Yoswa 5 – CCL & NIVUK

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yoswa 5:1-15

Mwambo wa Mdulidwe pa Giligala

1Mafumu onse a Aamori, a kummawa kwa Yorodani ndi mafumu onse a Akanaani a mʼmbali mwa Nyanja anamva momwe Yehova anawumitsira Yorodani pamene Aisraeli ankawoloka. Choncho anachita mantha ndi kutayiratu mtima chifukwa cha Aisraeliwo.

2Tsono Yehova anati kwa Yoswa, “Panga mipeni ya miyala ndipo uchitenso mwambo wa mdulidwe pa Aisraeli.” 3Choncho Yoswa anapanga mipeni ya miyala ndi kuchita mdulidwe Aisraeli ku Gibeyati Haaraloti.

4Chifukwa chimene Yoswa anachitira izi ndi ichi: Onse amene anatuluka mʼdziko la Igupto, amuna onse amene anali oyenera kumenya nkhondo anatha kufa mʼchipululu atatuluka mʼdziko la Igupto. 5Anthu onse amene anatuluka mʼdziko la Igupto anali atachita mwambo wa mdulidwe, koma onse amene anabadwira mʼchipululu, pa ulendo wochoka ku Igupto, sanachite. 6Aisraeli anakhala akuyenda mʼchipululu kwa zaka makumi anayi mpaka amuna onse amene potuluka mʼdziko la Igupto anali a msinkhu woyenera kupita ku nkhondo anamwalira. Iwo anafa chifukwa sanamvere mawu a Yehova. Yehova anawalumbirira kuti sadzalowa konse mʼdziko loyenda mkaka ndi uchi limene analonjeza kwa makolo awo kuti adzatipatsa. 7Koma ana awo amene analowa mʼmalo mwawo ndiwo amene Yoswa anawachita mdulidwe popeza sanachite pamene anali pa ulendo wawo mʼchipululu muja. 8Atamaliza kuchita mdulidwe uja, anthu onse anakakhala ku misasa yawo kudikira kuti zilonda zipole.

9Kenaka Yehova anati kwa Yoswa, “Kuyambira tsopano anthu a ku Igupto sadzakunyozaninso.” Nʼchifukwa chake malowa anatchedwa Giligala mpaka lero.

10Akupumulabe ku Giligala kuja mʼchigwa cha Yeriko, Aisraeli anachita chikondwerero cha Paska madzulo pa tsiku la 14 la mwezi woyamba womwewo. 11Mmawa mwake ndi pamene anayamba kudya zakudya za mʼdziko la Kanaani. Anaphika buledi wopanda yisiti ndi kukazinga tirigu tsiku lomwelo. 12Atangodya chakudya cha mʼdzikomo, mana anasiya kugwa, ndipo sanapezekenso. Kuyambira nthawi imeneyo Aisraeli anayamba kudya chakudya cha mʼdziko la Kanaani.

Kugwa kwa Makoma a Yeriko

13Tsiku lina pamene Yoswa anali pafupi ndi Yeriko, anakweza maso ake ndipo mwadzidzidzi anaona munthu atayima patsogolo pake ndi lupanga losolola mʼdzanja lake. Yoswa anapita pamene panali munthuyo ndipo anamufunsa kuti, “Kodi uli mbali yathu kapena ya adani athu?”

14Iye anayankha kuti “Sindili mbali iliyonse. Ndabwera monga mkulu wa asilikali a Yehova.” Pomwepo Yoswa anadzigwetsa chafufumimba kupereka ulemu, ndipo anamufunsa, “Kodi mbuye wanga muli ndi uthenga wotani kwa mtumiki wanu?”

15Mkulu wa asilikali a Yehova uja anayankha kuti, “Vula nsapato zako, pakuti wayima pa malo wopatulika.” Ndipo Yoswa anachitadi zimene anawuzidwazo.

New International Version – UK

Joshua 5:1-15

1Now when all the Amorite kings west of the Jordan and all the Canaanite kings along the coast heard how the Lord had dried up the Jordan before the Israelites until they5:1 Another textual tradition we had crossed over, their hearts melted in fear and they no longer had the courage to face the Israelites.

Circumcision and Passover at Gilgal

2At that time the Lord said to Joshua, ‘Make flint knives and circumcise the Israelites again.’ 3So Joshua made flint knives and circumcised the Israelites at Gibeath Haaraloth.5:3 Gibeath Haaraloth means the hill of foreskins.

4Now this is why he did so: all those who came out of Egypt – all the men of military age – died in the wilderness on the way after leaving Egypt. 5All the people that came out had been circumcised, but all the people born in the wilderness during the journey from Egypt had not. 6The Israelites had moved about in the wilderness for forty years until all the men who were of military age when they left Egypt had died, since they had not obeyed the Lord. For the Lord had sworn to them that they would not see the land that he had solemnly promised their ancestors to give us, a land flowing with milk and honey. 7So he raised up their sons in their place, and these were the ones Joshua circumcised. They were still uncircumcised because they had not been circumcised on the way. 8And after the whole nation had been circumcised, they remained where they were in camp until they were healed.

9Then the Lord said to Joshua, ‘Today I have rolled away the reproach of Egypt from you.’ So the place has been called Gilgal5:9 Gilgal sounds like the Hebrew for roll. to this day.

10On the evening of the fourteenth day of the month, while camped at Gilgal on the plains of Jericho, the Israelites celebrated the Passover. 11The day after the Passover, that very day, they ate some of the produce of the land: unleavened bread and roasted grain. 12The manna stopped the day after5:12 Or the day they ate this food from the land; there was no longer any manna for the Israelites, but that year they ate the produce of Canaan.

The fall of Jericho

13Now when Joshua was near Jericho, he looked up and saw a man standing in front of him with a drawn sword in his hand. Joshua went up to him and asked, ‘Are you for us or for our enemies?’

14‘Neither,’ he replied, ‘but as commander of the army of the Lord I have now come.’ Then Joshua fell face down to the ground in reverence, and asked him, ‘What message does my Lord5:14 Or lord have for his servant?’

15The commander of the Lord’s army replied, ‘Take off your sandals, for the place where you are standing is holy.’ And Joshua did so.