Sadaka Ya Nafaka
12:1 Kut 29:2, 41; Law 6:14-18; 5:11; 7:12; 24:7; Hes 15:4; 28:5; Neh 13:9; Isa 43:23“ ‘Mtu yeyote aletapo sadaka ya nafaka kwa Bwana, sadaka yake itakuwa ya unga laini. Atamimina mafuta juu yake, aweke uvumba juu yake, 22:2 Law 1:9; 5:11, 12; 6:15; 24:7; Isa 1:13; 53:12; 65:3; 66:3; Hes 5:26; 18:8; Za 16:5; 73:26; Mdo 10:4naye atapeleka kwa makuhani wana wa Aroni. Kuhani atachukua konzi moja iliyojaa unga laini na mafuta pamoja na uvumba wote, na kuuteketeza kama sehemu ya kumbukumbu juu ya madhabahu, sadaka iliyotolewa kwa moto, harufu nzuri ya kumpendeza Bwana. 32:3 Law 6:16; 10:12-13; Kut 30:36; Hes 18:9Sadaka ya nafaka iliyobaki ni ya Aroni na wanawe, ni sehemu ya sadaka iliyo takatifu sana iliyotolewa kwa Bwana kwa moto.
42:4 Law 7:9, 12; 8:26; 26:26; Kut 29:2“ ‘Kama utaleta sadaka ya nafaka iliyookwa jikoni, itakuwa ya unga laini: maandazi yaliyotengenezwa bila kutiwa chachu, yaliyochanganywa na mafuta, au mikate myembamba iliyotengenezwa bila kutiwa chachu, na iliyopakwa mafuta. 52:5 Law 6:21; 7:9; Eze 4:3Iwapo sadaka yako ya nafaka imeandaliwa kwenye kikaango, itakuwa ni ya unga laini uliochanganywa na mafuta, bila chachu. 6Ukande na kumimina mafuta juu yake; hii ni sadaka ya nafaka. 72:7 Law 7:9Kama sadaka yako ya nafaka imepikwa kwenye sufuria, itatengenezwa kwa unga laini na mafuta. 8Ilete hiyo sadaka ya nafaka iliyotengenezwa kwa vitu hivi kwa Bwana; mkabidhi kuhani ambaye ataipeleka madhabahuni. 92:9 Mwa 8:21; Kut 29:18; Rum 12:1Naye atatoa ile sehemu ya kumbukumbu kutoka kwenye hiyo sadaka ya nafaka na kuiteketeza juu ya madhabahu kuwa sadaka iliyotolewa kwa moto, harufu nzuri ya kumpendeza Bwana. 102:10 Ezr 2:63; Kut 29:18, 37Sadaka ya nafaka iliyobaki ni ya Aroni na wanawe; ni sehemu ya sadaka iliyo takatifu sana ya sadaka iliyotolewa kwa Bwana kwa moto.
112:11 Kut 34:25; 23:18; Law 6:16; Mt 16:12; Mk 8:15; 1Kor 5:8; Gal 5:8-9“ ‘Kila sadaka ya nafaka unayoleta kwa Bwana ni lazima ifanywe bila kutiwa chachu, kwa kuwa huna ruhusa kuchoma chachu yoyote au asali katika sadaka itolewayo kwa Bwana kwa moto. 122:12 Kut 34:22; 22:29; Law 23:10-11; Kum 26:10Unaweza kuzileta kwa Bwana kama sadaka ya malimbuko, lakini haziwezi kutolewa juu ya madhabahu kama harufu nzuri ya kupendeza. 132:13 Mk 9:49; Hes 18:19; 2Nya 13:5; Eze 43:24; Kol 4:6Koleza sadaka zako zote za nafaka kwa chumvi. Usiache kuweka chumvi ya Agano la Mungu wako katika sadaka zako za nafaka; weka chumvi kwenye sadaka zako zote.
