Jesaja 6 – HTB & CCL

Het Boek

Jesaja 6:1-13

1In het sterfjaar van koning Ozias aanschouwde ik den Heer, gezeten op een hoge en heerlijke troon; de sleep van zijn mantel bedekte heel de tempel. 2Serafs stonden om Hem heen, elk met zes vleugels; twee om het gelaat, twee om de voeten te bedekken, en twee om te vliegen. 3En ze riepen elkander toe: “Heilig, heilig, heilig is Jahweh der heirscharen; de hele aarde is vol van zijn glorie!” 4Van hun juichen trilden de drempels in hun voegen, en het hele huis stond vol rook. 5Ik riep uit: Wee mij, ik ben verloren! Want ik heb met mijn ogen den Koning, Jahweh der heirscharen, aanschouwd, ofschoon ik een mens ben met onreine lippen, en onder een volk met onreine lippen verblijf. 6Maar één der serafs vloog op mij af; met een gloeiende kool, die hij met een tang van het altaar had genomen, 7raakte hij mijn mond aan, en sprak: Zie, zij heeft uw lippen geraakt; nu is uw schuld verdwenen, uw zonde vergeven. 8Nu hoorde ik de stem van den Heer: Wien zal Ik zenden, en wie zal gaan uit onze naam? Ik zeide: Hier ben ik; zend mij! 9Toen sprak Hij: Ga heen, en zeg aan dit volk: Gij zult altijd weer horen, Maar nimmer verstaan; Scherp zult gij zien, Maar niet inzien. 10Verstomp het hart van dit volk, Verstop zijn oren, verblind zijn ogen: Opdat ze met hun ogen niet zien, Met hun oren niet horen, Met hun hart niet verstaan, Zich niet bekeren noch worden genezen. 11Ik zeide: Hoe lang zal dit duren, o Heer? Hij sprak: Tot de steden vernield zijn, En geen bewoners meer hebben; De huizen ontvolkt, Het land verwoest en verlaten; 12Tot Jahweh de mensen heeft weggevoerd, Op het land grote eenzaamheid ligt, 13En het tiende, dat restte, ook is verdelgd. Maar gelijk een stronk blijft staan, Waar terebint of eik zijn geveld, Zo blijft er een heilig zaad als zijn wortel!

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yesaya 6:1-13

Masomphenya a Yesaya

1Chaka chimene mfumu Uziya anamwalira, ndinaona Ambuye atakhala pa mpando waufumu, wautali ndi wokwezedwa, ndipo mkanjo wawo unali wautali; kotero kuti unadzaza mʼNyumba ya Yehova. 2Pamwamba pawo panayimirira Aserafi, aliyense anali ndi mapiko asanu ndi limodzi: awiri anaphimba nkhope zawo, awiri anaphimba mapazi awo, ndipo awiri ankawulukira. 3Ndipo Aserafiwo amafuwulirana kuti

“Woyera, woyera, woyera Yehova Wamphamvuzonse.

Dziko lonse lapansi ladzaza ndi ulemerero wake.”

4Chifukwa cha kufuwulako maziko a zitseko ndi ziwundo anagwedezeka ndipo mʼNyumba ya Yehova munadzaza utsi.

5Tsono ine ndinafuwula kuti, “Tsoka langa ine! Ndatayika! Pakuti ndine munthu wapakamwa poyipa, ndipo ndimakhala pakati pa anthu a pakamwa poyipa, ndipo ndi maso anga ndaona mfumu Yehova Wamphamvuzonse.”

6Pomwepo mmodzi mwa Aserafi aja anawulukira kwa ine ali ndi khala lamoto mʼdzanja lake, khala limene analichotsa ndi mbaniro pa guwa lansembe. 7Ndipo anandikhudza pakamwa panga ndi khala lamotolo nati, “Taona ndakhudza pa milomo yako ndi khalali; kulakwa kwako kwachotsedwa, machimo ako akhululukidwa.”

8Kenaka ndinamva mawu a Ambuye akuti, “Kodi ndidzatuma yani? Ndipo ndani adzapite mʼmalo mwathu?”

Ndipo ine ndinati, “Ndilipo. Tumeni!”

9Yehova anati, “Pita ndipo ukawawuze anthu awa:

“ ‘Kumva muzimva, koma osamvetsetsa;

kupenya muzipenya koma osaona kanthu.’

10Tsono anthu amenewa uwaphe mtima;

uwagonthetse makutu,

ndipo uwatseke mʼmaso.

Mwina angaone ndi maso awo,

angamve ndi makutu awo,

angamvetse ndi mitima yawo,

kenaka ndi kutembenuka mtima ndi kuchiritsidwa.”

11Pamenepo ine ndinati, “Zimenezo ndi mpaka liti Inu Ambuye?”

Ndipo Iyeyo anandiyankha kuti,

“Mpaka mizinda itasanduka mabwinja

nʼkusowa wokhalamo,

mpaka nyumba zitasowa anthu okhalamo,

mpaka dziko litasanduka chipululu ndithu,

12mpaka Yehova atasamutsira aliyense kutali,

dziko nʼkusiyidwa kwathunthu.

13Ndipo ngakhale chigawo chakhumi cha anthu chitatsala mʼdziko,

nachonso chidzawonongedwa.

Koma monga momwe mitengo ya muwanga ndi thundu

imasiyira chitsa pamene ayidula,

chonchonso mbewu yoyera idzatsalira ngati chitsa chotsala mʼdziko.”