Yona 2 – The Word of God in Contemporary Chichewa CCL

The Word of God in Contemporary Chichewa

Yona 2:1-10

Pemphero la Yona

1Yona ali mʼmimba mwa chinsomba chija anapemphera kwa Yehova Mulungu wake. 2Iye anati:

“Pamene ndinali mʼmavuto anga ndinayitana Yehova,

ndipo Iye anandiyankha.

Ndili ku dziko la anthu akufa ndinapempha thandizo,

ndipo Inu munamva kulira kwanga.

3Munandiponya mʼnyanja yozama,

mʼkati mwenimweni mwa nyanja,

ndipo madzi oyenda anandizungulira;

mafunde anu onse ndi mkokomo wake

zinandimiza.

4Ndinati, ‘Ine ndachotsedwa

pamaso panu;

komabe ndidzayangʼananso

ku Nyumba yanu yopatulika.’

5Madzi wondimiza anandichititsa mantha,

nyanja yozama inandizungulira;

udzu wa mʼmadzi zinakuta mutu wanga.

6Ndinatsikira kunsi ndithu, mʼtsinde mwa mapiri;

mipiringidzo ya dziko inanditsekereza kosatha.

Koma Inu munatulutsa moyo wanga mʼmandamo,

Inu Yehova Mulungu wanga.

7“Pamene moyo wanga umachoka mwa ine,

ine ndinakumbukira Inu Yehova,

ndipo pemphero langa linafika kwa inu,

ku Nyumba yanu yopatulika.

8“Iwo amene amagwiritsitsa mafano achabechabe

amataya chisomo chawo.

9Koma ine ndidzapereka kwa Inu nsembe

ndikuyimba nyimbo yamayamiko.

Chimene ndinalonjeza ndidzachikwaniritsa.

Chipulumutso chimachokera kwa Yehova.”

10Ndipo Yehova analamula chinsomba chija, ndipo chinakamusanza Yonayo mʼmbali mwa nyanja.