New International Version

Ecclesiastes 6

1I have seen another evil under the sun, and it weighs heavily on mankind: God gives some people wealth, possessions and honor, so that they lack nothing their hearts desire, but God does not grant them the ability to enjoy them, and strangers enjoy them instead. This is meaningless, a grievous evil.

A man may have a hundred children and live many years; yet no matter how long he lives, if he cannot enjoy his prosperity and does not receive proper burial, I say that a stillborn child is better off than he. It comes without meaning, it departs in darkness, and in darkness its name is shrouded. Though it never saw the sun or knew anything, it has more rest than does that man— even if he lives a thousand years twice over but fails to enjoy his prosperity. Do not all go to the same place?

Everyone’s toil is for their mouth,
    yet their appetite is never satisfied.
What advantage have the wise over fools?
What do the poor gain
    by knowing how to conduct themselves before others?
Better what the eye sees
    than the roving of the appetite.
This too is meaningless,
    a chasing after the wind.

10 Whatever exists has already been named,
    and what humanity is has been known;
no one can contend
    with someone who is stronger.
11 The more the words,
    the less the meaning,
    and how does that profit anyone?

12 For who knows what is good for a person in life, during the few and meaningless days they pass through like a shadow? Who can tell them what will happen under the sun after they are gone?

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mlaliki 6

1Ine ndinaona choyipa china pansi pano, ndipo chimasautsa anthu kwambiri: Mulungu amapereka chuma, zinthu ndi ulemu kwa munthu, kotero kuti munthuyo sasowa kanthu kalikonse kamene akukalakalaka, koma Mulungu samulola kuti adyerere zinthuzo, ndipo mʼmalo mwake amadyerera ndi mlendo. Izi ndi zopandapake, ndi zoyipa kwambiri.

Ngakhale munthu atabereka ana 100 ndi kukhala ndi moyo zaka zambiri; komatu ngakhale atakhala zaka zambiri chotani, ngati iye sangadyerere chuma chake ndi kuyikidwa mʼmanda mwaulemu, ine ndikuti mtayo umamuposa iyeyo. Mtayo umangopita pachabe ndipo umapita mu mdima, ndipo mu mdimamo dzina lake limayiwalika. Ngakhale kuti mtayowo sunaone dzuwa kapena kudziwa kanthu kalikonse, koma umapumula kuposa munthu uja, ngakhale munthuyo atakhala ndi moyo zaka 2,000, koma ndi kulephera kudyerera chuma chake. Kodi onsewa sapita malo amodzi?

Ntchito yonse ya munthu imathera pakamwa pake,
    komatu iye sakhutitsidwa ndi pangʼono pomwe.
Kodi munthu wanzeru
    amaposa motani chitsiru?
Kodi munthu wosauka amapindula chiyani
    podziwa kukhala bwino pamaso pa anthu ena?
Kuli bwino kumangoona zinthu ndi maso
    kusiyana ndi kumangozilakalaka mu mtima.
Izinso ndi zopandapake,
    nʼkungodzivuta chabe.

10 Chilichonse chimene chilipo anachitchula kale dzina,
    za mmene munthu alili nʼzodziwika;
sangathe kutsutsana ndi munthu
    amene ali wamphamvu kupambana iyeyo.
11 Mawu akachuluka
    zopandapake zimachulukanso,
    nanga munthu zimamupindulira chiyani?

12 Pakuti ndani amene amadziwa chomwe ndi chabwino pa moyo wa munthu, pakuti moyo wake ndi wa masiku ochepa ndi opandapake, umangopitira ngati mthunzi. Ndani amene angamufotokozere zimene zidzachitika pansi pano iye atapita?