2 Kings 17 – NIV & CCL

New International Version

2 Kings 17:1-41

Hoshea Last King of Israel

1In the twelfth year of Ahaz king of Judah, Hoshea son of Elah became king of Israel in Samaria, and he reigned nine years. 2He did evil in the eyes of the Lord, but not like the kings of Israel who preceded him.

3Shalmaneser king of Assyria came up to attack Hoshea, who had been Shalmaneser’s vassal and had paid him tribute. 4But the king of Assyria discovered that Hoshea was a traitor, for he had sent envoys to So17:4 So is probably an abbreviation for Osorkon. king of Egypt, and he no longer paid tribute to the king of Assyria, as he had done year by year. Therefore Shalmaneser seized him and put him in prison. 5The king of Assyria invaded the entire land, marched against Samaria and laid siege to it for three years. 6In the ninth year of Hoshea, the king of Assyria captured Samaria and deported the Israelites to Assyria. He settled them in Halah, in Gozan on the Habor River and in the towns of the Medes.

Israel Exiled Because of Sin

7All this took place because the Israelites had sinned against the Lord their God, who had brought them up out of Egypt from under the power of Pharaoh king of Egypt. They worshiped other gods 8and followed the practices of the nations the Lord had driven out before them, as well as the practices that the kings of Israel had introduced. 9The Israelites secretly did things against the Lord their God that were not right. From watchtower to fortified city they built themselves high places in all their towns. 10They set up sacred stones and Asherah poles on every high hill and under every spreading tree. 11At every high place they burned incense, as the nations whom the Lord had driven out before them had done. They did wicked things that aroused the Lord’s anger. 12They worshiped idols, though the Lord had said, “You shall not do this.”17:12 Exodus 20:4,5 13The Lord warned Israel and Judah through all his prophets and seers: “Turn from your evil ways. Observe my commands and decrees, in accordance with the entire Law that I commanded your ancestors to obey and that I delivered to you through my servants the prophets.”

14But they would not listen and were as stiff-necked as their ancestors, who did not trust in the Lord their God. 15They rejected his decrees and the covenant he had made with their ancestors and the statutes he had warned them to keep. They followed worthless idols and themselves became worthless. They imitated the nations around them although the Lord had ordered them, “Do not do as they do.”

16They forsook all the commands of the Lord their God and made for themselves two idols cast in the shape of calves, and an Asherah pole. They bowed down to all the starry hosts, and they worshiped Baal. 17They sacrificed their sons and daughters in the fire. They practiced divination and sought omens and sold themselves to do evil in the eyes of the Lord, arousing his anger.

18So the Lord was very angry with Israel and removed them from his presence. Only the tribe of Judah was left, 19and even Judah did not keep the commands of the Lord their God. They followed the practices Israel had introduced. 20Therefore the Lord rejected all the people of Israel; he afflicted them and gave them into the hands of plunderers, until he thrust them from his presence.

21When he tore Israel away from the house of David, they made Jeroboam son of Nebat their king. Jeroboam enticed Israel away from following the Lord and caused them to commit a great sin. 22The Israelites persisted in all the sins of Jeroboam and did not turn away from them 23until the Lord removed them from his presence, as he had warned through all his servants the prophets. So the people of Israel were taken from their homeland into exile in Assyria, and they are still there.

Samaria Resettled

24The king of Assyria brought people from Babylon, Kuthah, Avva, Hamath and Sepharvaim and settled them in the towns of Samaria to replace the Israelites. They took over Samaria and lived in its towns. 25When they first lived there, they did not worship the Lord; so he sent lions among them and they killed some of the people. 26It was reported to the king of Assyria: “The people you deported and resettled in the towns of Samaria do not know what the god of that country requires. He has sent lions among them, which are killing them off, because the people do not know what he requires.”

27Then the king of Assyria gave this order: “Have one of the priests you took captive from Samaria go back to live there and teach the people what the god of the land requires.” 28So one of the priests who had been exiled from Samaria came to live in Bethel and taught them how to worship the Lord.

29Nevertheless, each national group made its own gods in the several towns where they settled, and set them up in the shrines the people of Samaria had made at the high places. 30The people from Babylon made Sukkoth Benoth, those from Kuthah made Nergal, and those from Hamath made Ashima; 31the Avvites made Nibhaz and Tartak, and the Sepharvites burned their children in the fire as sacrifices to Adrammelek and Anammelek, the gods of Sepharvaim. 32They worshiped the Lord, but they also appointed all sorts of their own people to officiate for them as priests in the shrines at the high places. 33They worshiped the Lord, but they also served their own gods in accordance with the customs of the nations from which they had been brought.

34To this day they persist in their former practices. They neither worship the Lord nor adhere to the decrees and regulations, the laws and commands that the Lord gave the descendants of Jacob, whom he named Israel. 35When the Lord made a covenant with the Israelites, he commanded them: “Do not worship any other gods or bow down to them, serve them or sacrifice to them. 36But the Lord, who brought you up out of Egypt with mighty power and outstretched arm, is the one you must worship. To him you shall bow down and to him offer sacrifices. 37You must always be careful to keep the decrees and regulations, the laws and commands he wrote for you. Do not worship other gods. 38Do not forget the covenant I have made with you, and do not worship other gods. 39Rather, worship the Lord your God; it is he who will deliver you from the hand of all your enemies.”

