Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yobu 28

1Pali mgodi wa siliva
    ndiponso malo oyengerapo golide.
Chitsulo amachikumba pansi,
    ndipo mkuwa amawusungunula ku miyala yamkuwa.
Munthu amalowa mu mdima atatenga nyale,
    amafunafuna miyala mpaka ku malire a mgodiwo,
    kufuna mkuwa mu mdima wandiweyani.
Amakumba njira zapansi mu mgodimo, kutali ndi kumene kumakhala anthu,
    kumalo kumene phazi la munthu silinapondeko;
    iye amakhala ali lende pansipo namazungulira uku ndi uku.
Nthaka, imene imatulutsa zakudya,
    kunsi kwake kumachita ngati kwasandulizika ndi moto;
miyala ya safiro imachokera mʼmatanthwe ake,
    ndipo mʼfumbi lake mumakhala miyala yagolide.
Palibe mbalame yodya zinzake imene imadziwa njira yobisikayi,
    palibe kamtema amene anayiona.
Zirombo zolusa sizipondamo mʼnjiramo,
    ndipo mkango sudzeranso mʼmenemo.
Munthu amaphwanya matanthwe olimba,
    ndipo amagubuduza mapiri kuyambira mʼtsinde.
10 Amabowola njira mʼmatanthwewo;
    ndipo amaona chuma chonse cha mʼphirimo.
11 Amaletsa mitsinje ya pansipo kuti isayendenso,
    motero amatulutsira poyera zinthu zobisika.

12 “Koma nzeru zingapezeke kuti?
    Kodi kumvetsa zinthu kumakhala kuti?
13 Munthu sadziwa kufunika kwake kwa nzeruzo;
    nzeruyo sipezeka pa dziko lino la anthu amoyo.
14 Phompho likuti, ‘Sizipezeka mwa ine muno.’
    Nyanja ikuti, ‘Mwa ine munonso ayi.’
15 Nzeru sungazigule ndi golide wabwino kwambiri,
    mtengo wake sungawuyerekeze ndi siliva wambiri.
16 Nzeru singagulidwe ndi golide wa ku Ofiri,
    kapena ndi miyala ya onikisi kapena ya safiro.
17 Nzeru sungayiyerekeze ndi golide kapena mwala wa galasi,
    sungayigule ndi zokometsera zagolide.
18 Miyala ya korali ndi krisitali siyoyeneranso ndi kuyitchula nʼkomwe;
    mtengo wa nzeru ndi woposa miyala ya rubi.
19 Nzeru sungayiyerekeze ndi miyala ya topazi ya ku Kusi;
    nzeru singagulidwe ndi golide wabwino kwambiri.

20 “Kodi tsono nzeru zimachokera kuti?
    Kodi kumvetsa zinthu kumakhala kuti?
21 Malo ake ndi obisika kwa zamoyo zonse,
    ndi obisika ngakhale kwa mbalame zamlengalenga.
22 Chiwonongeko ndi imfa zikuti,
    ‘Tangomva mphekesera chabe ya zimenezo!’
23 Mulungu yekha ndiye amadziwa njira yake yopita kumeneko,
    ndipo Iye yekha amadziwa kumene nzeru imakhala,
24 pakuti Iye amayangʼana mpaka ku malekezero a dziko lapansi
    ndipo amaona zonse za kunsi kwa thambo.
25 Iye atapatsa mphepo mphamvu zake,
    nayeza kuzama kwa nyanja,
26 atakhazikitsa lamulo loti mvula izigwa
    ndi kukonza njira ya chingʼaningʼani cha bingu,
27 pamenepo ndi pamene anayangʼana nzeruzo naziyeza mtengo wake;
    nazikhazikitsa ndi kuzisanthula bwino lomwe.
28 Ndipo Iye anati kwa munthu,
    ‘Taonani, kuopa Ambuye, ndiye nzeru zimenezo
    ndipo kuthawa zoyipa ndiye kumvetsa zinthu kumeneko.’ ”