Kukomboa Kile Kilicho Cha Bwana
1Bwana akamwambia Mose, 227:2 Mwa 28:20; Hes 6:2; Kum 23:21-23; Amu 11:30-39; Ay 22:27; Yn 1:16; Mdo 21:23“Sema na Waisraeli uwaambie: ‘Kama mtu yeyote ataweka nadhiri maalum ili kuweka watu wakfu kwa Bwana, kwa kutoa kiasi cha thamani inayolingana, 327:3 Kut 30:13; Hes 3:47; 18:16; Eze 45:12thamani ya kukomboa mwanaume mwenye kati ya umri wa miaka ishirini na miaka sitini itakuwa shekeli hamsini27:3 Shekeli 50 za fedha ni sawa na gramu 600. za fedha, kulingana na shekeli ya mahali patakatifu; 4ikiwa ni mwanamke, weka thamani yake kwa shekeli thelathini.27:4 Shekeli 30 za fedha ni sawa na gramu 360. 527:5 Mwa 37:28Kama ni mtu mwenye umri wa miaka kati ya mitano na ishirini, weka thamani ya mwanaume kuwa shekeli ishirini,27:5 Shekeli 20 za fedha ni sawa na gramu 240. na mwanamke shekeli kumi.27:5 Shekeli 10 za fedha ni sawa na gramu 120. 627:6 Hes 3:47; 18:16Kama ni mtu mwenye umri kati ya mwezi mmoja na miaka mitano, weka thamani ya mwanaume kuwa shekeli tano za fedha, na ile ya mwanamke kuwa shekeli tatu27:6 Shekeli tatu za fedha ni sawa na gramu 36. za fedha. 7Kama ni mtu mwenye miaka sitini na zaidi, weka thamani ya mwanaume kuwa shekeli kumi na tano,27:7 Shekeli 15 za fedha ni sawa na gramu 180. na mwanamke shekeli kumi. 827:8 Law 5:11; 12:8; 14:21-22; Lk 21:1; 2Kor 8:12Kama mtu yeyote anayeweka nadhiri ni maskini mno kuweza kulipa kiasi kilichowekwa, atampeleka huyo mtu kwa kuhani, ambaye ataweka thamani yake kulingana na kile mweka nadhiri anachoweza kulipa.
927:9 Mwa 28:20; Kut 40:9; Hes 6:20; 18:17; Kum 15:19“ ‘Kama kile mtu alichokiwekea nadhiri ni mnyama anayekubalika kama sadaka kwa Bwana, mnyama wa namna hiyo aliyetolewa kwa Bwana anakuwa mtakatifu. 10Mtu haruhusiwi kumbadilisha au kutoa mnyama mzuri kwa mbaya, au mnyama mbaya kwa mzuri. Kama atatoa mnyama badala ya mwingine, wanyama wote wawili, yaani yule aliyetolewa na yule aliyebadiliwa, ni watakatifu. 1127:11 Kut 13:13; Hes 18:15Kama alichokiwekea nadhiri ni mnyama aliye najisi kiibada, yaani yule asiye kubalika kuwa sadaka kwa Bwana, huyo mnyama lazima aletwe kwa kuhani, 12ambaye ataamua ubora wa mnyama huyo, kama ni mzuri au mbaya. Thamani yoyote atakayoweka kuhani, hivyo ndivyo itakavyokuwa. 1327:13 Law 25:25; 5:16Kama mwenye mnyama atapenda kumkomboa mnyama huyo, lazima aongeze sehemu ya tano ya thamani yake.
1427:14 Law 25:29-31; Hes 18:14; 2Kor 9:10“ ‘Kama mtu ataweka nyumba yake wakfu kama kitu kitakatifu kwa Bwana, kuhani ataamua ubora wa nyumba hiyo, kama ni nzuri au mbaya. Thamani yoyote kuhani atakayoweka, basi hivyo ndivyo itakavyokuwa. 15Kama mtu aliyeweka nyumba yake wakfu ataikomboa, lazima aongeze sehemu ya tano ya thamani yake, nayo nyumba itakuwa yake tena.