40They would not listen, however, but persisted in their former practices. 41Even while these people were worshiping the Lord, they were serving their idols. To this day their children and grandchildren continue to do as their ancestors did.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Mafumu 17:1-41

Hoseya Mfumu Yotsiriza ya Israeli

1Mʼchaka cha 12 cha Ahazi mfumu ya Yuda, Hoseya mwana wa Ela anakhala mfumu ya Israeli mu Samariya ndipo analamulira zaka zisanu ndi zinayi. 2Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova, koma osafanana ndi mafumu a Israeli amene ankalamulira iye asanalowe ufumuwo.

3Salimenezeri mfumu ya ku Asiriya anabwera kudzathira nkhondo Hoseya amene anali pansi pa ulamuliro wake ndipo ankapereka msonkho kwa iyeyo. 4Koma mfumu ya ku Asiriya inazindikira kuti Hoseya akuwukira, pakuti Hoseyayo anali atatumiza nthumwi kwa So mfumu ya Igupto ndiponso analeka kukhoma msonkho kwa mfumu ya ku Asiriya, monga ankachitira chaka ndi chaka. Choncho Salimenezeri anagwira Hoseya ndi kumuyika mʼndende. 5Mfumu ya ku Asiriya inapita kukathira nkhondo dziko lonse la Israeli ndipo inapita mpaka ku Samariya ndipo inazinga mzindawo kwa zaka zitatu. 6Mʼchaka chachisanu ndi chinayi cha Hoseya, mfumu ya ku Asiriya inalanda Samariya ndipo inatenga Aisraeli ndi kupita nawo ku Asiriya. Anakawakhazika ku Hala ndi Habori mʼmbali mwa mtsinje wa Gozani ndi mʼmizinda ya Amedi.

Israeli Apita ku Ukapolo chifukwa cha Tchimo

7Zonsezi zinachitika chifukwa Aisraeli anachimwira Yehova Mulungu wawo, amene anawatulutsa mʼdziko la Igupto pansi pa ulamuliro wa Farao mfumu ya Igupto. Iwo ankapembedza milungu ina, 8ndiponso ankatsatira miyambo ya anthu a mitundu imene Yehova anayichotsa pamene iwo ankafika mʼdzikomo pamodzinso ndi miyambo yonse imene mafumu a Israeli anayambitsa. 9Ndipo Aisraeli ankachita zoyipa mwamseri kutsutsana ndi Yehova Mulungu wawo. Kuchokera ku nsanja ya alonda mpaka ku mzinda wotetezedwa, mʼmizinda yawo yonse anamangamo malo opembedzeramo mafano. 10Anayimika miyala ya chipembedzo ndi mitengo ya mafano a Asera pa phiri lililonse lalitali ndi pansi pa mtengo uliwonse wa masamba ambiri. 11Pa malo aliwonse opembedzera mafano, anthuwa ankafukiza lubani monga momwe ankachitira anthu a mitundu imene Yehova anayichotsa pamene iwo ankafika. Iwo anachita zinthu zoyipa zomwe zinaputa mkwiyo wa Yehova. 12Ndipo iwowo ankapembedza mafano ngakhale Yehova ananena kuti, “Musadzachite zimenezi.” 13Yehova anachenjeza Israeli ndi Yuda kudzera mwa aneneri ake onse ndi alosi kuti, “Lekani mchitidwe wanu woyipawo. Mverani malamulo anga ndi malangizo anga potsatira zonse zolembedwa mʼmalamulo a Mose, zimene ndinalamulira makolo anu kuti azimvere, kudzera mwa aneneri, atumiki anga.”

14Koma anthuwa sanamvere ndipo anawumitsa khosi ngati momwe analili makolo awo, amene sanadalire Yehova Mulungu wawo. 15Anakana malangizo ake ndi pangano anachita ndi makolo awo ndipo ananyoza zochenjeza za Yehova. Iwo anatsatira mafano achabechabe nasanduka achabechabe. Anthuwa anatsanzira mitundu ya anthu owazungulira ngakhale kuti Yehova anawalamula kuti, “Musamachite zomwe iwo amachita,” koma iwo anachita zomwe Yehova anawaletsa.

16Iwowo anasiya malamulo onse a Yehova Mulungu wawo, nadzipangira mafano awiri osungunula a ana angʼombe ndiponso fano la Asera, napembedza zonse zamlengalenga ndi kutumikira Baala. 17Ndipo anadutsitsa mʼmoto ana awo aamuna ndi aakazi. Iwo ankawombeza mawula, namachitanso zanyanga ndipo anadzipereka kuchita zoyipa pamaso pa Yehova namukwiyitsa.

