Tsogolo la Yerusalemu
1Tsoka kwa mzinda wa anthu opondereza,
owukira ndi odetsedwa!
2Sumvera aliyense,
sulandira chidzudzulo.
Sumadalira Yehova,
suyandikira pafupi ndi Mulungu wake.
3Akuluakulu ake ali ngati mikango yobuma,
olamulira ake ndi olusa ngati mimbulu ya nthawi ya madzulo,
zimene pofika mmawa sizisiya chilichonse.
4Aneneri ake ndi odzikuza;
anthu achinyengo.
Ansembe ake amadetsa malo opatulika
ndipo amaphwanya lamulo.
5Yehova amene ali pakati pawo ndi wolungama;
Iye salakwa.
Tsiku ndi tsiku amaweruza molungama,
ndipo tsiku lililonse salephera,
komabe ochita zoyipa sachita manyazi nʼkomwe.
6“Ndachotseratu mitundu ya anthu;
ndagwetsa malinga awo.
Ndipo sindinasiye ndi mmodzi yemwe mʼmisewu mwawo,
popanda aliyense wodutsa.
Mizinda yawo yawonongedwa;
palibe aliyense adzatsalemo.
7Ndinati,
‘Ndithudi, anthu a mu mzindawu adzandiopa
ndi kumvera kudzudzula kwanga!’
Ndipo sindidzawononga nyumba zawo,
kapena kuwalanganso.
Koma iwo anali okonzeka
kuchita mwachinyengo zinthu zonse zimene amachita.
8Choncho mundidikire,” akutero Yehova,
“chifukwa cha tsiku limene ndidzaperekera umboni.
Ndatsimikiza kusonkhanitsa pamodzi mitundu ya anthu,
kusonkhanitsa maufumu
ndi kutsanulira ukali wanga pa iwo;
mkwiyo wanga wonse woopsa.
Dziko lonse lidzatenthedwa
ndi moto wa mkwiyo wa nsanje yanga.
9“Pamenepo ndidzayeretsa milomo ya anthu a mitundu yonse
kuti anthu onsewo ayitane dzina la Yehova
ndi kumutumikira Iye pamodzi.
10Kuchokera kutsidya kwa mitsinje ya ku Kusi
anthu anga ondipembedza, omwazikana,
adzandibweretsera zopereka.
11Tsiku limenelo simudzachita manyazi
chifukwa cha zoyipa zonse munandichitira,
popeza ndidzachotsa onse mu mzinda uwu
amene amakondwera chifukwa cha kunyada kwawo.
Simudzakhalanso odzikuza
mʼphiri langa lopatulika.
12Koma ndidzasiya pakati panu
anthu ofatsa ndi odzichepetsa,
amene amadalira dzina la Yehova.
13Aisraeli otsala sadzachitanso zolakwika;
sadzayankhulanso zonama,
ngakhale chinyengo sichidzatuluka mʼkamwa mwawo.
Adzadya ndi kugona
ndipo palibe amene adzawachititse mantha.”
14Imba, iwe mwana wamkazi wa Ziyoni;
fuwula mokweza, iwe Israeli!
Sangalala ndi kukondwera ndi mtima wako wonse,
iwe mwana wamkazi wa Yerusalemu!
15Yehova wachotsa chilango chako,
wabweza mdani wako.
Yehova, Mfumu ya Israeli, ali pakati pako;
sudzaopanso chilichonse.
16Pa tsiku limenelo adzanena kwa Yerusalemu kuti,
“Usaope, iwe Ziyoni;
usafowoke.
17Yehova Mulungu wako ali pakati pako,
ali ndi mphamvu yopulumutsa.
Adzakondwera kwambiri mwa iwe,
adzakukhalitsa chete ndi chikondi chake,
adzayimba mokondwera chifukwa cha iwe.”
18“Ndidzakuchotserani zowawa
za pa zikondwerero zoyikika;
nʼzolemetsa ndi zochititsa manyazi.
19Taonani, nthawi imeneyo ndidzathana ndi
onse amene anakuponderezani;
ndidzapulumutsa olumala
ndi kusonkhanitsa amene anamwazika.
Ndidzawayamikira ndi kuwachitira ulemu
mʼdziko lililonse mmene anachititsidwa manyazi.
20Pa nthawi imeneyo ndidzakusonkhanitsani;
pa nthawi imeneyo ndidzakubweretsani ku mudzi kwanu.
Ndidzakuyamikirani ndi kukuchitirani ulemu
pakati pa mitundu ya anthu a dziko lapansi
pamene ndidzabwezeretsa mtendere wanu
inu mukuona,”
akutero Yehova.