1Yehova anayankhula ndi Yoweli mwana wa Petueli.
Kubwera kwa Dzombe
2Inu akuluakulu, imvani izi;
mvetserani, nonse amene mumakhala mʼdziko.
Kodi zinthu zokhala ngati izi zinayamba zaonekapo mʼnthawi yanu,
kapena mʼnthawi ya makolo anu?
3Muwafotokozere ana anu,
ndipo ana anuwo afotokozere ana awo,
ndipo ana awo adzafotokozere mʼbado winawo.
4Chimene dzombe losamera mapiko lasiya
dzombe lowuluka ladya;
chimene dzombe lowuluka lasiya
dzombe lalingʼono ladya;
chimene dzombe lalingʼono lasiya
chilimamine wadya.
5Dzukani, inu zidakwa ndipo mulire!
Lirani mofuwula, inu nonse amene mumamwa vinyo;
lirani mofuwula chifukwa cha vinyo watsopano,
pakuti wachotsedwa pakamwa panu.
6Mtundu wa anthu wathira nkhondo dziko langa,
wamphamvu ndi wosawerengeka;
uli ndi mano a mkango,
zibwano za mkango waukazi.
7Wawononga mphesa zanga
ndipo wathyola mitengo yanga ya mkuyu.
Wakungunula makungwa ake
ndi kuwataya,
kusiya nthambi zake zili mbee.
8Lirani ngati namwali wovala chiguduli,
chifukwa cha mwamuna wa utsikana wake.
9Chopereka cha chakudya ndi cha chakumwa
sizikuperekedwa ku nyumba ya Yehova.
Ansembe akulira,
amene amatumikira pamaso pa Yehova.
10Minda yaguga,
nthaka yauma;
tirigu wawonongeka,
vinyo watsopano watha,
mitengo ya mafuta yauma.
11Khalani ndi nkhawa, inu alimi,
lirani mofuwula inu alimi a mphesa;
imvani chisoni chifukwa cha tirigu ndi barele,
pakuti zokolola za mʼmunda zawonongeka.
12Mpesa wauma
ndipo mtengo wamkuyu wafota;
makangadza, kanjedza ndi mitengo ya apulosi,
mitengo yonse ya mʼmunda yauma.
Ndithudi chimwemwe cha anthu
chatheratu.
Mulungu Ayitana Anthu kuti Atembenuke
13Inu ansembe, valani ziguduli ndipo lirani;
lirani mofuwula, inu amene mumatumikira pa guwa lansembe.
Bwerani, fundani ziguduli usiku wonse,
inu amene mumatumikira pamaso pa Mulungu wanga;
pakuti chopereka cha chakudya ndi cha chakumwa
sizikupezekanso mʼnyumba ya Mulungu wanu.
14Lengezani tsiku lopatulika losala zakudya,
itanani msonkhano wopatulika.
Sonkhanitsani akuluakulu
ndi anthu onse okhala mʼdziko
ku nyumba ya Yehova Mulungu wanu
ndipo alirire Yehova.
15Kalanga ine tsikulo!
Pakuti tsiku la Yehova layandikira;
lidzabwera ngati chiwonongeko chochokera kwa Wamphamvuzonse.
16Kodi chakudya chathu sichachotsedwa
ife tikuona?
Kodi mʼnyumba ya Mulungu wathu
simulibe chimwemwe ndi chisangalalo?
17Mbewu zikunyala
poti pansi ndi powuma.
Nyumba zosungiramo zinthu zawonongeka;
nkhokwe zapasuka
popeza tirigu wauma.
18Taonani mmene zikulirira ziweto;
ngʼombe zikungoyenda uku ndi uku
chifukwa zilibe msipu;
ngakhalenso nkhosa zikusauka.
19Kwa Inu Yehova ndilirira,
pakuti moto wapsereza msipu wakuthengo,
malawi amoto apsereza mitengo yonse ya mʼtchire.
20Ngakhale nyama zakuthengo zikulirira Inu;
timitsinje tonse taphwa
ndipo moto wapsereza msipu wa kuthengo.