18Choncho Yehova anakwiya nawo kwambiri Aisraeli ndipo anawachotsa pamaso pake. Palibe amene anatsala kupatula fuko la Yuda lokha. 19Yuda nayenso sanasunge malamulo a Yehova Mulungu wawo. Iwo ankatsatira machitidwe amene Israeli anayambitsa. 20Motero Yehova anakana Aisraeli onse. Iye anawazunza nawapereka mʼmanja mwa anthu ofunkha mpaka Iye atawachotseratu pamaso pake.

21Yehova atangʼamba Israeli kumuchotsa ku nyumba ya Davide, Aisraeliwo anasankha Yeroboamu mwana wa Nebati kukhala mfumu yawo. Yeroboamu ananyengerera Aisraeli kuti asatsatire Yehova ndipo anawachimwitsa tchimo lalikulu. 22Aisraeli anakakamira machimo onse amene Yeroboamu anachita ndipo sanawasiye 23mpaka pamene Yehova anawachotsa pamaso pake monga anawachenjezera kudzera mwa atumiki ake onse, aneneri. Choncho Aisraeli anachotsedwa mʼdziko lawo kupita ku ukapolo ku Asiriya ndipo ali komweko mpaka lero lino.

Anthu Achilendo Akhala mu Samariya

24Mfumu ya ku Asiriya inabweretsa anthu a ku Babuloni, Kuta, Awa, Hamati ndi a ku Sefaravaimu kudzawakhazika mʼmizinda ya Samariya kulowa mʼmalo mwa Aisraeli. Iwo anatenga Samariya ndi kukhala mʼmizinda yake. 25Iwo atayamba kukhala kumeneko, sanapembedze Yehova choncho Yehova anatumiza mikango pakati pawo ndipo inapha ena mwa iwo. 26Tsono mfumu ya ku Asiriya inawuzidwa za nkhaniyi kuti, “Anthu amene munawatumiza ndi kuwakhazika mʼmizinda ya Samariya sakudziwa chimene Mulungu wa dzikolo amafuna. Choncho Iye watumiza mikango pakati pawo imene ikuwapha chifukwa anthuwo sadziwa chimene Mulungu wa dzikolo amafuna.”

27Tsono mfumu ya ku Asiriya inalamula kuti, “Tengani wansembe mmodzi mwa amene munawagwira ukapolo, mupite naye kumeneko ndipo akakhale komweko nakaphunzitse anthu zimene Mulungu wa dzikolo amafuna.” 28Choncho mmodzi mwa ansembe amene anawatenga ku Samariya anabwera kudzakhala ku Beteli ndipo ankaphunzitsa anthuwo kupembedza Yehova.

29Koma mtundu uliwonse wa anthu unkapangabe mafano a milungu yawoyawo mʼmizinda yambiri imene anthuwo ankakhala, ndipo anayika milunguyo mʼnyumba za milungu zimene anthu a ku Samariya anamanga ku malo opembedzera mafano. 30Anthu a ku Babuloni anapanga Sukoti-Benoti, anthu a ku Kuti anapanga Nerigali, ndipo anthu a ku Hamati anapanga Asima; 31Aava anapanga Nibihazi ndi Taritaki, ndipo Asefaravaimu ankawotcha ana awo pa moto ngati nsembe kwa Adirameleki ndi Anameleki, milungu ya Asefaravaimu. 32Iwo ankapembedza Yehova, koma ankadzisankhira okha pakati pawo anthu wamba kuti akhale ansembe awo ku nyumba za milungu za ku malo opembedzera mafano. 33Iwowo ankapembedza Yehova, komanso ankatumikira milungu yawo molingana ndi miyambo ya mitundu ya kumene ankachokera.

34Mpaka lero lino iwo akupitirizabe kuchita zimene ankachita poyamba. Sapembedza Yehova kapenanso kutsata malangizo ake ndi malamulo ake, chiphunzitso chake monga mwa malamulo amene Yehova anawapereka kwa zidzukulu za Yakobo, amene anamutcha Israeli. 35Pamene Yehova anachita pangano ndi Aisraeli, Iye anawalamula kuti, “Musapembedze milungu ina kapena kuyigwadira iyo, kuyitumikira kapena kupereka nsembe kwa iyoyo. 36Koma Yehova amene anakutulutsani mʼdziko la Igupto ndi dzanja lake lamphamvu ndiye amene muyenera kumupembedza. 37Muyenera kusamalitsa nthawi zonse kusunga malangizo anga ndi malemba anga, chiphunzitso ndi malamulo amene anakulemberani. Musapembedze milungu ina. 38Musayiwale pangano limene ndinapangana nanu ndipo musamapembedze milungu ina. 39Mʼmalo mwake muzipembedza Yehova Mulungu wanu pakuti ndiye amene adzakulanditsani mʼdzanja la adani anu onse.”

40Komabe iwo sanamvere ndipo anapitiriza kuchita zomwe ankachita kale. 41Ngakhale anthuwo ankapembedza Yehova, ankatumikiranso mafano awo. Mpaka lero lino ana awo ndi zidzukulu zawo zikupitiriza kuchita zomwe ankachita makolo awo.