Yoswa 6 – CCL & CARS

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yoswa 6:1-27

1Tsono mzinda wa Yeriko unali utatsekedwa kuti Aisraeli asalowe. Palibe amene amatuluka kapena kulowa.

2Kenaka Yehova anati kwa Yoswa, “Taona ndapereka Yeriko, pamodzi ndi mfumu yake ndi ankhondo ake mʼmanja mwako. 3Tsono iwe pamodzi ndi ankhondo ako onse muzizungulira mzindawu masiku asanu ndi limodzi, kamodzi pa tsiku. 4Ansembe asanu ndi awiri, atanyamula malipenga a nyanga za nkhosa zazimuna, akhale patsogolo pa Bokosi la Chipangano. Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri mudzazungulire mzindawu kasanu ndi kawiri ansembe akuliza malipenga. 5Ansembe adzalize malipenga kosalekeza. Tsono anthu onse akadzamva kuliza kumeneku adzafuwule kwambiri, ndipo makoma a mzindawo adzagwa. Zikadzatero ankhondo adzalowe mu mzindawo.”

6Ndipo Yoswa mwana wa Nuni anayitana ansembe ndipo anawawuza kuti, “Nyamulani Bokosi la Chipangano cha Yehova ndipo ansembe asanu ndi awiri anyamule malipenga. Iwowa akhale patsogolo pake.” 7Ndipo analamulira anthu kuti, “Yambani kuyenda! Yendani mozungulira mzinda ndipo ankhondo akhale patsogolo pa Bokosi la Yehova.”

8Mofanana ndi mmene Yoswa anayankhulira kwa anthu aja, ansembe asanu ndi awiri anapita patsogolo pa Bokosi la Chipangano la Yehova akuliza malipenga a nyanga za nkhosa zija, ndipo Bokosi la Chipangano cha Yehova limabwera pambuyo pawo. 9Ankhondo amayenda patsogolo pa ansembe amene amayimba malipenga, ndiponso gulu lina pambuyo pa Bokosilo. Nthawi yonseyi nʼkuti malipenga akulira. 10Koma Yoswa nʼkuti atalamulira anthu kuti, “Musafuwule, musakweze mawu anu kapena kuyankhula mpaka tsiku limene ndidzakuwuzani kuti mufuwule. Pamenepo mudzafuwule!” 11Ansembe onyamula Bokosi la Chipangano la Yehova anazungulira mzindawo kamodzi. Kenaka anthu anabwerera ku msasa wawo kukagona.

12Yoswa anadzuka mmawa tsiku linalo ndipo ansembe ananyamula Bokosi la Yehova. 13Ansembe asanu ndi awiri onyamula malipenga asanu ndi awiri anakhala patsogolo pa Bokosi la Yehova akuyimba malipenga. Ankhondo anali patsogolo pawo ndipo gulu lina linatsatira Bokosi la Yehova. Apa nʼkuti malipenga akulira. 14Tsiku lachiwiri anazunguliranso mzinda kamodzi ndi kubwerera ku misasa. Iwo anachita izi kwa masiku asanu ndi limodzi.

15Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri, anadzuka mʼbandakucha ndipo anazungulira mzindawo kasanu ndi kawiri. Ndi pa tsiku lokhali limene anazungulira mzindawu kasanu ndi kawiri. 16Pomwe amazungulira kachisanu ndi chiwiri, ansembe akuliza malipenga mokweza, Yoswa analamulira anthu kuti “Fuwulani pakuti Yehova wakupatsani mzindawu! 17Mzindawu ndi zonse zimene zili mʼmenemo muziwononge. Rahabe yekha, mayi wadama, ndi aliyense amene ali pamodzi naye mʼnyumba mwake asaphedwe, chifukwa anabisa anthu odzazonda, amene ife tinawatuma 18Koma musatenge kanthu kalikonse koyenera kuwonongedwa. Mukadzangotenga kanthu kalikonse koyenera kuwonongedwa, mudzaputa mavuto, misasa ya Israeli idzawonongedwa. 19Zonse za siliva ndi golide, ziwiya zamkuwa ndi zachitsulo, ndi zake za Yehova ndipo ziyenera kukasungidwa mosungiramo chuma chake.”

20Ansembe analiza malipenga. Anthu atamva kulira kwa malipenga, anafuwula kwambiri ndipo makoma a Yeriko anagwa. Choncho ankhondo anabwera ku mzinda uja nawulanda. 21Iwo analowa mu mzindawo nawononga ndi lupanga chilichonse chamoyo kuyambira amuna, akazi, ana ndi akulu, ngʼombe, nkhosa ndi abulu.

22Yoswa anawuza anthu awiri amene anakazonda dziko aja kuti, “Pitani ku nyumba ya mkazi wadama uja ndipo mukamutulutse iye pamodzi ndi onse amene ali naye ndipo mukabwere nawo kuno, munamulumbirira.” 23Choncho iwo anapita nakatenga Rahabe, abambo ake ndi amayi ake, abale ake ndi onse amene anali naye. Iwo anatulutsa banja lake lonse ndipo analiyika kuseri kwa msasa wa Aisraeli.

