Yoswa 23 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yoswa 23:1-16

Kutsanzika kwa Yoswa

1Panapita nthawi yayitali kuchokera pamene Yehova anakhazikitsa mtendere pakati pa Aisraeli ndi adani awo owazungulira. Nthawi imeneyi nʼkuti Yoswa atakalamba, ali ndi zaka zambiri. 2Yoswayo anayitanitsa Aisraeli onse pamodzi ndi akuluakulu, atsogoleri, oweruza, ndi oyangʼanira anthu antchito ndipo anawawuza kuti, “Ine ndakalamba ndipo ndili ndi zaka zambiri. 3Inu mwaona zonse zimene Yehova Mulungu wanu wachita kwa mitundu yonseyi chifukwa cha inu. Ndi Yehova Mulungu wanu amene anakumenyerani nkhondo. 4Tsono onani! Mitundu ya anthu otsalawa ndayipereka kwa mafuko anu pamodzi ndi mitundu ya anthu ya pakati pa Yorodani ndi Nyanja Yayikulu ya kumadzulo imene ndinayigonjetsa. 5Yehova Mulungu wanu ndiye adzawathamangitsa pamaso panu. Mudzatenga dziko lawo monga Yehova anakulonjezerani.

6“Choncho khalani amphamvu, ndipo samalani kuti mumvere zonse zimene zalembedwa mʼbuku la malamulo a Mose. Musapatuke pa malamulo onse amene alembedwamo. 7Musagwirizane ndi mitundu ya anthu imene yatsala pakati panu. Musatchule mayina a milungu yawo kapena kuyitchula polumbira. Musayitumikire kapena kuyigwadira. 8Koma mukuyenera kugwiritsa Yehova Mulungu wanu, monga mwachitira mpaka lero lino.

9“Yehova wapirikitsa patsogolo panu mitundu ya anthu ikuluikulu ndi yolimba. Mpaka lero palibe amene watha kulimbana nanu. 10Aliyense wa inu atha kuthamangitsa anthu 1,000 chifukwa Yehova Mulungu wanu ndiye amakumenyerani nkhondo, monga momwe analonjezera. 11Choncho samalitsani kuti mukonde Yehova Mulungu wanu.

12“Koma ngati mubwerera mʼmbuyo ndi kuphatikizana ndi mitundu yotsalayi imene ili pakati panu ndi kumakwatirana nayo, 13pamenepo mudziwe kuti Yehova, Mulungu wanu, sadzapirikitsa mitundu imeneyi pamaso panu, koma idzakhala ngati msampha kwa inu kapenanso khwekhwe lokukolani. Idzakhala ngati zikwapu pa msana panu kapenanso ngati minga mʼmaso mwanu mpaka mutatha psiti mʼdziko labwinoli limene Yehova Mulungu wanu wakupatsani.

14“Aliyense wa inu akudziwa mu mtima mwake komanso mʼmoyo mwake kuti zabwino zonse zimene Yehova Mulungu wanu anakulonjezani zachitika. Palibe lonjezo ndi limodzi lomwe limene silinakwaniritsidwe. 15Monga momwe Yehova Mulungu wanu wakuchitirani zabwino zonse zimene ananena kuti adzachita, Yehovayo angathenso kukuchitirani zoyipa zonse zimene waopseza, mpaka kukuchotsani mʼdziko lokoma limene anakupatsani. 16Ngati muphwanya pangano la Yehova Mulungu wanu, limene anakulamulirani nʼkumapita kukatumikira milungu ina ndi kuyigwadira, Yehova adzakukwiyirani, ndiye mudzachotsedwa mʼdziko labwinoli limene Yehova wakupatsani.”

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

約書亞記 23:1-16

約書亞的訣別之言

1此後很長時間,耶和華使以色列人四境太平,沒有戰事。約書亞年事已高, 2他召來了以色列的長老、族長、審判官和官長,對他們說:「我已經老了, 3你們都親眼看見你們的上帝耶和華怎樣為了你們而對付列邦,親自為你們爭戰。 4約旦河到地中海的這片土地,無論是已征服的還是沒有征服的,我已經用抽籤的方式分給你們各支派作產業。 5你們的上帝耶和華必把列邦從你們面前趕出去,使他們離開你們。這樣,你們就可以承受他們的土地,正如你們的上帝耶和華的應許。 6所以,你們應當剛強,謹遵摩西律法書上所記載的一切,不可有半點偏離。 7不可與你們中間剩下的異族混雜,不可提他們的神明或憑它們起誓,不可供奉、祭拜他們的神明。 8你們要一如既往地倚靠你們的上帝耶和華, 9因為祂為你們趕走了強大的外族人,至今無人敵得過你們。 10你們一個人能打敗他們一千人,因為你們的上帝耶和華照著祂的應許為你們爭戰。 11所以你們要特別謹慎,愛你們的上帝耶和華。 12如果你們悖逆,跟你們當中剩下的異族人聯合,通婚往來, 13毫無疑問,你們的上帝耶和華必不再為你們趕走他們。相反,他們還要成為設在你們當中的圈套和陷阱,你們的肉中刺、眼中釘,直到你們在你們的上帝耶和華所賜給你們的這塊美好的土地上滅亡。

14「我快要走完人世的路程了。你們深知你們的上帝耶和華賜給你們的一切美好應許沒有一句落空,都已經應驗了。 15正如你們的上帝耶和華已成就祂應許給你們的一切福氣,如果你們違背祂,祂必照樣降各樣災禍給你們,直到把你們從祂所賜的這美好土地上毀滅。 16你們如果違背你們的上帝耶和華吩咐你們遵守的約,去供奉、祭拜別的神明,祂必向你們發怒,使你們在祂所賜的這美好土地上迅速滅亡。」