Yesu Aonekera kwa Ophunzira ku Nyanja ya Tiberiya
1Zitatha izi Yesu anaonekeranso kwa ophunzira ake, mʼmbali mwa nyanja ya Tiberiya. Anadzionetsera motere: 2Simoni Petro, Tomasi (otchedwa Didimo), Natanieli wochokera ku Kana wa ku Galileya, ana a Zebedayo, ndi ophunzira ena awiri anali limodzi. 3Simoni Petro anawawuza iwo kuti, “Ine ndikupita kukasodza,” ndipo iwo anati, “ife tipita nawe.” Choncho anapita ndi kulowa mʼbwato, koma usiku umenewo sanagwire kanthu.
4Mmamawa, Yesu anayimirira mʼmbali mwa nyanja, koma ophunzira ake sanazindikire kuti anali Yesu.
5Yesu anawafunsa iwo kuti, “Anzanga, kodi muli nsomba?”
Iwo anayankha kuti, “Ayi.”
6Iye anati, “Ponyani khoka lanu kudzanja lamanja la bwato lanu ndipo mupha kanthu.” Atatero, iwo analephera kukoka ukonde chifukwa chakuchuluka kwa nsomba.
7Kenaka ophunzira amene Yesu amamukonda anati kwa Petro, “Ndi Ambuye!” Petro atangomva iye akunena kuti ndi Ambuye, iye anavala chovala chake (pakuti anali atavula) ndipo analumphira mʼnyanja. 8Ophunzira enawo analowa mʼbwato akukoka ukonde odzaza ndi nsomba, popeza iwo sanali kutali kuchokera ku mtunda, pafupifupi mamita makumi asanu ndi anayi. 9Atafika pa mtunda, iwo anaona moto wamakala pamenepo ndi nsomba, ndi buledi.
10Yesu anawawuza kuti, “Tabweretsa nsomba zina mwagwirazo.”
11Simoni Petro anakwera mʼbwato ndi kukokera khoka ku gombe, lodzaza ndi nsomba zikuluzikulu 153, komabe ndi nsomba zochuluka chotero khoka silinangʼambike. 12Yesu anawawuza kuti, “Bwerani mudzalandire chakudya chammawa.” Palibe mmodzi wa ophunzira anayesa kumufunsa Iye, “Kodi ndinu ndani?” Iwo anadziwa kuti anali Ambuye. 13Yesu anabwera, natenga buledi ndikuwapatsa iwo, ndipo anachita chimodzimodzi ndi nsomba. 14Aka kanali tsopano kachitatu Yesu akuonekera kwa ophunzira ake Iye ataukitsidwa kwa akufa.
Yesu Abwezeretsa Petro
15Iwo atamaliza kudya chakudya chammawa, Yesu anati kwa Simoni Petro, “Simoni, mwana wa Yohane, kodi umandikonda Ine kuposa mmene amandikondera awa?”
Iye anati, “Inde Ambuye, Inu mukudziwa kuti Ine ndimakukondani.”
Yesu anati, “Samala ana ankhosa anga.”
16Yesu anatinso, “Simoni, mwana wa Yohane, kodi umandikondadi Ine?”
Iye anayankha kuti, “Inde, Ambuye, Inu mukudziwa kuti ine ndimakukondani.”
Yesu anati, “Weta nkhosa zanga.”
17Yesu anati kwa iye kachitatu, “Simoni, mwana wa Yohane, kodi umandikondadi Ine?”
Petro anadzimvera chisoni chifukwa Yesu anamufunsa kachitatu kuti, “Kodi umandikonda Ine?” Iye anati, “Ambuye, Inu mudziwa zinthu zonse. Inu mukudziwa kuti Ine ndimakukondani.”
Yesu anati, “Dyetsa nkhosa zanga. 18Zoonadi, Ine ndikukuwuza kuti uli wamngʼono unkadziveka wekha lamba ndi kupita kumene unkafuna; koma ukadzakalamba udzatambasula manja ako ndipo wina wake adzakuveka ndikukutsogolera kupita kumene sukufuna kupita.” 19Yesu ananena izi kumuzindikiritsa mtundu wa imfa imene Petro adzalemekezera nayo Mulungu. Kenaka Iye anati kwa Petro, “Nditsate Ine!”
20Petro anatembenuka ndi kuona kuti ophunzira amene Yesu amamukonda amawatsatira iwo. (Uyu ndi amene anatsamira pachifuwa cha Yesu pa chakudya chamadzulo ndipo iye anati, “Ambuye, kodi ndi ndani amene adzakuperekani Inu?” 21Petro atamuona iye, anafunsa kuti, “Ambuye, nanga uyu?”
22Yesu anayankha kuti, “Ine nditafuna kuti akhalebe ndi moyo mpaka nditabweranso, zikukukhudza bwanji zimenezo? Iwe uyenera kunditsata Ine.” 23Chifukwa cha ichi mbiri inafala pakati pa abale kuti wophunzira uyu sadzafa. Koma Yesu sananene kuti iye sadzafa. Iye anati, “Ine nditafuna kuti akhalebe ndi moyo mpaka nditabweranso, zikukukhudza bwanji zimenezo?”
24Uyu ndi wophunzira amene akuchitira umboni ndipo ndi amene analemba. Ife tidziwa kuti umboni wake ndi woona.
25Koma palinso zina zambiri zimene Yesu anachita. Zikanalembedwa zonsezi, ndikhulupirira dziko lonse lapansi likanasowa malo osungirako mabuku onse amene akanalembedwa.