24Kenaka iwo anawotcha mzinda wonse ndi chilichonse chimene chinali mʼmenemo, kupatulapo zasiliva ndi zagolide pamodzi ndi ziwiya zamkuwa ndi zachitsulo zimene anakaziyika mʼnyumba yosungiramo chuma cha Yehova. 25Koma Yoswa sanaphe Rahabe, mkazi wadamayo pamodzi ndi banja lake ndi onse amene anali naye, chifukwa anabisa anthu amene iye anawatuma kukazonda Yeriko. Zidzukulu zake za Rahabeyo zikukhala pakati pa Aisraeli mpaka lero.

26Pa nthawi imeneyo Yoswa anapereka chenjezo motemberera kuti, “Akhale wotembereredwa pamaso pa Yehova munthu amene adzamangenso mzinda uwu wa Yeriko:

“Aliyense amene adzayike maziko ake,

mwana wake wamwamuna wachisamba adzafa,

aliyense womanga zipata zake

mwana wake wamngʼono adzafa.”

27Motero Yehova anali ndi Yoswa, ndipo mbiri yake inafalikira dziko lonse.

Священное Писание

Иешуа 6:1-26

1И Вечный сказал Иешуа:

– Смотри, Я отдал Иерихон вместе с его царём и храбрыми воинами в твои руки. 2Обходи город вместе со всеми воинами раз в день. Делай это в течение шести дней. 3Пусть семь священнослужителей идут перед сундуком, и пусть каждый держит в своих руках по бараньему рогу. На седьмой день обойдите вокруг города семь раз, а священнослужители должны трубить в рога. 4Когда вы услышите, как они протрубят долгий сигнал, пусть весь народ издаст громкий крик. Тогда стена города рухнет до своего основания и народ устремится прямо в город.

5Иешуа, сын Нуна, призвал священнослужителей и сказал им:

– Возьмите сундук соглашения, и пусть каждый из семи священнослужителей несёт перед ним по рогу.

6Народу же он велел:

– Вперёд! Обойдите город, а перед сундуком Вечного пусть идёт вооружённая стража.

7Когда Иешуа сказал всё народу, семь священнослужителей, трубя в рога, двинулись вперёд, перед Вечным, а сундук соглашения с Вечным последовал за ними. 8Вооружённая стража шла перед священнослужителями, которые трубили в рога, а замыкала шествие другая стража, что шла за сундуком. Всё это время трубили рога. 9Но Иешуа велел народу:

– Не издавайте военного клича, не поднимайте голоса, не говорите ни слова до того дня, когда я сам не велю вам закричать. И только тогда кричите!

10Так сундук Вечного обнесли вокруг города один раз. После этого весь народ вернулся в лагерь и ночевал там.

11На следующее утро Иешуа встал рано, и священнослужители взяли сундук Вечного. 12Семеро священнослужителей, трубя в рога, двинулись вперёд перед сундуком Вечного. Вооружённые люди шли перед ним, а замыкала шествие стража, что шла за сундуком Вечного; рога же постоянно трубили. 13На второй день исраильтяне обошли город один раз и вернулись в лагерь. Так они делали шесть дней. 14На седьмой день они поднялись на заре и обошли вокруг города семь раз таким же образом. Только в этот день они обошли город семь раз. 15И на седьмой раз, когда священнослужители протрубили в рога, Иешуа велел народу:

– Кричите, потому что Вечный отдал вам город! 16Город должен быть полностью уничтожен, он и всё, что в нём, принадлежит Вечному. Только блудница Рахав и все, кто находится с ней в доме, должны остаться в живых, потому что она спрятала лазутчиков, которых мы посылали. 17Но берегитесь подлежащих уничтожению вещей, чтобы вам не погубить самих себя, взяв что-либо из них. Тогда вы обречёте на гибель лагерь исраильтян и наведёте на него беду. 18Всё серебро, золото и изделия из бронзы и железа – это святыня Вечного, они поступят в Его сокровищницу.

19Когда рога протрубили, народ закричал, и при трубном звуке, когда народ издал громкий крик, стена рухнула до самого основания. Тогда все устремились прямо в город и захватили его. 20Они полностью уничтожили город, истребив в нём мечом всякое живое существо – мужчин и женщин, молодых и стариков, волов, овец и ослов.

21Иешуа сказал двум людям, которые разведывали эту землю:

– Идите в дом блудницы Рахав и выведите её вместе со всей семьёй, как вы ей поклялись.

22И юноши, которые были лазутчиками, вошли и вывели Рахав, её отца, мать, братьев и всех её родственников. Они вывели всю её семью и оставили их за пределами исраильского лагеря. 23После этого они сожгли весь город и всё, что в нём, но серебро, золото и изделия из бронзы и железа они положили в сокровищницу дома Вечного. 24А блудницу Рахав с её семьёй и всеми её родственниками Иешуа пощадил, потому что она спрятала людей, которых он посылал лазутчиками в Иерихон. Её семья живёт среди исраильтян и до сих пор.

25Тогда-то Иешуа и произнёс это заклятие:

– Проклят перед Вечным тот человек, который станет отстраивать этот город, Иерихон:

Ценой своего первенца

он заложит его основания;

ценой своего младшего

он поставит его врата.

26Вечный был с Иешуа, и слава Иешуа распространялась по всей земле.