Yesaya 59 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yesaya 59:1-21

Tchimo, Kuvomereza ndi Chipulumutso

1Taonani, mkono wa Yehova si waufupi kuti sungathe kupulumutsa,

kapena khutu lake kuti ndilogontha kuti sangamve.

2Koma zoyipa zanu zakulekanitsani

ndi Mulungu wanu;

ndipo wakufulatirani chifukwa cha machimo anu,

kotero Iye sadzamva.

3Pakuti manja anu ali psuu ndi magazi.

Munayipitsa zala zanu ndi zamphulupulu.

Pakamwa panu payankhula zabodza,

ndipo lilime lanu lanena zinthu zoyipa.

4Palibe amene akuyimba mnzake mlandu molungama,

palibe amene akupita ku mlandu moona mtima.

Iwo amadalira mawu opanda pake ndipo amayankhula mabodza;

amalingalira za mphulupulu ndipo amachita zoyipa.

5Iwo amayikira mazira a mamba

ndipo amaluka ukonde wakangawude.

Aliyense amene adzadya mazira awo adzafa,

ndipo ngati dzira limodzi lasweka limatulutsa mphiri.

6Ukonde wawo wa kangawude sangawuvale ngati chovala;

ndipo chimene apangacho sangachifunde.

Ntchito zawo ndi zoyipa,

ndipo amakonda kuchita zandewu ndi manja awo.

7Amathamangira kukachita zoyipa;

sachedwa kupha anthu osalakwa.

Maganizo awo ndi maganizo oyipa;

kulikonse kumene amapita amasiyako bwinja ndi chiwonongeko.

8Iwo sadziwa kuchita za mtendere;

zonse zimene amachita nʼzopanda chilungamo.

Njira zawo zonse nʼzokhotakhota;

aliyense oyenda mʼnjira zimenezo sadzapeza mtendere.

9Anthu akuti, “Chifukwa cha zimenezi chilungamo chatitalikira;

ndipo chipulumutso sichitifikira.

Timafunafuna kuwala koma timangopeza mdima okhaokha;

tinayembekezera kuyera koma timayenda mu mdima wandiweyani.

10Timapapasapapasa khoma ngati munthu wosaona,

kuyangʼanayangʼana njira ngati anthu opanda maso.

Timapunthwa dzuwa lili paliwombo ngati kuti ndi usiku;

timakhala pansi mu mdima ngati anthu akufa.

11Tonse timabangula ngati zimbalangondo:

Timalira modandaula ngati nkhunda.

Tinayembekezera kuweruza kolungama; koma sitikupeza.

Timayembekezera chipulumutso koma chimakhala nafe kutali.”

12Pakuti zolakwa zathu nʼzochuluka pamaso panu,

ndipo machimo athu akutsutsana nafe.

Zolakwa zathu zili ndi ife nthawi zonse

ndipo tikuvomereza machimo athu:

13Tawukira ndi kumukana Yehova.

Tafulatira Mulungu wathu,

pa kupondereza anzathu ndi kupandukira Yehova,

ndi pa kuyankhula mabodza amene tawaganiza mʼmitima mwathu.

14Motero kuweruza kolungama kwalekeka

ndipo choonadi chili kutali ndi ife;

kukhulupirika sikukupezekanso mʼmabwalo a milandu,

ndipo kuona mtima sikukupezekanso mʼmenemo.

15Choonadi sichikupezeka kumeneko,

ndipo wina akakana kuchita nawo zoyipa amapeza mavuto.

Yehova anaziona zimenezi ndipo zinamunyansa

kuti panalibe chiweruzo cholungama.

16Yehova anaona kuti panalibe ndi mmodzi yemwe,

Iye anadabwa kuti panalibe ndi mmodzi yemwe woti nʼkupembedzera;

Choncho mphamvu zake zomwe zinamuthandiza,

ndipo anadzilimbitsa ndi kulungama kwake;

17Iye anavala chilungamo ngati chovala chachitsulo chapachifuwa,

ndipo kumutu kwake amavala chipewa chachipulumutso;

anavala kulipsira ngati chovala

ndipo anadzikuta ndi mkwiyo ngati chofunda.

18Iye adzawabwezera chilango adani a anthu ake

molingana ndi zimene anachita,

adzaonetsa ukali kwa adani ake

ndi kubwezera chilango odana naye.

Adzalanga ngakhale okhala mayiko akutali.

19Choncho akadzabwera ngati madzi

oyendetsedwa ndi mphepo yamphamvu yamkuntho.

Anthu onse kuyambira kumadzulo mpaka kummawa

adzaopa dzina la Yehova ndi ulemerero wake.

20“Mpulumutsi adzabwera ku Ziyoni

kudzapulumutsa anthu a fuko la Yakobo amene analapa machimo awo,”

akutero Yehova.

21Yehova akuti, “Kunena za pangano lake ndi iwo, Mzimu wanga umene uli pa inu, ndiponso mawu anga amene ndayika mʼkamwa mwanu sadzachoka mʼkamwa mwanu, kapena kuchoka mʼkamwa mwa ana anu, kapena mʼkamwa mwa zidzukulu zawo kuyambira tsopano mpaka kalekale,”

akutero Yehova.