16“ ‘Kama mtu anaweka sehemu ya ardhi ya jamaa yake wakfu kwa Bwana, thamani yake itawekwa kulingana na kiasi cha mbegu inayohitajiwa kupandwa katika ardhi hiyo, yaani homeri27:16 Homeri moja ni sawa na efa 10, ambazo ni sawa na kilo 100. moja ya mbegu za shayiri kwa shekeli hamsini za fedha. 17Kama akiweka shamba lake wakfu katika Mwaka wa Yubile, ile thamani iliyokwisha wekwa itakuwa iyo hiyo. 1827:18 Law 25:10-15; 25:15-16Lakini kama akiweka shamba lake wakfu baada ya Yubile, kuhani ataweka thamani kulingana na idadi ya miaka iliyobaki kufikia Mwaka wa Yubile unaofuata, na thamani yake iliyoamuliwa itapunguzwa. 1927:19 Law 25:25Kama mtu anayeweka wakfu shamba anataka kulikomboa, lazima aongeze sehemu ya tano ya thamani yake, nalo shamba litakuwa lake tena. 20Kama pengine halikomboi shamba hilo, au kama ameliuza kwa mtu mwingine, kamwe haliwezi kukombolewa. 2127:21 Law 25:10; Hes 18:14; Eze 44:29Shamba hilo litakapoachiwa mwaka wa Yubile, litakuwa takatifu, kama shamba lililotolewa kwa Bwana, nalo litakuwa mali ya makuhani.
22“ ‘Kama mtu ameweka wakfu kwa Bwana shamba alilonunua, ambalo si sehemu ya ardhi ya jamaa yake, 2327:23 Law 25:15kuhani ataamua thamani yake hadi Mwaka wa Yubile, naye huyo mtu atalazimika kulipa thamani yake siku hiyo kama kitu kitakatifu kwa Bwana. 2427:24 Law 25:28Katika Mwaka wa Yubile, shamba litarudishwa kwa mtu yule ambaye lilinunuliwa kutoka kwake, yule ambaye ardhi ilikuwa mali yake. 2527:25 Kut 30:13; Hes 3:47; Eze 45:12; Hes 18:16Kila thamani lazima iwekwe kulingana na shekeli ya mahali patakatifu,27:25 Shekeli moja ya mahali patakatifu ni sawa na gramu 11. gera ishirini kwa shekeli.
2627:26 Kut 13:12; 22:30; Hes 18:17; Kut 15:19“ ‘Lakini hakuna mtu atakayeweka wakfu mzaliwa wa kwanza wa mnyama, kwa kuwa mzaliwa wa kwanza tayari ni mali ya Bwana; awe ngʼombe au kondoo, ni wa Bwana. 27Kama ni mmoja wa wanyama walio najisi, aweza kumnunua kwa bei iliyowekwa, akiongeza sehemu ya tano ya thamani yake. Kama hatamkomboa, mnyama huyo atauzwa kwa bei iliyowekwa.
2827:28 Hes 18:14; Yos 6:17-19; Amu 11:30-31“ ‘Lakini chochote kile mtu alicho nacho na akakiweka wakfu27:28 Akakiweka wakfu ina maana ya kumpa Mungu kabisa, daima, bila kurudiwa. kwa Bwana, iwe ni binadamu, au mnyama, au ardhi ya jamaa, hakiwezi kuuzwa au kukombolewa. Chochote kilichowekwa wakfu ni kitakatifu sana kwa Bwana.
2927:29 Kum 7:26“ ‘Mtu yeyote aliyewekwa wakfu ili kuangamizwa, hawezi kukombolewa. Mtu kama huyo lazima auawe.
