverka för Herrens hus, allt i enlighet med vad Herren tidigare sagt. 14Nebukadnessar förde bort hela Jerusalem till exilen: alla officerare och krigare, hantverkare och smeder, sammanlagt 10 000 fångar. Det var bara de fattigaste som blev kvar i landet. 15Nebukadnessar förde bort Jojakin, kungens mor, hans hustrur, ämbetsmännen och de mäktiga i landet från Jerusalem till Babylon. 16Soldaterna som fördes bort var 7 000 till antalet, alla krigsdugliga, och hantverkarna och smederna uppgick till 1 000. Den babyloniske kungen förde dem med sig i fångenskap till Babylon. 17Han utsåg kung Jojakins farbror Mattanja till ny kung, och han ändrade hans namn till Sidkia.

Sidkia regerar i Juda

(2 Krön 36:11-14; Jer 52:1-3)

18Sidkia var tjugoett år gammal när han blev kung, och han regerade elva år i Jerusalem. Hans mor hette Hamutal och var dotter till Jeremia från Livna. 19Han gjorde det som var ont i Herrens ögon, precis som Jojakim hade gjort.

20Herren förkastade till sist i sin vrede både Jerusalem och Juda.

Jerusalem erövras av Nebukadnessar

(2 Krön 36:15-20; Jer 39:1-10; 52:4-27)

Men Sidkia gjorde uppror mot kungen i Babylonien.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Mafumu 24:1-20

1Pa nthawi ya ulamuliro wa Yehoyakimu, Nebukadinezara mfumu ya Babuloni anadzathira nkhondo dzikolo ndipo Yehoyakimu anakhala pansi pa ulamuliro wake zaka zitatu. Koma kenaka anasintha maganizo ake nawukira Nebukadinezara. 2Yehova anatumiza magulu a Ababuloni, Aaramu, Amowabu ndi Aamoni, kudzathira nkhondo Yuda. Iye anawatumiza kudzawononga Yuda molingana ndi mawu amene Yehova ananeneratu kudzera mwa aneneri ake. 3Ndithu, izi zinachitikira Yuda monga momwe Yehova analamulira nʼcholinga choti awachotse pamaso pake chifukwa cha machimo a Manase ndi zonse zimene anachita, 4kuphatikizapo kukhetsa magazi a anthu osalakwa. Chifukwa iye anadzaza Yerusalemu ndi magazi a anthu osalakwa ndipo Yehova sanafune kumukhululukira.

5Ntchito zina za Yehoyakimu ndi zonse zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda? 6Yehoyakimu anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda pamodzi ndi makolo ake. Ndipo Yehoyakini mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.

7Mfumu ya Igupto sinatulukenso mʼdziko lake chifukwa mfumu ya Babuloni inalanda mayiko onse kuchokera ku Mtsinje wa ku Igupto mpaka ku Mtsinje wa Yufurate.

Yoyakini Mfumu ya Yuda

8Yehoyakini anakhala mfumu ali ndi zaka 18 ndipo analamulira mu Yerusalemu miyezi itatu. Amayi ake anali Nehusita mwana wa Elinatani wa ku Yerusalemu. 9Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova monga anachitira abambo ake.

10Nthawi imeneyo ankhondo a Nebukadinezara mfumu ya Babuloni anabwera ku Yerusalemu nazinga mzindawo ndi misasa ya nkhondo 11ndipo Nebukadinezara anafika ku mzindawo pamene ankhondo ake anawuzinga. 12Yehoyakini mfumu ya Yuda pamodzi ndi amayi ake, atumiki ake, anthu ake olemekezeka ndiponso akuluakulu onse anadzipereka kwa mfumu ya ku Babuloni.

Mfumu ya Babuloni inagwira Yoyakini ukapolo mʼchaka chachisanu ndi chitatu cha ufumu wake. 13Monga ananenera Yehova, Nebukadinezara anachotsa chuma chonse cha mʼNyumba ya Yehova ndiponso cha mʼnyumba ya mfumu ndipo anatenga ziwiya zonse zagolide za ku Nyumba ya Yehova zimene Solomoni mfumu ya Israeli anapanga. 14Anatenga anthu onse a mu Yerusalemu kupita nawo ku ukapolo. Akuluakulu onse pamodzi ndi anthu ankhondo, anthu onse aluso ndi amisiri osula onse pamodzi analipo 10,000. Osauka okha ndiye anatsala mʼdzikomo.

15Nebukadinezara anatenga Yehoyakini ngati kapolo kupita naye ku Babuloni. Mu Yerusalemu anatenganso amayi a mfumu, akazi ake, akuluakulu ake ndiponso anthu olemekezeka mʼdzikomo. 16Mfumu ya Babuloni inatumizanso ku Babuloni anthu ankhondo 70,000, anthu amphamvu ndi okonzeka kupita ku nkhondo, anthu aluso ndi amisiri osula 1,000. 17Iye analonga ufumu Mataniya, malume wa Yoyakini mʼmalo mwake ndipo anasintha dzina lake kuti akhale Zedekiya.

Zedekiya Mfumu ya Yuda

18Zedekiya anakhala mfumu ali ndi zaka 21 ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka 11. Amayi ake anali Hamutali mwana wa Yeremiya wa ku Libina. 19Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova monga anachitira Yehoyakimu. 20Zonsezi zinachitikira Yerusalemu ndi Yuda chifukwa cha mkwiyo wa Mulungu ndipo pa mapeto pake anawachotsa pamaso pake.

Kuwonongeka kwa Yerusalemu

Ndipo Zedekiya anawukira mfumu ya Babuloni.