Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yobu 4

Mawu a Elifazi

1Pamenepo Elifazi wa ku Temani anayankha kuti,

“Ngati wina atakuyankha, kodi ungakhumudwe?
    Koma ndani angakhale chete wosayankhula?
Taganiza momwe iwe walangizira anthu ambiri,
    momwe walimbitsira anthu ofowoka.
Mawu ako analimbitsa anthu ofuna kugwa;
    unachirikiza anthu wotha mphamvu.
Koma tsopano mavuto akufikira ndipo wataya mtima,
    zakukhudza ndipo uli ndi mantha.
Kodi kuopa Mulungu kwako sindiko kulimbika mtima kwako?
    Ndipo moyo wako wosalakwa ndiye chiyembekezo chako?

“Ganiza bwino tsopano: Kodi munthu wosalakwa anawonongekapo nʼkale lonse?
    Nʼkuti kumene munthu wolungama mtima anaphedwa?
Monga ndaonera ine, anthu amene amatipula zoyipa,
    ndi iwo amene amadzala mavuto, amakolola zomwezo.
Iwo amaphedwa ndi mpweya wa Mulungu;
    amawonongeka ndi mpweya waukali wa mkwiyo wake.
10 Mikango imabangula ndi kulira,
    komabe mano a mikango yamphamvu amathyoledwa.
11 Mkango umafa chifukwa chosowa nyama,
    ndipo ana amkango amamwazikana.

12 “Mawu anabwera kwa ine mwamseri,
    makutu anga anamva kunongʼona kwake.
13 Mʼkati mwa maloto ochititsa mantha usiku,
    nthawi imene anthu amagona tulo tofa nato,
14 ndinagwidwa ndi mantha, ndi kuyamba kunjenjemera
    ndipo mafupa anga onse anaweyeseka.
15 Pamenepo mzimu unadutsa pamaso panga,
    ndipo ubweya wa pa thupi langa unayima kuti njoo.
16 Chinthucho chinayimirira
    koma sindinathe kuzindikira kuti chinali chiyani.
Chinthu chinayima patsogolo panga,
    kunali zii ndipo ndinamva mawu akuti,
17 ‘Kodi munthu angathe kukhala wolungama kupambana Mulungu?
    Kodi munthu angathe kukhala wangwiro kupambana Mlengi wake?
18 Ngati Mulungu sakhulupirira atumiki ake omwe,
    ngati Iye amawapeza angelo ake ndi cholakwa,
19 nanga kuli bwanji ndi iwo amene amakhala mʼnyumba zadothi,
    amene maziko awo ndi fumbi,
    amene amathudzuka mosavuta ngati kadziwotche!
20 Mmawa ali moyo, pofika madzulo afa;
    mwakachetechete, amawonongeka kwamuyaya.
21 Kodi zonse zimene ali nazo sizimatheratu,
    kotero kuti amafa osadziwa nʼkanthu komwe?’