3027:30 Hes 18:26; Kum 7:6; 12:6, 17; 14:22-28; 2Nya 31:6; Neh 10:37; 12:44; 13:5; Mal 3:8; Ezr 9:2; Isa 6:13“ ‘Zaka ya kila kitu kutoka shambani, iwe ni nafaka kutoka kwa ardhi, au tunda kutoka kwa miti, ni mali ya Bwana; ni takatifu kwa Bwana. 3127:31 Law 25:25; 5:16Kama mtu akikomboa chochote cha zaka yake, lazima aongeze sehemu ya tano ya thamani yake. 3227:32 Za 89:32; Yer 33:13; Eze 20:37; Mik 7:14Zaka yote ya kundi la ngʼombe au la kondoo na mbuzi, kila mnyama wa kumi apitaye chini ya fimbo ya yule awachungaye, atakuwa mtakatifu kwa Bwana. 3327:33 Hes 18:21Yule mnyama wa kumi hatachaguliwa kwa kigezo cha uzuri au ubaya, naye haruhusiwi kubadiliwa. Ikiwa atabadiliwa, basi mnyama yule wa kwanza na huyo aliyebadiliwa wote watahesabiwa kuwa watakatifu, na haiwezekani kuwakomboa.’ ”
3427:34 Kut 19:11; Law 7:38; Kum 4:5; Mdo 7:38Haya ndiyo maagizo Bwana aliyompa Mose juu ya Mlima Sinai kwa ajili ya Waisraeli.
Kuwombola Zomwe ndi za Yehova
1Yehova anawuza Mose kuti, 2“Yankhula ndi Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Ngati munthu anachita lumbiro lapadera loti adzapereka munthu mnzake kwa Yehova ndipo akufuna kuti amuwombole, 3mtengo wake ukhale masekeli a siliva makumi asanu, molingana ndi kawerengedwe ka ku Nyumba ya Mulungu, ngati munthuyo ndi wamwamuna wa zaka zapakati pa 20 ndi 60. 4Ndipo ngati ndi wamkazi, mtengo wake ukhale masekeli makumi atatu. 5Mtengo wa munthu wamwamuna wa zaka zapakati pa zisanu ndi makumi awiri ukhale masekeli makumi awiri ndipo munthu wamkazi ukhale masekeli khumi. 6Ngati ndi munthu wamwamuna wa pakati pa mwezi umodzi ndi zaka zisanu, mtengo wa munthu wamwamuna ukhale masekeli asanu a siliva ndipo ngati ndi wamkazi, ukhale masekeli atatu a siliva. 7Ngati ndi munthu wa zaka makumi asanu ndi limodzi kapena kuposerapo, mtengo wa wamwamuna ukhale masekeli khumi ndi asanu, ndipo wamkazi ukhale masekeli khumi. 8Ngati munthu amene anachita lumbiro ndi wosauka kwambiri kuti sangathe kulipira ndalama zimenezo, abwere ndi munthu woperekedwa uja kwa wansembe, ndipo wansembeyo ayike mtengo woti munthu wolumbirayo angathe kulipira.
9“ ‘Ngati chimene anachitira lumbiro kuti apereke ndi nyama imene amapereka kukhala nsembe kwa Yehova, zonse zimene amapereka kwa Yehova nʼzopatulika. 10Munthu asasinthanitse ndi ina kapena kupereka ina yabwino mʼmalo mwa yoyipa, kapena yoyipa mʼmalo mwa yabwino. Ngati asinthitsa nyama ina mʼmalo mwa ina, nyamayo pamodzi ndi inzake wasinthitsayo zikhala zopatulika. 11Ngati chimene anachitira lumbiro ndi nyama yodetsedwa, nyama imene siloledwa kuyipereka kukhala nsembe kwa Yehova, nyamayo abwere nayo kwa wansembe, 12ndipo wansembeyo atchule mtengo wake poona ngati ndi yabwino kapena ndi yoyipa. Mtengo umene wansembe atchule ndiwo udzakhale mtengo wake. 13Ngati mwini wakeyo akufuna kuwombola nyamayo, awonjezere pa mtengo wake wa nyamayo chimodzi mwa zigawo zisanu zamtengowo.
14“ ‘Ngati munthu apereka nyumba yake kuti ikhale yopatulika kwa Yehova, wansembe atchule mtengo wake poona ngati ndi yabwino kapena ndi yoyipa. Mtengo umene wansembe atchule ndiwo udzakhale mtengo wake. 15Ngati munthu amene wapereka nyumbayo afuna kuyiwombola nyumbayo, awonjezere pamtengo wake wa nyumbayo, limodzi mwa magawo asanu amtengowo. Ndipo nyumbayo idzakhalanso yake.