142:14 Kut 34:22; Hes 15:20; Kum 16:13; 26:2; Rut 3:2; Kut 23:19; Mit 3:9; 2Fal 4:42“ ‘Kama ukileta malimbuko ya sadaka ya nafaka kwa Bwana, utatoa masuke yaliyopondwa ya nafaka mpya iliyookwa kwa moto. 15Weka mafuta na uvumba juu yake; ni sadaka ya nafaka. 162:16 Hes 4:16; Yer 14:12Kuhani atateketeza ile sehemu ya kumbukumbu kutoka kwenye hiyo sadaka ya nafaka iliyopondwa kwa mafuta, pamoja na uvumba wote, kama sadaka iliyotolewa kwa Bwana kwa moto.
Nsembe Zachakudya
1“ ‘Munthu wina aliyense akabwera ndi nsembe ya chakudya kwa Yehova, chopereka chake chizikhala ufa wosalala. Ufawo ausakanize ndi mafuta ndi lubani, 2ndipo apite nawo kwa ansembe, ana a Aaroni. Atapeko modzazitsa dzanja ufa wosalala uja kuti ukhale wachikumbutso pamodzi ndi mafuta ndi lubani ndipo atenthe zonsezi pa guwa lansembe kuti zilandiridwe ndi Yehova mʼmalo mwa chopereka chonse. Iyi ndi nsembe yotentha pa moto ndiponso fungo lokomera Yehova. 3Zotsala za nsembe ya chakudyazo ndi za Aaroni pamodzi ndi ana ake. Chimenechi ndi chigawo chopatulika kwambiri chifukwa chatapidwa pa chopereka chotentha pa moto cha Yehova.
4“ ‘Ukabweretsa nsembe ya chakudya chophika mu uvuni, ikhale ya buledi wa ufa wosalala wopanda yisiti koma wosakaniza ndi mafuta, kapena timitanda ta buledi topyapyala, topanda yisiti koma topaka mafuta. 5Ngati nsembe yako yachakudya ndi yophika pa chitsulo chamoto, ikhale ya buledi wa ufa wosalala wopanda yisiti koma wosakaniza ndi mafuta. 6Umuduledule bulediyo ndi kumupaka mafuta; imeneyo ndi nsembe yachakudya. 7Ngati nsembe yako yachakudya ndi yophikidwa pa chiwaya, ikhale ya buledi wa ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta. 8Munthu azibwera ndi nsembe za chakudya zimene wapanga ndi zinthu zimenezi. Atachipereka kwa wansembe, iyeyu adzipita nacho ku guwa. 9Wansembeyo atengeko gawo lina la nsembeyo kukhala ufa wachikumbutso kuti ilandiridwe ndi Yehova mʼmalo mwa nsembe yonse ndipo ayitenthe pa moto monga nsembe yopsereza ya fungo lokomera Yehova. 10Zotsala za nsembe ya chakudyayo zikhale za Aaroni ndi ana ake. Chimenechi ndi chigawo chopatulika kwambiri chifukwa chatapidwa pa chopereka chotentha pa moto cha Yehova.
11“ ‘Nsembe ya chakudya chilichonse imene ubweretsa kwa Yehova ikhale yopanda yisiti, pakuti suyenera kupereka kwa Yehova nsembe yotentha pa moto imene ili ndi yisiti kapena uchi. 12Ziwirizi ungathe kubwera nazo kwa Yehova ngati chopereka cha zokolola zoyambirira. Koma usazitenthe pa guwa kuti zikhale fungo lokomera Yehova. 13Zopereka zako zonse zachakudya uzithire mchere. Usayiwale kuthira mchere pa chopereka chako popeza mcherewo ukusonyeza pangano pakati pa iwe ndi Mulungu wako. Tsono uzinthira mchere pa chopereka chako chilichonse.
14“ ‘Mukamapereka kwa Yehova chopereka cha chakudya choyamba kucha, choperekacho chikhale cha chipatso chatsopano chokazinga pa moto ndi chopunthapuntha. 15Uchithire mafuta ndi lubani pakuti ndi chopereka cha chakudya. 16Tsono wansembe atenthe gawo la chopereka chopunthapuntha chija kuti chikhala ufa wachikumbutso ndi cha mafuta pamodzi ndi lubani yense kuti Yehova alandire mʼmalo mwa zopereka zonse. Ichi ndi chopereka chotentha pa moto cha Yehova.