16“ ‘Ngati munthu apereka kwa Yehova mbali ina ya malo a makolo ake, mtengo umene awuyike ukhale wolingana ndi mtengo wa mbewu zimene zimadzabzalidwamo. Zikhale mbewu za barele za makilogalamu makumi awiri ndipo mtengo wake ukhale masekeli makumi asanu. 17Ngati munthu apereka munda wake kuyambira chaka chokondwerera zaka makumi asanu, mtengo wake ukhale umene unakhazikitsidwa. 18Koma ngati apereka mundawo chaka chokondwerera zaka makumi asanu chitapita, wansembe adzatchula mtengo molingana ndi zaka zomwe zatsala kuti chifike chaka china chokondwerera zaka makumi asanu, ndipo mtengo wake udzakhala wotsikirapo. 19Ngati munthu amene wapereka munda afuna kuwuwombola, ayenera kuwonjezera pa mtengo wake wa mundawo, limodzi mwa magawo asanu a mtengowo. Ndipo mundawo udzakhalanso wake. 20Koma ngati sawuwombola mundawo, kapena ngati waugulitsa kwa munthu wina, mundawo sudzawomboledwanso. 21Mwini mundawo akawusiya mʼchaka chokondwerera zaka makumi asanu ndiye kuti mundawo udzakhala wopatulika monga woperekedwa kwa Yehova: udzakhala munda wa ansembe.
22“ ‘Ngati munthu apereka kwa Yehova munda umene anagula, umene si malo a makolo ake, 23wansembe atchule mtengo wake kufikira pa chaka chokondwerera zaka makumi asanu, ndipo munthuyo apereke ndalama zokwanira mtengo wake pa tsikulo monga ndalama zopatulika kwa Yehova. 24Pa chaka chokondwerera zaka makumi asanu, mundawo udzabwezedwa kwa munthu amene anawugulitsayo, amene malowo anali ake. 25Potchula mtengo uliwonse wansembe awerengere molingana ndi mtengo wa sekeli wa ku Nyumba ya Mulungu: magera makumi awiri pa sekeli imodzi.
26“ ‘Koma pasapezeke munthu wopereka mwana woyamba kubadwa wa nyama, popeza mwana woyamba kubadwa ali kale wa Yehova, kaya ndi ngʼombe kapena nkhosa, zimenezi ndi za Yehova. 27Ngati ili nyama yodetsedwa, ayiwombole pa mtengo umene wansembe wawuyika, ndi kuwonjezeranso pa mtengo wake wa nyamayo, limodzi mwa magawo asanu amtengowo. Ngati sayiwombola, igulitsidwe pa mtengo umene wansembe awuyike.
28“ ‘Koma chinthu chilichonse choperekedwa kwa Yehova, kaya ndi munthu, nyama, kaya ndi malo a makolo, chimenechi chisagulitsidwe kapena kuwomboledwa. Choperekedwa kwa Yehova motere nʼchopatulika kwambiri.
29“ ‘Munthu amene waperekedwa kotheratu sangawomboledwe. Munthuyo ayenera kuphedwa.
30“ ‘Chakhumi chilichonse chochokera mʼdziko, kaya ndi tirigu wochokera mʼnthaka kapena chipatso cha mʼmitengo ndi za Yehova. Chimenecho ndi chopatulika kwa Yehova. 31Ngati munthu afuna kuwombola chakhumi chilichonse, awonjezere pamtengo wake chimodzi mwa zigawo zisanu za mtengowo. 32Chakhumi cha ngʼombe ndi nkhosa, kapena kuti nyama iliyonse ya khumi imene mʼbusa wayiwerenga idzakhala yopatulikira kwa Yehova. 33Palibe amene adzaloledwa kusankha nyama yomwe ili yabwino kapena kusinthitsa. Ngati asinthitsa, nyamayo pamodzi ndi inzakeyo zidzakhala zopatulika ndipo sangaziwombole.’ ”
34Amenewa ndi malamulo amene Yehova anamupatsa Mose pa Phiri la Sinai kuti awuze Aisraeli.